Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukumbukira Mlengi Wathu Kuyambira Paunyamata

Kukumbukira Mlengi Wathu Kuyambira Paunyamata

Mbiri ya Moyo Wake

Kukumbukira Mlengi Wathu Kuyambira Paunyamata

YOSIMBIDWA NDI DAVID Z. HIBSHMAN

“Ngati ano alidi mapeto a moyo wanga, sindikukayika kuti ndakhala wokhulupirika kwa Yehova. Ndikum’pempha kuti andisamalilire David wanga. Zikomo kwambiri Yehova pondipatsa David, ndiponso potimangira banja lathu. Linali losangalatsadi ndiponso lachimwemwe chodzaza tsaya!”

TANGOGANIZIRANI mmene ndinamvera pamene ndinapeza mawu otsirizaŵa m’kabuku ka mkazi wanga kolembamo zochitika za tsiku ndi tsiku, pambuyo poika maliro ake m’March 1992. Miyezi isanu yokha m’mbuyo mwake tinapanga phwando lokumbukira kuti Helen anali atakwanitsa zaka 60 ali mu utumiki wa nthaŵi zonse.

Ndikukumbukira bwino tsiku limene Helen ndi ine tinakhala moyandikana kwambiri pamsonkhano wa ku Columbus, Ohio, U.S.A. m’chaka cha 1931. Helen anali asanakwanitse kwenikweni zaka 14, koma ankadziŵa bwino kufunika kwa msonkhano umenewo mwinanso kuposa ine. Changu cha Helen pa utumiki chinaoneka patangotha nthaŵi yochepa pamene iye ndi amayi ake amene anali amasiye anakhala apainiya, monga momwe alaliki a nthaŵi zonse a Mboni za Yehova amawatchulira. Iwo anasiya nyumba yawo yabwino kuti akalalikire kumadera a kumidzi a kumwera kwa dziko la United States.

Choloŵa Changa Chachikristu

Mu 1910, makolo anga pamodzi ndi ana awo aang’ono aŵiri, anasamuka kum’maŵa kwa Pennsylvania n’kupita mu mzinda wa Grove, kumadzulo kwa bomalo. Kumeneko anagula nyumba polipirako pang’ono chabe ndipo anakhala anthu olimbikira kwambiri m’chipembedzo cha Reformed Church. Posapita nthaŵi William Evans anawayendera. Iye anali Wophunzira Baibulo, dzina limene Mboni za Yehova zinkadziŵika nalo panthaŵiyo. Bambo, amene panthaŵiyi zaka zawo zinali cha m’ma 20, ndi mayi omwe anali ocheperako ndi zaka zisanu, anamvetsera zimene munthu wansangala wa ku Wales ameneyu anali kunena, ndipo anamuitana kuti adzadye naye chakudya. Posapita nthaŵi analandira choonadi cha Baibulo chimene anali kuphunzira.

Pofuna kuyandikira mpingo, bambo anasamutsira banja lawolo ku tauni ya Sharon, pamtunda wapafupifupi makilomita 25. Patatha miyezi ingapo, mu 1911 kapena 1912, Bambo ndi Mayi anabatizidwa. Charles Taze Russell, pulezidenti woyamba wa Watch Tower Society, ndi yemwe anakamba nkhani ya ubatizo. Ine ndinabadwa pa December 4, 1916, makolo anga ali kale ndi ana ena anayi. Panthaŵi ya kubadwa kwanga, panalengezedwa kuti: “Kwabadwa mbale wina woyenera kumukonda.” M’pamene panabwerera dzina langa lakuti David, kutanthauza kuti “Wokondedwa.”

Ndili ndi milungu inayi, ananditengera kumsonkhano kwa nthaŵi yoyamba. M’masiku akale amenewo, bambo wanga ndi achimwene anga anali kuyenda makilomita angapo kupita ku misonkhano ya mpingo ndipo mayi anali kutenga mlongo wanga ndi ine n’kukwera nafe galimoto. Misonkhanoyo inkachitika m’zigawo ziŵiri, chakum’maŵa ndi chakumadzulo. Tikakhala kunyumba nthaŵi zambiri macheza athu ankakhala okhudza nkhani za m’magazini ya Nsanja ya Olonda ndiponso Golden Age, dzina loyamba la Galamukani!

Kupindula Ndi Zitsanzo Zabwino

Mpingo wathu unayenderedwa ndi aulendo achipembedzo ambiri, amene pano timati okamba nkhani oyendayenda. Nthaŵi zambiri anali kukhala nafe tsiku limodzi kapena aŵiri. Wokamba nkhani amene sindimuiŵala anali Walter J. Thorn amene ‘anakumbukira Mlengi wake Wamkulu m’masiku a unyamata wake’. (Mlaliki 12:1) Pamene ndinali mnyamata ndinali kuperekeza Bambo wanga pokaonetsa “Seŵero la Pakanema la Chilengedwe.” Ilo linali nkhani yambali zinayi yoonetsa zithunzi ndiponso mawu okopedwa okhudza mbiri ya mtundu wa anthu.

Ngakhale kuti Mbale Evans ndi mkazi wake, Miriam, analibe ana, iwo anasanduka makolo ndiponso agogo auzimu a banja lathu. Nthaŵi zonse William anali kutchula Bambo anga kuti “Mwana wanga,” ndipo iye pamodzi ndi Miriam anaika mzimu wolalikira m’banja mwathu. Kumayambiriro kwa zaka za zana la 20, Mbale Evans ankapita ku Wales kukayambitsa choonadi cha Baibulo kudera lozungulira mzinda wa Swansea. Kumeneko anthu ankamutcha kuti mlaliki wa ku America.

Mu 1928, Mbale Evans anasiya ntchito yake ndipo anayamba kulalikira m’dera la kumapiri a ku West Virginia. Akulu anga aŵiri, Clarence amene anali wazaka 21 ndiponso Carl amene anali wazaka 19, anapita naye. Anyamata anayi tonsefe takhala zaka zambiri mu utumiki wa nthaŵi zonse. Kwenikweni tonsefe tinakhalako oyang’anira oyendayenda a Mboni za Yehova tili anyamata. Posachedwapa, a Mary, amene ali ang’ono awo wotsiriza a mayi, omwe pano ali ndi zaka za m’ma 90, anandilembera izi: “Tikuyamikiradi kuti Mbale Evans anali kuchita changu pa utumiki ndipo kuti anayendera mzinda wa Grove!” Mayi anga aang’ono ameneŵa, a Mary, alinso m’gulu la anthu amene anakumbukira Mlengi wawo kuyambira paunyamata.

Kupita Kumisonkhano Ikuluikulu

Bambo wokha ndiponso Clarence ndiwo anatha kupita ku msonkhano wosaiwalika wa ku Cedar Point, Ohio, mu 1922. Komabe pofika 1924 anali atagula galimoto, ndipo banja lathu lonse linapita kumsonkhano wa ku Columbus, Ohio. Anafe ankafuna kuti tizipeza tokha ndalama zokagulira zakudya zathu pamsonkhanowo umene unali wa masiku asanu ndi atatu. Makolo anga anali ndi maganizo akuti munthu aliyense m’banjalo ayenera kuphunzira kudzithandiza yekha. Motero tinkaŵeta nkhuku ndi akalulu ndiponso tinali ndi ming’oma ya njuchi. Ndipo anyamata tonsefe tinali ndi malo amene tinkatulako nyuzipepala nthaŵi zonse n’kumalandirako ndalama.

Pamene nthaŵi ya msonkhano wa ku Toronto, Canada, inakwana mu 1927, n’kuti tili ndi mn’gono wathu wamiyezi isanu ndi umodzi, wotchedwa Paul. Anandipatsa ntchito yakuti makolo anga akapita ku Toronto ndi ana enawo, ineyo ndikhale panyumba ndi kusamalira Paul mothandizidwa ndi a Mary, amayi anga aang’ono amene anali wokwatiwa. Anandifupa pondipatsa ndalama zokwanira madola khumi, zimene ndinagulira suti yatsopano. Nthaŵi zonse ankatiphunzitsa kuti tizivala bwino kumisonkhano ndiponso kuti tizisamalira zovala zathu.

Panthaŵi yomwe kunkachitika msonkhano wosaiwalika mu 1931 ku Columbus, Ohio, n’kuti Clarence ndi Carl atakwatira ndiponso akuchita upainiya pamodzi ndi akazi awo. Onse anali kukhala m’mahema oyenda nawo paulendo opangidwa panyumba. Carl anakwatira Claire Houston amene kwawo kunali kumzinda wa Wheeling ku West Virginia, ndipo n’chifukwa chake kumsonkhano wa ku Columbus ndinakhala mogundizana ndi Helen, mng’ono wake wa Claire.

Utumiki wa Nthaŵi Zonse

Ndinamaliza maphunziro a sekondale mu 1932 ndili ndi zaka 15, ndipo chaka chotsatira ndinakapatsira mkulu wanga Clarence, galimoto yogwiritsidwapo kale ntchito. Iye anali kuchita upainiya ku South Carolina. Ndinafunsira utumiki wa upainiya ndipo ndinayamba kuchita upainiya pamodzi ndi Clarence ndi mkazi wake. Helen naye n’kuti akuchita upainiya mu mzinda wa Hopkinsville, ku Kentucky, ndipo ndinamulembera kalata kwa nthaŵi yoyamba. Poyankha, iye anandifunsa kuti: “Kodi ndiwe mpainiya?”

Ndipo m’kalata yanga, imene Helen anaisunga kufikira imfa yake patatha zaka 60, ndinamuyankha kuti: “Inde ndine mpainiya, ndipo ndikufunitsitsa kuti ndidzakhalebe choncho.” M’kalatayo, ndinamuuza Helen nkhani yokhudza kugaŵira kabuku kotchedwa The Kingdom, the Hope of the World (Ufumu, Chiyembekezo cha Dziko Lapansi) kwa atsogoleri achipembedzo ndiponso kwa akuluakulu a khoti m’gawo langa lolalikira.

Mu 1933, Bambo anandipangira hema lokhala ndi matayala. Inali ngolo yaikulu ya mamitala 2.4 m’litali, ndipo mamitala 2 m’lifupi, ndiponso makoma ake anali opangidwa ndi chinsalu chokungidwa bwino mozungulira zitsulo zoonda zoongoka ndipo inali ndi zenera kutsogolo ndi kumbuyo komwe. Imeneyi ndiyo inali nyumba yanga kwa zaka zinayi zimene ndinkachita upainiya kuchokera panthaŵiyi.

Mu March 1934, tinalipo anthu asanu ndi atatu; Clarence ndi Carl, akazi awo, Helen ndi amayi ake, mlamu wake wa Clarence ndi ine, amene tinayamba ulendo kulowera cha kumadzulo kuti tikakhale nawo pamsonkhano mu mzinda wa Los Angeles, ku California. Anthu ena anakwera ndipo anali kugona mu ngolo yanga. Ine ndinkagona m’galimoto, ndipo enawo ankagona m’nyumba zolipira. Chifukwa chakuti galimoto inali kuwonongekawonongeka, tinakafika ku Los Angeles pa tsiku lachiŵiri la msonkhano wa masiku asanu ndi limodziwo. Pamsonkhanowo, pa March 26, Helen ndi ine tinasonyeza kudzipatulira kwathu kwa Yehova mwa ubatizo wa m’madzi.

Pamsonkhanowo Joseph F. Rutherford, amene panthaŵiyo anali pulezidenti wa Watch Tower Society, anakumana ndi apainiya onse. Iye anatilimbikitsa potiuza kuti tinali ankhondo olimba mtima omenyera choonadi cha Baibulo. Pachochitika chimenechi, panakonzedwa kuti apainiya athandizidwe mwakuwapatsa ndalama kuti apitirize utumiki wawo.

Maphunziro Okhala Mpaka Kalekale

Titabwerera kuchokera kumsonkhano ku Los Angeles, tonse tinagaŵana uthenga wabwino wa Ufumu ndi anthu a m’maboma onse a South Carolina, Virginia, West Virginia, ndiponso Kentucky. Patatha zaka zingapo Helen analemba za nthaŵi imeneyo kuti: “Kunalibe mpingo umene munthu ukanadalirapo, kapena mabwenzi oti akanathandiza, chifukwa chakuti tinalidi alendo m’dziko lachilendo. Koma tsopano ndadziŵa kuti ndinali kuphunzira. Ndinali kututa chuma.”

Iye anafunsa kuti: “Kodi mtsikana amagwiritsa ntchito bwanji nthaŵi yake akakhala kuti watalikirana ndi anzake ndiponso kumudzi kwawo? Komabe sikuti zinali zovuta kwambiri. Sindikumbuka zoti ndinasungulumwako. Ndinkaŵerenga kwambiri. Sitinalephereko kuŵerenga mabuku athu ofotokoza za Baibulo ndiponso kuphunzira. Ndinkakonda kukhala pafupi ndi amayi anga, kuphunzira kugwiritsa ntchito mosamala ndalama zimene tinali nazo, kugula zinthu, kusintha matayala akaphwa, kuphika, kusoka, ndiponso kulalikira. Sindinong’oneza bondo ngakhale pang’ono ndipo ndingakonde kuzichitanso zimenezi.”

Helen ndi mayi ake anali okhutira ndi ngolo imene ankakhalamo m’zaka zimenezo, ngakhale kuti mayi ake anali ndi nyumba yabwino kwambiri. Pambuyo pa msonkhano wa ku Columbus, Ohio, mu 1937, thanzi la mayi ake a Helen linaipiraipira, ndipo anagonekedwa m’chipatala. Iwo anamwalira akuchitabe utumiki wawo m’dera la Philippi, ku West Virginia, mu November 1937.

Kukwatira Ndiponso Kupitirizabe Utumiki

Pa June 10, 1938, Helen ndi ine tinakwatirana ndipo tinachita mwambo waung’ono m’nyumba imene Helen anabadwira m’dera la Elm Grove, kufupi ndi mzinda wa Wheeling, ku West Virginia. Mbale wathu wokondedwa, Evans, amene analidziŵitsa banja lathu za choonadi zaka zingapo ine ndisanabadwe, ndi amene anakamba nkhani ya ukwati. Pambuyo pa chikwaticho, Helen ndi ine tinakonza zakuti tibwerere ku ntchito ya upainiya kum’mawa kwa Kentucky, koma tinadabwa kwambiri pamene tinaitanidwa kuti tikachite ntchito yoyendera nthambi. Ntchito imeneyi inaphatikizamo kuyendera magulu a Mboni za Yehova kumadzulo kwa Kentucky ndi kumbali zina za Tennessee kukawathandiza pa utumiki wawo. Panthaŵiyo kunali olengeza Ufumu oterewa pafupifupi 75 okha mmalo onse amene tinayendera.

Panthaŵiyi, anthu ambiri anali ndi mzimu wa utundu, ndipo ndinkangoti ndimangidwa chifukwa cha kusaloŵererapo kwanga m’zadziko monga Mkristu. (Yesaya 2:4) Komabe chifukwa cha mbiri yanga ya ntchito yolalikira, ndinalandira chilolezo kuchokera ku bungwe lomwe limaumiriza anthu kuyamba usilikali chimene chinanditheketsa kupitirizabe kuchita utumiki wa nthaŵi zonse.

Pamene tinkayamba kuchita utumiki woyendayenda, pafupifupi aliyense ankanenapo kanthu pa za kuchepa kwa msinkhu wathu. Mu mzinda wa Hopkinsville, ku Kentucky, mlongo wina wachikristu anamukumbatira Helen mwachimwemwe chachikulu ndipo anamufunsa kuti: “Kodi ukundikumbukira?” Mu 1933, Helen anamulalikira mayiyu pa sitolo ya mwamuna wake. Iye anali mphunzitsi wa Sande sukulu, koma ataŵerenga buku limene Helen anamusiyira, iye anakaima kutsogolo kwa ophunzirawo ndipo anapepesa chifukwa chowaphunzitsa ziphunzitso zosakhala za Baibulo. Atasiya tchalitchicho, iye anayamba kulalikira choonadi cha Baibulo kudera kumene ankakhala. Helen ndi ine tinatumikira kumadzulo kwa Kentucky kwa zaka zitatu, ndipo mlongoyo pamodzi ndi mwamuna wake anachititsa kuti kunyumba kwawo kungosanduka kwathu.

Masiku amenewo tinkachita misonkhano ing’onoing’ono kumadera amene tinkakhala, ndipo A. H. Macmillan anachititsa umodzi wa misonkhanoyi. Iye anali atakhalako m’nyumba ya makolo a Helen pamene Helen anali wamng’ono, choncho pa nthaŵi ya msonkhanowo, iye anasankha zokhala ndi ife m’nyumba yathu yoyenda yotalika mamitala 5, mmene munali bedi lapadera. Nayenso anakumbukira Mlengi wake Wamkulu m’masiku a unyamata wake, atapatulira moyo wake kwa Yehova mu 1900, pamene anali wazaka 23.

Mu November 1941 ntchito ya abale oyendayenda inaimitsidwa kwa kanthaŵi, ndipo ine ndinapatsidwa ntchito ya upainiya m’dera la Hazard, ku Kentucky. Nthaŵi iyinso tinali kugwira ntchito pamodzi ndi mkulu wanga Carl ndi mkazi wake Claire. Kumeneku Joseph Houston, amene anali mwana wa mchimwene wake wa Helen, anadzakhala nafe, ndipo anayamba kuchita upainiya. Anakhala mu utumiki wa nthaŵi zonse kwa zaka pafupifupi 50, ndipo anamwalira mwadzidzidzi atadwala nthenda ya mtima mu 1992 pamene anali kutumikira mokhulupirika ku likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York.

Mu 1943 tinatumizidwa mumzinda wa Rockville, ku Connecticut. Uku kunali ngati kudziko lachilendo kwa Helen ndi ine chifukwa chakuti tinazoloŵera kulalikira kumwera. Mumzinda wa Rockville, Helen ankachititsa maphunziro a Baibulo apanyumba opitirira 20 pamlungu. M’kupita kwa nthaŵi, tinachita lendi chipinda choyenerera kukhala Nyumba ya Ufumu, ndipo mpingo waung’ono unakozedwa.

Pamene tinali kutumikira ku Rockville, tinaitanidwa kuti tikakhale nawo pa kalasi yachisanu ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower mu mzinda wa South Lansing, New York. Tinasangalala pakumva kuti Aubrey ndiponso Bertha Bivens, amene anali anzathu pamene tinali kuchita upainiya ku Kentucky adzakhalanso m’kalasi lathu.

Sukulu Ndiponso Ntchito Yathu Yatsopano

Ngakhale kuti tinali tidakali ana, anzathu ambiri m’kalasiyo anali ana kuposa ife. Inde, anali kukumbukira Mlengi wawo Wamkulu muunyamata wawo. Tinamaliza maphunziro athuwo mu July 1945, kumapeto kwa nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse. Pamene tinali kudikira gawo lathu lokachitako umishonale, tinali kutumikira pamodzi ndi mpingo wa Flatbush mu mzinda wa Brooklyn, ku New York. Potsiriza pake, pa October 21, 1946, ife pamodzi ndi anzathu a m’kalasi asanu ndi mmodzi kuphatikizapo banja la Bivens, tinakwera ndege kupita kumudzi wathu watsopano ku mzinda wa Guatemala umene uli m’dziko lotchedwanso Guatemala. Panthaŵiyo, kunali Mboni za Yehova zosakwana 50 m’dziko lonselo la ku Central America.

Mu April 1949 ena ochepa chabe mwa amishonalefe tinatumizidwa ku Quetzaltenango, mzinda wachiŵiri m’dzikolo pa ukulu ndiponso kufunika kwake. Mzinda umenewu uli pamtunda wa mamitala 2,300 kuchokera pamwamba pa nyanja, ndipo mpweya wake wochokera kumapiri umachita kuti yeziyezi. Helen ananena mwachidule ntchito yathu kumeneku polemba kuti: “Tinali ndi mwaŵi wolalikira m’matauni ndiponso m’midzi yambiri. Tinkadzuka pafupifupi folo koloko m’maŵa ndi kukakwera basi (imene nthaŵi zambiri mawindo ake ankakhala otsekedwa ndi masaka) kupita ku tauni ina yakutali. Ndipo kumeneko tinkalalikirako kwa maola pafupifupi asanu ndi atatu ndipo tinkabwerako madzulo.” Lero kumadera ambiri otereŵa kuli mipingo, kuphatikizapo ina isanu ndi umodzi ya ku Quetzaltenango.

Pasanathe nthaŵi yaitali panali chilengezo chakuti pakufunika amishonale oti akatumikire ku Puerto Barrios, mzinda wachitatu mwa mizinda yaikuluikulu ya m’Guatemala ndipo uli m’gombe la Caribbean. Anzathu okondedwa banja la Bivens, amene tinatumikira nawo pamodzi kwa zaka zisanu ku Guatemala, anali m’gulu la amene anatumizidwa ku gawo latsopanoli. Zinatiwawa kwambiri mmene timasiyana nawo ndipo tinasungulumwa kwabasi. Chifukwa chakuti panyumba ya amishonalepo panangotsala Helen ndi ine, tinasamuka kupita kunyumba ina yaing’ono. Mu 1955, Helen ndi ine tinavomera kupita kugawo lina ku mzinda wina wa dera lotentha wotchedwa Mazatenango. Mng’ono wanga wotsiriza, Paul, ndi mkazi wake Dolores, amene anamaliza sukulu ya Gileadi mu 1953, anali atatumikira kumeneku ife titangotsala pang’ono kufikako.

Pofika 1958 tinali ndi Mboni zoposa 700, mipingo 20, ndi madera atatu m’dziko la Guatemala. Helen ndi ine tinachita nawonso ntchito yoyendayenda, kuyendera magulu ang’onoang’ono a Mboni ndiponso kuyendera mipingo ingapo, kuphatikizapo wa ku Quetzaltenango uja. Kenaka, m’mwezi wa August 1959, tinaitanidwa kuti tibwerere mumzinda wa Guatemala, kumene tinakakhala pa ofesi yanthambi. Ndinapatsidwa ntchito ya panthambi, pamene Helen anapitiriza utumiki wa umishonale kwa zaka 16 zotsatira. Kenaka nayenso anayamba kugwira ntchito pa ofesi yanthambi.

Madalitso Owonjezereka

Zikuoneka kuti m’zaka za m’mbuyomo nthaŵi zonse ndinali wamng’ono kwambiri pa onse otumikira Yehova. Koma tsopano nthaŵi zambiri wamkulu kwambiri ndimakhala ine, monga momwe zinalili pamene ndinali pa sukulu ya nthambi ku Patterson, New York mu 1996. Pakuti ine ndinathandizidwa kwambiri ndi achikulire pa unyamata wanga, nanenso ndimaona kuti ndi mwaŵi wanga pothandiza achinyamata ambiri, m’zaka makumi angapo zaposachedwapa, amene akufunitsitsa kukumbukira Mlengi wawo paunyamata wawo.

Yehova akupitiriza kupereka madalitso pa anthu ake kuno ku Guatemala. Mu 1999 kunali mipingo yopitirira 60 mu mzinda wa Guatemala. Ndipo kumpoto, kumwera, kum’maŵa, ndiponso kumadzulo, kuli mipingo ina yambiri ndiponso alaliki zikwizikwi a uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ofalitsa a Ufumu osakwana 50 amene tinawapeza titangofika, pafupifupi zaka 53 zapitazo awonjezeka mpaka kupitirira 19,000!

Pali Zifukwa Zambiri Zothokozera

Palibe munthu amene amakhala popanda mavuto, koma nthaŵi zonse tingathe ‘kum’senza Yehova nkhaŵa zathu.’ (Salmo 55:22) Nthaŵi zambiri iye amatichirikiza kudzera m’chilimbikitso cha mabwenzi otikonda. Mwachitsanzo, zaka zochepa asanamwalire, Helen anandipatsa kachitsulo kamene kanasindikizidwa mawu a pa Ahebri 6:10 pamene amati: “Mulungu sali wopanda chilungamo kuti sangasamale za ntchito yanu ndi chikondi chanu chimene mwasonyeza pa Iye potumikira anthu Ake ndi popitirizabe kutero.”​—Weymouth.

Ena mwa mawu amene iye analemba pa kapepala kamene anaphatikapo anali akuti: “Wokondedwa wanga wamtengo wapatali, sindingathe kukupatsa zinthu zambiri, kupatulako CHIKONDI CHANGA CHONSE . . . Lemba ili ndilokuyenera kwambiri, ndipo ndikukupempha kuti uliike pa desiki yako, osati chifukwa chakuti ndakupatsa ndine, koma chifukwa chakuti ndilogwirizana ndi iwe pa utumiki wako umene wauchita kwa zaka zambiri. Mpaka pano, kachitsulo kameneka kali khale pa desiki ya mu ofesi yanga ku nthambi ya ku Guatemala.

Ndatumikira Yehova kuyambira pa unyamata wanga, ndipo tsopano pokhala m’zaka zanga zauchikulire, ndikuthokoza Yehova chifukwa cha thanzi langa labwino limene limanditheketsa kuchita ntchito zimene ndapatsidwa. Ndikamaŵerenga Baibulo monga mwa nthaŵi zonse, nthaŵi zambiri ndimapeza malemba amene ndikuganiza kuti wokondedwa wanga Helen akadawalemba mzere kunsi m’Baibulo lake. Zimenezi zinandichitikira pamene ndinali kuŵerenganso Salmo 48:14 limene limati: “Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu ku nthaŵi za nthaŵi: Adzatitsogolera kufikira imfa.”

Ndimasangalala kwambiri kuuza ena za tsiku la chiukiriro limene tikuliona m’tsogolo mwathu pamene anthu a mitundu yonse a m’mbuyo adzakhala akulandira okondedwa awo kuchokera ku imfa kupita m’dziko latsopano. N’chiyembekezo chosangalatsa bwanji! Padzakhalatu misozi yachimwemwe imene idzakhetsedwe uku tikukumbukira kuti n’zoonadi Yehova ndi Mulungu ‘amene amatonthoza ochepetsedwa’!​—2 Akorinto 7:6, NW.

[Chithunzi patsamba 25]

Kuyambira pamwamba chakumanzere kumapita kumanja mukuona: Mayi, Bambo, Azakhali anga a Eva, ndi achimwene anga Carl ndi Clarence, mu 1910

[Zithunzi patsamba 26]

Ndili ndi Helen mu 1947 ndi mu 1992