Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Sunagoge wa Nthawi ya Atumwi: Sunagoge wa mu nthawi ya atumwi ayenera kuti ankaoneka chonchi. Pojambula chithunzichi anatsatira zinthu zina zimene zapezeka musunagoge wa ku Gamla yemwe anamangidwa mu nthawi ya atumwi. Sunagogeyu akupezeka pa mtunda wa makilomita pafupifupi 10 kumpoto chakum’mawa kwa nyanja ya Galileya.

Kodi masunagoge anayamba bwanji?

MAWU oti sunagoge anachokera ku mawu achigiriki otanthauza “kusonkhana.” Mawuwa ndi oyenera chifukwa kuyambira kale, Ayuda ankasonkhana m’masunagoge kuti aphunzire kapena alambire. Mawu oti sunagoge sapezeka m’Malemba Achiheberi. Koma Malemba Achigiriki amasonyeza kuti pamene inkafika nthawi ya Yesu malo amenewa anali alipo kale.

Akatswiri ambiri amakhulupirira kuti masunagoge anayamba pa nthawi imene Ayuda anali ku ukapolo ku Babulo. Buku lina limanena kuti: “Akapolowa anali kutali ndi Kachisi m’dziko lachilendoli koma ankafuna kulimbikitsidwa chifukwa cha mavuto amene ankakumana nawo. Choncho ankasonkhana, makamaka patsiku la Sabata, n’kumawerenga Malemba.” (Encyclopaedia Judaica) Zikuoneka kuti atamasulidwa ku ukapolowu, Ayuda ankamanga masunagoge kumene anali ndipo ankasonkhana kumeneko kuti azipemphera komanso kuwerenga Malemba.

Choncho pofika nthawi ya Yesu, Ayuda amene ankakhala ku Isiraeli, ku Middle East komanso m’mbali mwa nyanja ya Mediterranean, anali atayamba kale kusonkhana m’masunagoge kuti azichita zinthu zokhudza kulambira komanso zinthu zina. Pulofesa wina wakuyunivesite yachiheberi ku Yerusalemu ananena kuti anthu ankapita kusunagoge kuti “akaphunzire, achite zikondwerero zopatulika, akaweruze milandu, akapereke zopereka komanso akakambirane nkhani zokhudza ndale ndi nkhani zina.” Pulofesayo anati: “Koma misonkhano yofunika kwambiri m’masunagogewa inali yokhudza kulambira.” Choncho m’pomveka kuti Yesu ankakonda kupita kumisonkhano yakusunagoge kuti akaphunzitse anthu, kuwalangiza komanso kuwalimbikitsa. (Maliko 1:21; 6:2; Luka 4:16) Mpingo wachikhristu utakhazikitsidwa, mtumwi Paulo ankakondanso kulalikira m’masunagoge. Paulo akafika mumzinda ankayamba wapita kukalalikira musunagoge chifukwa chakuti anthu okonda kulambira ankapezeka kumeneko.​—Mac. 17:1, 2; 18:4.