MBIRI YA MOYO WANGA
Masisitere Anasintha N’kukhala Alongo
ZAKA zambiri m’mbuyomo, mchemwali wanga anakwiya kwambiri n’kundilalatira kuti: “Usandiuzenso za chipembedzo chakocho. Zimandinyansa kwambiri ndipo iwenso umandinyansa.” Panopa ndili ndi zaka 91 koma ndimakumbukirabe mmene mawuwa anandipwetekera. Komabe zomwe zinatichitikira n’zogwirizana ndi lemba la Mlaliki 7:8 lomwe limati: “Mapeto a chinthu amakhala bwino kuposa chiyambi chake.”—Felisa.
Felisa: Ndinabadwira m’banja losauka ku Spain. Banja lathu Linali lachikatolika ndipo tinkalimbikira kwambiri. Achibale athu 13 anali ansembe ndipo ena anali ndi maudindo osiyanasiyana. M’bale wawo wina wa mayi anga anali wansembe komanso mphunzitsi wa sukulu yachikatolika. Iye atamwalira, Papa Yohane Paulo Wachiwiri anamupempherera kuti Mulungu amulandire kumwamba. Bambo anga ankasula zitsulo ndipo mayi anga ankalima. M’banja lathu tinalimo ana 8 ndipo ine ndinali wamkulu.
Pamene ndinali ndi zaka 12, nkhondo yapachiweniweni inayambika ku Spain. Koma nkhondoyo itatha, bambo anga anamangidwa chifukwa choti mfundo zawo zinkasemphana ndi boma la pa nthawiyo. Izi zinapangitsa kuti mayi anga azivutika kutisamalira. Kenako mnzawo anawauza kuti atumize azichemwali anga atatu kumalo okhala masisitere mumzinda wa Bilbao kuti asamavutike ndi njala. Mayina a azichemwali angawo ndi Araceli, Lauri ndi Ramoni.
Araceli: Pamene ankatitumiza ku Bilbao, ine ndinali ndi zaka 14, Lauri anali ndi zaka 12 ndipo Ramoni anali ndi zaka 10. Tinkawasowa kwambiri achibale athu. Tinkagwira ntchito yoyeretsa koma patapita zaka ziwiri, anatitumiza kumalo ena a masisitere ku Zaragoza kumene ankasunga anthu okalamba. Tinkagwira ntchito yoyeretsa m’khitchini ndipo inali yovuta kwambiri.
Felisa: Mayi anga ndi achimwene awo, omwe analinso wansembe, anagwirizana zonditumizanso ku Zaragoza. Anachita izi kuti ndisiyane ndi mnyamata wina amene ankandifuna. Popeza ndinkakonda kwambiri za Mulungu, ndinavomera kupita. Tsiku lililonse ndinkapita ku Misa ndipo ndinkafuna kudzakhala mmishonale potengera m’bale wanga amene anali ku Africa.
Moyo wa kumene ndinkakhala sunkandisangalatsa ndipo masisitere sankandilimbikitsa kuti ndikatumikire kudziko lina. Patangopita chaka chimodzi ndinabwerera kunyumba kuti ndizikasamalira amalume anga. Tsiku lililonse ndinkagwira ntchito zapakhomo komanso kupemphera nawo pogwiritsa ntchito kolona. Ndinkakonda kusamalira maluwa komanso kukongoletsa zifaniziro za Mariya ndi za anthu ena amene amati ndi oyera mtima.
Araceli: Patapita nthawi, moyo wathu kumalo a masisitere unasintha kwambiri. Nditapanga malumbiro, masisitere anaganiza zotisiyanitsa. Ramoni anatsala ku Zaragoza, Lauri anapita ku Valencia ndipo ine ananditumiza ku Madrid. Nditafika ndinakachitanso malumbiro achiwiri. Ku Madrid kunali malo ogona ana asukulu, achikulire komanso alendo choncho kunali ntchito yambiri. Ine ndinkagwira ntchito kukachipatala ka kumeneko.
Ndinkaganiza kuti moyo wa masisitere ndi wabwino ndipo undithandiza kuphunzira Baibulo. Koma palibe amene ankakamba za Mulungu kapena Yesu ndipo sitinkagwiritsa ntchito Baibulo. Tinkangolambira Mariya komanso kuphunzira Chilatini ndi moyo wa anthu oyera mtima. Koma nthawi yambiri tinkangogwira ntchito yowawa.
Ndinayamba kuda nkhawa kwambiri ndipo ndinakambirana ndi mayi mfumu. Ndinawauza kuti sindikufuna kumagwira ntchito yongolemeretsa anthu ena, pamene achibale anga akuvutika. Nditatero ananditsekera m’kachipinda kenakake n’cholinga choti ndisinthe maganizo ofuna kuchoka.
Masisiterewo anayesapo kundiuza katatu konse kuti ndizipita kwathu pofuna kungoona ngati ndingachokedi. Ataona kuti ndatsimikizadi, anandiuza kuti ndilembe mawu akuti, “Ndikuchoka chifukwa chakuti ndikufuna kukatumikira Satana osati Mulungu.” Izi zinandikhumudwitsa kwambiri. Ngakhale kuti ndinkafuna kuchoka, sindinalembe zimenezi. Kenako ndinafotokozera wansembe zonse zimene zinachitikazi. Iye anakonza zoti ndibwerere ku Zaragoza. Nditangokhala miyezi itatu kumeneko, ndinaloledwa kubwerera kwathu. Pasanapite nthawi yaitali, Lauri ndi Ramoni nawonso anachoka kumalo a masisitere kumene ankakhala kuja.
“BUKU LOLETSEDWA” LINATISIYANITSA
Felisa: Patapita nthawi ndinakwatiwa n’kusamukira ku Cantabria. Ndinkapitabe kutchalitchi nthawi zonse ndipo Lamlungu linalake wansembe analengeza mokwiya kuti: “Mwaliona buku ili! Ngati munthu wina anakupatsani buku limeneli, mulibweretse kwa ine kapena mulitaye.” Buku lake linali lakuti, Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya.
Ndinalibe bukuli koma atanena zimenezi, ndinayamba kulifuna. Ndiyeno patangopita masiku ochepa, a Mboni awiri anabwera n’kudzandipatsa bukulo. Ndinaliwerenga tsiku lomwelo ndipo a Mboni aja atabweranso ndinavomera kuti azindiphunzitsa Baibulo.
Zimene ndinkaphunzirazo zinandikhudza kwambiri. Ndinayamba kukonda Yehova komanso utumiki ndipo ndinasiya kupita kutchalitchi kwathu. Ndinabatizidwa mu 1973 ndipo ndinkayesetsa kuuza anthu am’banja lathu za Yehova ngakhale kuti zinali zovuta. Monga ndanenera poyamba paja, anthu a m’banja lathu, makamaka Araceli, ankanditsutsa kwambiri.
Araceli: Zimene ndinkakumana nazo kumalo a masisitere zinandichititsa kuti ndizikhala wokwiya. Koma ndinkayesetsa kupita kutchalitchi n’kumapemphera pogwiritsa ntchito kolona. Ndinkapempha Mulungu kuti andithandize kumvetsa bwino Baibulo. Koma ndinkaona kuti Felisa watengeka kwambiri ndi zimene ankaphunzira ndipo ndinkadana nazo kwambiri.
Patapita zaka zingapo ndinabwerera ku Madrid kukagwira ntchito ndipo ndinakwatiwa. Koma kenako ndinayamba kukayikira za chipembedzo chathu. Ndinazindikira kuti anthu ambiri sankatsatira zimene Yesu anaphunzitsa ngakhale kuti ankakonda kupita kutchalitchi. Choncho, ndinasiyiratu kupita kutchalitchi. Sindinkakhulupiriranso anthu amene amati ndi oyera mtima, zoti tiziulula machimo kwa ansembe komanso zoti Mulungu amawotcha anthu. Ndinatayanso mafano amene ndinali nawo. Koma sindinkadziwa ngati zimene ndinachitazi zinali zoyenera. Ndinakhumudwa kwambiri koma ndinkapemphera kwa Mulungu kuti: “Chonde mundithandize ndikufuna ndikudziweni.”
Ndimakumbukira kuti nthawi zina a Mboni za Yehova ankabwera kunyumba kwathu, koma ineyo sindinkatuluka m’nyumba kuti ndilankhule nawo. Pa nthawiyi sindinkakhulupiriranso chipembedzo chilichonse.Lauri ankakhala ku France ndipo Ramoni ankakhala ku Spain. Cha m’ma 1980, onse anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni. Ndinkaona kuti nawonso asocheretsedwa ngati Felisa. Ndiyeno ndinakumana ndi mayi wina dzina lake Angelines. Patapita nthawi anakhala mnzanga wapamtima. Nayenso anali wa Mboni za Yehova ndipo iyeyo ndi mwamuna wake ankandipempha kuti azindiphunzitsa Baibulo. Anazindikira kuti ndinkafunika kuphunzira Baibulo ngakhale kuti ndinkadana ndi zipembedzo. Kenako ndinawauza kuti: “Ndikhoza kuyamba kuphunzira pokhapokha ngati mungalole kuti ndizigwiritsa ntchito Baibulo langa.” Apa ndinkanena za Baibulo lomasuliridwa ndi Nácar-Colunga.
BAIBULO LINATIGWIRIZANITSA
Felisa: Pamene ndinkabatizidwa mu 1973 n’kuti mumzinda wa Santander muli a Mboni 70 okha. Gawo lathu linali lalikulu kwambiri moti tinkayenda pa basi kenako pa galimoto ina kuti tikalalikire kumidzi yonse.
Ndakhala ndikuphunzira ndi anthu ambirimbiri ndipo anthu 11 anabatizidwa. Ambiri mwa anthuwa anali a Katolika. Popeza nanenso ndinali Mkatolika, ndinkadziwa kuti m’pofunika kuwamvetsa komanso kuwalezera mtima kwambiri. Ndinkaona kuti akufunika nthawi yokwanira kuti Baibulo komanso mzimu woyera ziwathandize kusiya zikhulupiriro zawo. (Aheb. 4:12) Mwamuna wanga anali wapolisi ndipo anabatizidwa mu 1979. Nawonso mayi anga anayamba kuphunzira Baibulo koma anamwalira pasanapite nthawi.
Araceli: Nditangoyamba kuphunzira ndi a Mboni ndinkawakayikira kwambiri. Koma nditaphunzira milungu ingapo, ndinaona kuti zikundithandiza moti mkwiyo wanga uja unayamba kuchepa. Chimene chinkandisangalatsa n’chakuti a Mboni ankatsatira zimene amaphunzitsa. Mtima wokayikira uja unatha ndipo chikhulupiriro changa chinayamba kulimba komanso ndinayamba kusangalala. Ngakhale anzanga ankandiuza kuti: “Musasiye zimene mukuphunzirazo.”
Tsiku lina ndinapemphera kuti: “Yehova ndikuthokoza kwambiri kuti munandilezera mtima. Munandipatsa mwayi woti ndidziwe bwino Baibulo.” Ndinapempha Felisa kuti andikhululukire chifukwa cha mawu achipongwe amene ndinamulankhula aja. Tinkakonda kukambirana mfundo za m’Baibulo ndipo zokangana zija zinatha. Kenako mu 1989 ndinabatizidwa ndipo n’kuti ndili ndi zaka 61.
Felisa: Panopa ndili ndi zaka 91, mwamuna wanga anamwalira ndipo mphamvu zanga zinachepa. Koma ndimawerenga Baibulo tsiku lililonse, ndimayesetsa kupezeka pamisonkhano komanso kulalikira mmene ndingathere.
Araceli: Ndimakonda kwambiri kulalikira masisitere ndi ansembe. Mwina n’chifukwa chakuti nanenso ndinali sisitere. Ambiri ndimawapatsa mabuku athu ndipo amamvetsera ndikamawalalikira. Tsiku lina ndikukambirana ndi wansembe wina, ananena kuti: “Mayi, zonse mukunenazi n’zoona. Koma mukuganiza kuti pamsinkhu wanga uno ndingasinthenso n’kupita kuti? Kodi ansembe anzanga komanso achibale adzati bwanji?” Ndiyeno ndinamuyankha kuti: “Nanga Mulungu adzati bwanji?” Anazindikira kuti sakuganiza bwino koma sanalimbe mtima kuti apitirize kuphunzira.
Tsiku limene sindidzaliiwala ndi limene mwamuna wanga ananena kuti akufuna kupita nawo kumisonkhano. Iye anali ndi zaka zoposa 80 koma kuyambira nthawi imeneyo sanajombepo kumisonkhano. Anayamba kuphunzira Baibulo mpaka anakhala wofalitsa wosabatizidwa. Ndimasangalala ndikamakumbukira nthawi imene tinkalalikira limodzi. Koma iye anamwalira kutangotsala miyezi iwiri kuti abatizidwe.
Felisa: Ndimasangalala kwambiri ndikaganizira zoti azichemwali anga atatu amene ankanditsutsa, anasintha n’kukhala alongo. Timasangalalanso kukhala limodzi n’kumakambirana za Yehova komanso Mawu ake. Tingati Baibulo latithandiza kukhala ogwirizana. *
^ ndime 29 Panopa Araceli ali ndi zaka 87, Felisa 91 ndipo Ramoni ali ndi zaka 83. Onsewa akutumikira Yehova mwakhama. Lauri anamwalira mu 1990 ali wokhulupirika kwa Yehova.