Kodi Mukudziwa?
Kodi bambo a Yosefe anali ndani?
Yosefe, yemwe anali kalipentala wa ku Nazareti, ndiye anali bambo a Yesu omulera. Koma kodi bambo a Yosefe anali ndani? Uthenga Wabwino wa Mateyu umanena kuti bambo ake anali Yakobo, pomwe Uthenga Wabwino wa Luka umanena kuti Yosefe anali “mwana wa Heli.” Kodi zimenezi zikusonyeza kuti Baibulo likunena mfundo zotsutsana?—Luka 3:23; Mateyu 1:16.
Mateyu analemba kuti: “Yakobo anabereka Yosefe.” Mawu achigiriki omwe anawagwiritsa ntchito pamenepa, amasonyeza kuti Yakobo analidi bambo omubereka a Yosefe. Choncho, Mateyu ankafotokoza za banja limene Yosefe anabadwiramo lomwe linali mzere wachifumu wa Davide. Ndiye popeza kuti Yosefe anali bambo a Yesu omulera, Yesu analidi woyenera kupatsidwa mpando wachifumu wa Davide.
Koma Luka analemba kuti: ‘Yosefe anali mwana wa Heli.’ Mawu akuti “mwana wa,” angatanthauzenso “mkamwini.” Mfundo yangati imeneyi ikupezekanso pa Luka 3:27, pomwe pamanena zokhudza Salatiyeli. Iye anali mwana wa Yekoniya koma amatchulidwanso kuti “mwana wa Neri.” (1 Mbiri 3:17; Mateyu 1:12) Salatiyeli anali mkamwini wa Neri chifukwa anakwatira mwana wake wina yemwe sanatchulidwe dzina. Ndi mmenenso zinalili ndi Yosefe. Iye akutchulidwa kuti “mwana” wa Heli chifukwa anakwatira Mariya, yemwe anali mwana wa Heliyo. Ndiyetu apa Luka ankangotchula mzere womwe Yesu anabadwira “monga munthu,” kudzere kwa mayi ake Mariya. (Aroma 1:3) Choncho, malemba awiri onsewa amangosonyeza mabanja omwe Yesu anabadwira kuchokera kwa bambo ake komanso mayi ake.
Kodi anthu akale ankagwiritsa ntchito utoto komanso nsalu zotani?
Anthu akale a ku Middle East ankapanga nsalu kuchokera ku ubweya wa nkhosa, mbuzi ndi ngamila. Komano nsalu zambiri zinkapangidwa kuchokera ku ubweya wa nkhosa. Ndiye n’chifukwa chake nthawi zambiri Baibulo limakonda kutchula nkhosa, kumeta ubweya wa nkhosa komanso nsalu zopangidwa ndi ubweya wa nkhosa. (1 Samueli 25:2; 2 Mafumu 3:4; Yobu 31:20) Nthawi zinanso ankapanga nsalu kuchokera ku zomera zinazake zotchedwa fulakesi zomwe zinkalimidwa ku Iguputo ndi ku Isiraeli. (Genesis 41:42; Yoswa 2:6) N’kutheka kuti Aisiraeli akale sankalima thonje, koma Baibulo limasonyeza kuti anthu a ku Perisiya ankagwiritsa ntchito nsalu zopangidwa ndi thonje. (Esitere 1:6) Nsalu za silika zinali zodula kwambiri ndipo Aisiraeli ankazigula kwa amalonda ochokera kum’mawa.—Chivumbulutso 18:11, 12.
Buku lina limanena kuti, “Ubweya womwe ankapangira nsalu unkakhala wa mitundu yosiyanasiyana. Wina unkakhala woyera, wina unkakhala wabulawuni.” (Jesus and His World.) Komanso, nthawi zambiri ubweyawu ankaupaka utoto. Utoto wa mtundu wa pepo unali wodula kwambiri ndipo unkapangidwa kuchokera ku nkhono zinazake zam’madzi. Utoto wofiira, wachikasu, wabuluu komanso wakuda, ankaupeza kuchokera ku zomera, mizu, masamba ndiponso tizilombo tina ting’onoting’ono.