Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kachigawo ka buku la Yesaya komwe kanapezeka m’mipukutu ya ku Nyanja Yakufa. M’munsi mwake muli kachigawo ka buku la Yesaya ka m’Baibulo lamasiku ano la Chiarabu. Uthenga wa m’Mawu a Mulungu sunasinthe

Kodi Mawu a Mulungu Anasinthidwa?

Kodi Mawu a Mulungu Anasinthidwa?

Anthu ena amaona kuti Mawu a Mulungu opezeka m’Malemba Opatulika anasinthidwa. Mneneri Yesaya ananena kuti Mawu a Mulungu “adzakhala mpaka kalekale.” (Yesaya 40:8) Kodi tingatsimikizire bwanji kuti Mawu a Mulungu sanasinthidwe?

Mulungu ali ndi mphamvu zochititsa kuti Mawu ake asungidwe bwino popanda kusinthidwa kapena kuwonongedwa. Pa nthawi imene anthu ankakopera Mawu a Mulungu, ankawerenga chilembo chilichonse pofuna kutsimikizira kuti sanawonjezere, kuchotsera kapena kusintha mawu ena alionse. Popeza anthu si angwiro, ena mwa anthu omwe ankakopera Mawuwa analakwitsa zinthu zina zing’onozing’ono.

KODI TINGATSIMIKIZIRE BWANJI KUTI M’MALEMBA OPATULIKA A MASIKU ANO MULI UTHENGA WOCHOKERADI KWA MULUNGU?

Anthu anakopera masauzande ambirimbiri a mipukutu yakale ya Malemba Opatulika. Mpukutu umodzi ukapezeka ndi zolakwika ngakhale zing’onozing’ono, n’zosavuta kudziwa kuti zolondola n’ziti pouyerekezera ndi mipukutu inanso.​—Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yamutu wakuti, “Kodi Baibulo Linasinthidwa Kapena Kusokonezedwa?” pa jw.org.

Taganizirani za mipukutu yakale imene anthu amtundu wa Bedouin anapeza mu 1947 m’mapanga pafupi ndi Nyanja Yakufa. M’mipukutu yakaleyi muli mbali zina za Malemba Opatulika zomwe zakhalapo kwa zaka zoposa 2,000. Akatswiri anayerekezera mipukutu yakaleyi ndi Malemba Opatulika omwe tili nawo masiku ano. Ndiye kodi anapeza zotani?

Akatswiri anapeza kuti zimene zili m’Mawu a Mulungu amene tili nawo masiku ano n’zofanana ndi zimene zili m’mipukutu yoyambirira. * Zimene akatswiriwa anachita pofufuza mosamala m’mipukutu yakale zikutitsimikizira kuti uthenga womwe uli m’Malemba Opatulika ndi umenedi unachokera kwa Mulungu. Sitikukayikira kuti Mulungu anaonetsetsa kuti Malemba Opatulika asungidwa bwino ndiponso ndi olondola kuti atithandize masiku ano.

Choncho, tikamawerenga Mawu a Mulungu timakhulupirira ndi mtima wonse kuti ndi olondola. Poganizira zimenezi, tiyeni tione zimene tingaphunzire zokhudza Mulungu kuchokera kwa aneneri ake.

^ ndime 7 Buku lakuti The Complete Dead Sea Scrolls in English, lolembedwa ndi Geza Vermes, tsamba 16.