Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?

Yesu anauza ophunzira ake kuti azipemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere. Iye ankadziwa kuti si cholinga cha Mulungu kuti padzikoli pazichitika zinthu zoipa ndiponso kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungathetse mavuto. Koma kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zotani?

ZIMENE UFUMU WA MULUNGU WACHITA KALE

Munkhani yapitayi, takambirana zinthu zimene Yesu ananena kuti zidzakhala chizindikiro. Zinthu zimenezi zimapereka umboni wakuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba ndipo Mfumu yake ndi Yesu Khristu.

Baibulo limanena kuti Yesu atangoyamba kulamulira, anachotsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba. Popeza kuti anaponyedwa padzikoli, zinthu zakhala zikuipiraipirabe kuchokera mu 1914.​—Chivumbulutso 12:7, 9.

Ngakhale kuti padzikoli pali mavuto ambiri, Yesu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, wakhala akuthandiza anthu ambiri. Iye ananeneratu za ntchito yophunzitsa anthu Baibulo padziko lonse. Ntchitoyi ikuthandiza anthu ambiri kuphunzira mfundo za m’Baibulo komanso kuzigwiritsa ntchito. (Yesaya 2:2-4) Anthu ambiri aphunzira kuona ntchito yawo moyenera, mmene angakhalire ndi banja losangalala komanso kusangalala ndi chuma chawo popanda kuona kuti chumacho ndi chofunika kwambiri. Anthu amenewa akukhala ndi moyo wabwino panopa ndipo akuyamba kukhala anthu amene Mulungu akufuna kuti adzakhale nzika za Ufumu wake.

KODI UFUMU WA MULUNGU UDZACHITANSO ZINTHU ZITI M’TSOGOLOMU?

Ngakhale kuti Yesu anayamba kale kulamulira kumwamba, maboma a anthu akulamulirabe padzikoli. Komabe, Mulungu wauza Yesu kuti: “Pita ukagonjetse anthu pakati pa adani ako.” (Salimo 110:2) Posachedwapa, Yesu adzawononga anthu onse otsutsa Ufumu wa Mulungu ndipo adzachotsa mavuto omwe anthu omvera Mulungu amakumana nawo.

Pa nthawi imeneyo, Ufumu wa Mulungu

  • Udzawononga zipembedzo zonyenga. Zipembedzo zomwe zakhala zikuphunzitsa mabodza okhudza Mulungu ndiponso kuchititsa kuti anthu azivutika, zidzathetsedwa. Baibulo limayerekezera zipembedzo zonyenga ndi hule. Zipembedzozi zikadzawonongedwa, anthu ambiri adzadabwa.​—Chivumbulutso 17:15, 16.

  • Udzathetsa maulamuliro a anthu. Ufumu wa Mulungu udzathetsa maulamuliro onse a anthu.​—Chivumbulutso 19:15, 17, 18.

  • Udzachotsa anthu oipa. Kodi anthu amene amachita zoipa ndipo safuna kumvera Mulungu zidzawathera bwanji? “Oipa adzachotsedwa padziko lapansi ndipo achinyengo adzazulidwamo.”​—Miyambo 2:22.

  • Udzawononga Satana ndi ziwanda. Satana ndi ziwanda ‘sadzasocheretsanso mitundu ya anthu.’​—Chivumbulutso 20:3, 10.

Kodi zonsezi zidzakhudza bwanji anthu amene ali kumbali ya Ufumu wa Mulungu?

ZIMENE UFUMU WA MULUNGU UDZACHITIRE ANTHU

Yesu azidzalamulira dzikoli ali kumwamba ndipo adzachita zambiri kuposa zimene wolamulira aliyense padzikoli angachite. Iye azidzalamulira mothandizidwa ndi anthu 144,000 osankhidwa kuchokera padziko lapansi. (Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 3) Yesu adzaonetsetsa kuti chifuniro cha Mulungu chikuchitika padzikoli. Ndiye kodi Ufumu wa Mulungu udzawachitira zotani anthu?

  • Udzathetsa matenda komanso imfa. “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala,’” ndipo “imfa sidzakhalaponso.”​—Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:4.

  • Udzabweretsa mtendere weniweni. “Mtendere wa ana ako udzakhala wochuluka” ndipo “aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu ndipo sipadzakhala wowaopsa.”​—Yesaya 54:13; Mika 4:4.

  • Udzapatsa anthu ntchito yosangalatsa. “Anthu anga osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo. Sadzagwira ntchito pachabe.”​—Yesaya 65:22, 23.

  • Udzathetsa mavuto azachilengedwe. “Chipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala. Dera lachipululu lidzakondwa ndipo lidzachita maluwa n’kukhala lokongola ngati duwa la safironi.”​—Yesaya 35:1.

  • Udzaphunzitsa anthu zimene angachite kuti akhale ndi moyo wosatha. “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”​—Yohane 17:3.

Mulungu amafuna kuti mudzapeze madalitso amenewa. (Yesaya 48:18) Nkhani yotsatira ifotokoza zimene mungachite panopa kuti mudzalandire madalitsowa.