Mawu kwa Owerenga
Wokondedwa Wowerenga
M’maganiziyi muli nkhani zophunzira 5 zomwe ziyankhe mafunso otsatirawa:
Loyamba, kodi Yehova anakonza zotani pofuna kutithandiza kuti tizimumvera ndi kumutumikira ngakhale kuti ndife ochimwa?
Lachiwiri, kodi Yehova wakhala akutiphunzitsa zotani zokhudza kulapa kwenikweni, nanga wakhala akuthandiza bwanji ochimwa kuti alape?
Lachitatu, kodi mpingo wa ku Korinto unalangizidwa kuti uthandize bwanji munthu wina yemwe anachita tchimo lalikulu mwadala?
La 4, kodi akulu masiku ano angathandize bwanji munthu yemwe wachita tchimo lalikulu?
La 5, kodi mpingo ungatani kuti upitirize kusonyeza chikondi ndi chifundo kwa munthu wochimwa yemwe wachotsedwa?