MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA
Mungaphunzitse Bwanji Ana Anu Kukhala Odzichepetsa?
VUTO LIMENE LIMAKHALAPO
-
Mwana wanu ali ndi zaka 10 zokha koma akusonyeza mtima wodzikonda.
-
Amafuna kuti aliyense azimuona ngati bwana.
Mwina mukudzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani akupanga zimenezi? N’zoona kuti sindifuna kuti azidziona ngati wachabechabe komabe sindifuna kuti azidzionanso ngati wofunika kwambiri kuposa anthu ena.’
Kodi n’zotheka kuphunzitsa mwana kukhala wodzichepetsa popanda kum’pangitsa kudziona ngati wachabechabe?
ZIMENE MUYENERA KUDZIWA
Masiku ano, makolo amalimbikitsidwa kupanga zomwe ana awo akufuna. Amalimbikitsidwanso kuti aziwayamikira ngakhale atakhala kuti sanapange chilichonse chanzeru komanso kupewa kuwadzudzula akalakwitsa zinazake. Amanena kuti mwana amene amadziona kuti ndi wofunika kwambiri, amakula bwino ndipo sadzikayikira. Koma kodi n’zimene zimachitikadi? Buku lina linafotokoza kuti: “Ana amene amakula ndi maganizo oti iwowo ndi ofunika kwambiri, amaona anthu ena ngati achabechabe.”—Generation Me.
Ana amene amangoyamikiridwa zilizonse, amakula akuganiza kuti sangalephere kuchita zinthu zina kapenanso kukumana ndi zinthu zokhumudwitsa. Komanso akakula, amalephera kukhala bwino ndi anthu ena ndipo amadzayamba kuvutika maganizo.
Ana sadzikayikira akamaona zinthu zomwe akwanitsa kuchita osati chifukwa chomangokhalira kuwauza kuti ndi ofunika. Choncho kuti mwana asamadzikayikire amafunika kuphunzira komanso kudziwa bwino ntchito zomwe angakwanitse kuchita. (Miyambo 22:29) Amafunikanso kuganizira zofuna za anthu ena. (1 Akorinto 10:24) Kuti akwanitse kuchita zimenezi amafunika kukhala wodzichepetsa.
ZIMENE MUNGACHITE
Muzimuyamikira akachita bwino. Ngati mwana wanu wakhoza bwino kusukulu, muzimuyamikira. Koma ngati walephera, musamathamangire kuloza chala aphunzitsi ake. Mukamachita zimenezi mwanayo sangaphunzire kudzichepetsa. Koma muzimuthandiza kudziwa zimene angachite kuti ulendo wina adzachite bwino. Imeneyi si nthawi yomuyamikira. Mudzamuyamikira nthawi ina akadzachita bwino.
Muzimudzudzula akalakwitsa. Zimenezi sizikutanthauza kuti muzimudzudzula pa chilichonse chimene angalakwitse. (Akolose 3:21) Ngati chimene walakwitsacho n’chachikulu, simuyenera kungonyalanyaza koma muzimuthandiza. Muzichitanso zimenezi ngati wayamba kusonyeza khalidwe loipa. Mukamulekerera akhoza kukula ndi khalidwe loipalo.
Mwachitsanzo, mwina mwana wanu wamwamuna wayamba kudzitama. Ngati mutamulekerera, khalidweli likhoza kukula ndipo sangapeze anzake. Muzimulangiza kuti munthu wodzitama sapeza anzake ndipo akhoza kupanga zinthu zomwe angachite nazo manyazi. (Miyambo 27:2) Muzimuthandizanso kudziwa kuti munthu wodzichepetsa sakhalira kuuza ena za luso lake. Mukamapereka malangizo ngati amenewa kwa mwana wanu mwachikondi, mudzamuphunzitsa kukhala wodzichepetsa ndipo sangamadzione ngati wachabechabe.—Lemba lothandiza: Mateyu 23:12.
Muzimuthandiza kudziwa kuti zinthu zimasintha. Mukamangomupatsa mwana wanu chilichonse chomwe akufuna, amayamba kudziona ngati bwana. Tiyerekeze kuti mwana wanu akufuna mum’gulire chinachake chomwe mukuona kuti simungakwanitse. Mufotokozereni chifukwa chake simungagule chilichonse chomwe simunachiike pa bajeti. Kapena tiyerekezenso kuti mwalephera kupita kunyanja kapena kumalo ena ake kukasangalala, mufotokozereni kuti nthawi zina zinthu zimatha kusintha ndipo ndi mmene moyo ulili. Mwina mungamuuze zimene inuyo mumachita zinthu zokhumudwitsa zikakuchitikirani. Nthawi zina mukakumana ndi vuto linalake, muziwauza ana anu ndipo muziona kuti ndi mwayi wanu kuwathandiza kudziwiratu kuti nawonso azidzakumana ndi mavuto akadzakula.—Lemba lothandiza: Miyambo 29:21.
Muziwalimbikitsa kukhala opatsa. Muzithandiza mwana wanu kudziwa kuti “kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Mungachite zimenezi polemba mayina a anthu amene mungawathandize komanso mmene mungawathandizire monga kuwagulira zinthu, kuwapatsa ndalama ya thiransipoti kapena kuwakonzera zinthu zomwe zawonongeka. Kenako muzipita ndi mwana wanuyo pokathandiza anthuwo. Mwana wanu adzachita chidwi akamaona kuti mukusangalala chifukwa chothandiza ena. Adzaphunziranso kukhala wodzichepetsa poona zimene mumachita.—Lemba lothandiza: Luka 6:38.