“Mupitirize Kukonda Abale”
“Mupitirize kukonda abale.”—AHEB. 13:1.
NYIMBO: 72, 119
1, 2. N’chifukwa chiyani Paulo analembera kalata Akhristu achiheberi?
M’CHAKA cha 61 C.E., Akhristu ambiri a m’madera a ku Isiraeli anali pa mtendere. Ngakhale kuti pa nthawiyi mtumwi Paulo anali m’ndende, ankayembekezera kuti sipadutsa nthawi yaitali asanatuluke. Nayenso Timoteyo anali atangotuluka kumene m’ndende ndipo ankafuna kukayendera abale a ku Yudeya limodzi ndi Paulo. (Aheb. 13:23) Komabe pa nthawiyi n’kuti kutangotsala zaka 5 zokha kuti asilikali achiroma azungulire mzinda wa Yerusalemu. Komanso n’kuti patatha zaka 28 kuchokera pamene Yesu anapereka malangizo akuti Akhristu a mu Yerusalemu ndiponso m’dera lonse la Yudeya, adzathawe akadzangoona magulu ankhondo atazungulira mzindawo.—Luka 21:20-24.
2 Pa zaka 28 zimenezi Akhristu achiyuda a ku Isiraeli anali atasonyeza kale kupirira chifukwa anali atazunzidwa komanso kukumana ndi mavuto ena. (Aheb. 10:32-34) Komabe Paulo ankadziwa kuti Akhristuwa anali atatsala pang’ono kukumana ndi mayesero ena aakulu kwambiri. (Mat. 24:20, 21; Aheb. 12:4) Ndiyeno ankafuna kuti iwo akhale okonzeka kukumana ndi vuto lililonse. Akhristuwo ankafunika kukhala opirira komanso kukhala ndi chikhulupiriro cholimba chimene chikanawathandiza kuti apulumuke. (Werengani Aheberi 10:36-39.) Choncho mzimu wa Yehova unachititsa Paulo kuti awalembere kalata yowalimbikitsa. Kalatayi ndi buku la m’Baibulo la Aheberi.
3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene zili m’buku la Aheberi zingatithandizenso ifeyo?
3 Masiku anonso, kalata imene Paulo analembera Akhristu achiheberiwo ingatithandize. Tikutero chifukwa chakuti ifenso tikukhala m’nthawi yovuta. Anthu a Yehovafe tazunzidwapo komanso kukumana ndi mavuto ena. (2 Tim. 3:1, 12) Koma tapirira zinthu zimenezi ndipo tasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba. Komabe panopa ambirife tili pa mtendere ndipo sitikuzunzidwa. Ngakhale zili choncho, tiyenera kukumbukira kuti mofanana ndi Akhristu a m’nthawi ya Paulo, posachedwapa tikumana ndi mayesero aakulu kwambiri.—Werengani Luka 21:34-36.
4. Kodi lemba la chaka chino ndi loti chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani ndi lothandiza?
4 N’chiyani chingatithandize kukonzekera mayesero amenewa? M’buku la Aheberi, Paulo anafotokoza zinthu zingapo zimene zingatithandize kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Chinthu chimodzi chimene ananena chikupezeka m’vesi loyamba la chaputala chomaliza cha kalatayi. Vesili ndi limene lasankhidwa kuti likhale lemba la chaka chino cha 2016 ndipo limati: “Mupitirize kukonda abale.”—Aheb. 13:1.
Lemba la chaka chino cha 2016: “Mupitirize kukonda abale.”—Aheberi 13:1
KODI KUKONDA ABALE KUMATANTHAUZA CHIYANI?
5. Kodi kukonda abale kumatanthauza chiyani?
5 Kodi kukonda abale kumatanthauza chiyani? Mawu achigiriki amene Paulo anagwiritsa ntchito m’lembali, (phi·la·del·phiʹa) amanena za kukonda munthu ndi mtima wonse ngati mmene timachitira ndi wachibale kapena mnzathu wapamtima. (Yoh. 11:36) Sikuti anthu a Mulungufe timangonena kuti timakondana. Chikondi chathu chimakhala chenicheni. (Mat. 23:8) Timatsatira malangizo akuti: “Pokonda abale, khalani ndi chikondi chenicheni pakati panu. Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) Timagwirizana kwambiri chifukwa chokhala ndi chikondi chimenechi komanso cha a·gaʹpe, chomwe munthu amakhala nacho chifukwa chotsatira mfundo zolungama za Mulungu.
6. Kodi tiziwaona bwanji Akhristu anzathu?
6 Katswiri wina wa Baibulo ananena kuti Akhristu ndi amene amakonda kugwiritsa ntchito mawu akuti ‘kukonda abale.’ N’zoona kuti kale Ayuda ankagwiritsa ntchito mawu oti “abale” akamanena za anthu ena amene sanali achibale awo enieni. Komabe ankagwiritsa ntchito mawuwa ponena za Ayuda anzawo okha, osati anthu amitundu ina. Mosiyana ndi zimenezi, Akhristu amaona kuti Mkhristu aliyense ndi m’bale wawo, mosaganizira za mtundu wake. (Aroma 10:12) Yehova watiphunzitsa kuti tiyenera kukonda Akhristu anzathu ngati abale athu enieni. (1 Ates. 4:9) Koma n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi?
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUPITIRIZA KUKONDA ABALE?
7. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukonda abale athu?
7 Choyamba, tiyenera kukonda abale athu chifukwa Mulungu amafuna kuti tizichita zimenezi. Sitinganene kuti timakonda Mulungu ngati sitikonda abale athu. (1 Yoh. 4:7, 20, 21) Chifukwa china n’chakuti timafunika kuthandizana, makamaka tikakumana ndi mavuto. Paulo ankadziwa kuti Akhristu ena achiheberi amene anawalembera kalata yake, adzayenera kuthawa n’kusiya nyumba komanso katundu wawo. Yesu ananena kuti nthawi imeneyo idzakhala yovuta kwambiri. (Maliko 13:14-18; Luka 21:21-23) Choncho Akhristuwo ankafunika kukondana kwambiri kuti adzathe kuthandizana pa nthawi yovutayo.—Aroma 12:9.
8. Kodi tiyenera kuchita chiyani panopa, chisautso chachikulu chisanayambe?
8 Posachedwapa chisautso chachikulu chiyamba. (Maliko 13:19; Chiv. 7:1-3) Pa nthawiyo, tidzayenera kutsatira malangizo ochokera kwa Yehova akuti: “Inu anthu anga, pitani mukalowe m’zipinda zanu zamkati ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Mwina ‘zipinda zamkati’ zimenezi zikuimira mipingo, kumene timasonkhana ndi abale ndi alongo athu n’kumalambira Yehova. Komabe sikuti timangofunika kusonkhana ndi abale athu. Mtumwi Paulo anauza Akhristu achiheberi kuti akasonkhana ayenera kulimbikitsana kuti azikondana. (Aheb. 10:24, 25) Choncho, tiyenera kuyamba panopa kukondana ndi abale athu. Zimenezi zidzatithandiza tikadzakumana ndi mayesero aakulu m’tsogolo.
9. (a) Kodi ndi pa nthawi ziti pamene tingasonyeze kuti timakonda abale athu? (b) Perekani zitsanzo zosonyeza kuti anthu a Yehova amakondana.
9 Ngakhale panopa abale athu ambiri amakumana ndi mavuto monga zivomezi, kusefukira kwa madzi ndiponso mphepo zamkuntho. Palinso ena amene akuvutika chifukwa chotsutsidwa komanso kuzunzidwa. (Mat. 24:6-9) Kuwonjezera pamenepo, timakumananso ndi mavuto azachuma chifukwa anthu ambiri m’dzikoli amachita zachinyengo. (Chiv. 6:5, 6) Akhristu anzathu akakumana ndi mavuto ngati amenewa, tiziona kuti ndi nthawi yosonyeza kuti timawakonda. Tiyenera kupitiriza kukonda abale athu ngakhale kuti masiku ano anthu ambiri alibe chikondi chenicheni.—Mat. 24:12. [1]
KODI TINGATANI KUTI TIPITIRIZE KUKONDA ABALE?
10. Kodi tsopano tikambirana chiyani?
10 Ngakhale kuti timakumana ndi mavuto ambiri, kodi tingatani kuti tizikondabe abale athu? Nanga tingasonyeze bwanji kuti timawakondadi? Mtumwi Paulo atanena kuti “mupitirize kukonda abale,” anafotokozanso njira zingapo zimene tingachitire zimenezi. Pa njira zimenezo, tiyeni tsopano tikambirane njira 6.
11, 12. Kodi “kuchereza alendo” kumatanthauza chiyani? (Onani chithunzi patsamba 7.)
11 “Musaiwale kuchereza alendo.” (Werengani Aheberi 13:2.) Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “kuchereza alendo,” amatanthauza “kukomera mtima anthu osawadziwa.” Mawu amenewa akutikumbutsa zimene Abulahamu ndi Loti anachita. Pa nthawi ina, analandira bwino anthu amene sankawadziwa. Koma kenako anazindikira kuti anthuwo anali angelo. (Gen. 18:2-5; 19:1-3) Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo cha Abulahamu ndi Loti pofuna kulimbikitsa Akhristu achiheberi kuti azichereza abale awo posonyeza kuti amawakonda.
12 Kodi timasonyeza chikondi poitanira anthu kunyumba kwathu kuti tidzadye nawo kapena kucheza nawo? Tisaganize kuti tiyenera kukonza chakudya chambiri kapena chapamwamba. Komanso sitiyenera kuitana anthu okhawo amene angadzatiitanenso kapena kutichitira zinazake. (Luka 10:42; 14:12-14) Tisaiwale kuti cholinga chathu ndi kulimbikitsana osati kuwasonyeza kuti tili ndi zinthu zambiri. N’kutheka kuti sitikudziwa bwino woyang’anira dera wathu komanso mkazi wake. Ndiye kodi sizingakhale bwino kuwaitanira kunyumba kwathu? (3 Yoh. 5-8) N’zoona kuti tonse timatanganidwa ndiponso timakumana ndi mavuto. Komabe tiyenera kukumbukira kuti “kuchereza alendo” n’kofunika kwambiri.
13, 14. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ‘tikukumbukira amene ali m’ndende’?
13 “Kumbukirani amene ali m’ndende.” (Werengani Aheberi 13:3.) Apa sikuti Paulo ankangonena za munthu wina aliyense amene ali kundende. Koma ankanena za Akhristu amene anamangidwa chifukwa chotumikira Mulungu. Pamene ankalemba mawu amenewa, nayenso n’kuti atakhala m’ndende zaka pafupifupi 4. (Afil. 1:12-14) Iye anayamikira abale chifukwa chomusonyeza chifundo pamene anali m’ndende. (Aheb. 10:34) Akhristu achiheberi ankakhala kutali ndipo sakanatha kukathandiza Paulo kundende ngati mmene ena ankachitira. Koma kodi Akhristuwa akanamuthandiza bwanji? Akanatha kumupempherera kuti Mulungu amuthandize.—Aheb. 13:18, 19.
14 Masiku anonso sitingathe kuthandiza abale athu onse amene ali m’ndende ngati mmene abale apafupi angawathandizire. Koma tingasonyeze kuti timawamvera chisoni komanso kuwakonda tikamapempha Yehova mochokera pansi pa mtima kuti awathandize. Mwachitsanzo, tingapempherere abale ndi alongo komanso ana amene ali m’ndende ku Eritrea. Ena mwa anthu amenewa, ndi M’bale Paulos Eyassu, M’bale Isaac Mogos ndi M’bale Negede Teklemariam omwe akhala m’ndende zaka zoposa 20.
15. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ‘timalemekeza ukwati’?
15 “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse.” (Werengani Aheberi 13:4.) Tingasonyezenso kuti timakonda abale tikamalemekeza ukwati n’kumapewa chiwerewere. (1 Tim. 5:1, 2) Mkhristu akachita chiwerewere ndi m’bale kapena mlongo, amakhala kuti walakwira munthu amene wachita naye chiwerewereyo komanso achibale a munthuyo. Zimenezi zingachititse kuti abale asamakhulupirirane ndiponso kukondana. (1 Ates. 4:3-8) Komanso kodi mkazi angamve bwanji atadziwa kuti mwamuna wake amaonera zolaula mobisa? Nanga kodi mwamuna amene amachita zimenezi amasonyeza kuti amakondadi mkazi wake ndiponso kulemekeza ukwati?—Mat. 5:28.
16. Kodi kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo kumatithandiza bwanji kukonda abale athu?
16 “Mukhale okhutira ndi zimene muli nazo.” (Werengani Aheberi 13:5.) Tikamakhulupirira kwambiri Yehova, timaona zinthu moyenera ndipo timakhutira ndi zimene tili nazo. (1 Tim. 6:6-8) Timazindikiranso kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ndiponso kugwirizana ndi abale ndi alongo athu ndi kofunika kwambiri kuposa chilichonse. Munthu amene ndi wansanje, wadyera, wokonda kudandaula komanso kupezera ena zifukwa zimamuvuta kuti azikondana ndi abale ake. Koma munthu wokhutira ndi zimene ali nazo sachita zimenezi ndipo amakonda kugawana zinthu ndi ena.—1 Tim. 6:17-19.
17. Kodi ‘kukhala olimba mtima’ kumatithandiza bwanji kukonda abale athu?
17 ‘Mukhale olimba mtima.’ (Werengani Aheberi 13:6.) Tikamakhulupirira Yehova timachita zinthu molimba mtima tikakumana ndi mavuto. Izi zimatithandizanso kuti tiziona zinthu moyenera. Tikamaona zinthu moyenera zingakhale zosavuta kuti tizikonda abale athu komanso kuwalimbikitsa. (1 Ates. 5:14, 15) Ngakhale pa nthawi yovuta kwambiri pa chisautso chachikulu, tidzatha ‘kuimirira chilili ndi kutukula mitu yathu’ podziwa kuti Yehova atipulumutsa.—Luka 21:25-28.
18. N’chiyani chingatithandize kuti tizikonda abale amene akutsogolera mumpingo?
18 “Kumbukirani amene akutsogolera pakati panu.” (Werengani Aheberi 13:7, 17.) Akulu amagwira ntchito mwakhama potithandiza ndipo sayembekezera malipiro alionse. Tikamaganizira zimenezi, timawakonda komanso kuwayamikira kwambiri ndipo timapewa kuchita chilichonse chimene chingachititse kuti azigwira ntchito yawo modandaula. Tikamawamvera ndiponso kuwagonjera timasonyeza kuti timawakonda ndiponso ‘kuwapatsa ulemu waukulu chifukwa cha ntchito imene amagwira.’—1 Ates. 5:13.
TIZIKONDANA KWAMBIRI
19, 20. Kodi tingatani kuti tizikondabe abale athu?
19 Anthu ambiri amadziwa kuti anthu a Yehovafe timakondana kwambiri. Mtumwi Paulo anasonyezanso kuti zimenezi ndi zoona. Ndipo analimbikitsa abale ndi alongo kuti apitirize kukondana kwambiri. (1 Ates. 4:9, 10) Tizikumbukira kuti nthawi zonse tikhoza kupeza njira zina zomwe tingasonyezere kuti timakonda abale athu.
20 Choncho tikamaganizira lemba la chaka chino, tizidzifunsa mafunso awa: Kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndine wochereza? Nanga kodi ndingakumbukire bwanji abale amene ali m’ndende? Kodi ndimalemekeza ukwati? Ndingatani kuti ndizikhutira ndi zimene ndili nazo? Kodi ndingachite chiyani kuti ndizikhulupirira kwambiri Yehova? Nanga ndingatani kuti ndizimvera amene akutsogolera mumpingo wathu? Tisamangoona lemba la chaka chino ngati chikwangwani cha m’Nyumba ya Ufumu, koma tiyeni tiziyesetsa kulitsatira pogwiritsa ntchito mfundo 6 zimene takambiranazi. Tizikumbukira zimene lembali limanena kuti: “Mupitirize kukonda abale.”—Aheb. 13:1.
^ [1] (ndime 9) Werengani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2002, tsamba 8 ndi 9 ndiponso mutu 20 m’buku lakuti, Ufumu wa Mulungu Ukulamulira kuti muone zitsanzo za mmene a Mboni za Yehova amasonyezera chikondi kwa abale awo pa nthawi ya mavuto.