NKHANI YA PACHIKUTO | MASOMPHENYA OTITHANDIZA KUMVETSA ZA KUMWAMBA
Mafunso Okhudza Mmene Zilili Kumwamba
Kodi munayamba mwadzifunsapo mafunso okhudza kumwamba komanso kuti kumakhala ndani? Kuyambira kalekale anthu akhala akufunsa mafunso pa nkhaniyi. Anthu ena amakhulupirira kuti kumwamba kuli mizimu ya anthu amene anamwalira. Ena amaganiza kuti ndi malo osangalatsa komanso amtendere wokhawokha komwe kumakhala angelo. Enanso amakhulupirira kuti ndi malo amene kumakhala milungu yambirimbiri.
Anthu ambiri amanena kuti n’zosatheka kudziwa mmene kumwamba kulili chifukwa palibe munthu amene anakhalako. Koma zimenezi si zoona chifukwa Yesu Khristu anakhalako kumwamba asanabwere padziko lapansi. Nthawi ina anauza atsogoleri achipembedzo akale kuti: “Ndinatsika kuchokera kumwamba kudzachita chifuniro cha iye amene anandituma, osati chifuniro changa.” Choncho pamene ankauza atumwi ake kuti, “m’nyumba ya Atate wanga muli malo ambiri okhalamo,” ankafotokoza zinthu zoti anazionapo.—Yohane 6:38; 14:2.
Atate ake a Yesu ndi Mulungu amene dzina lake ndi Yehova ndipo amakhala kumwamba. (Salimo 83:18) Choncho palibe amene angafotokoze momveka bwino za kumwamba kuposa Yehova Mulungu ndiponso Yesu. Masomphenya amene anaonetsa anthu ena okhulupirika angatithandize kudziwa zambiri zokhudza kumwamba.
Nkhani yotsatira ifotokoza malemba ena a m’Baibulo okhudza zimene anthu ena anaona m’masomphenya. Popeza kuti kumwamba kulibe zinthu zoti tingathe kuziona, m’masomphenyawa Mulungu anagwiritsa ntchito zinthu zooneka n’cholinga choti atithandize kumvetsa zinthu zakumwambazo. Masomphenyawa akuthandizani kudziwa bwino kuti kumwamba kuli ndani.