Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kutumikira Limodzi ndi Mlonda

Kutumikira Limodzi ndi Mlonda

Kutumikira Limodzi ndi Mlonda

“Ambuye [“Yehova,” NW] inu, ine ndiimabe pamwamba pa nsanja nthaŵi ya usana, ndipo ndiikidwa mu ulonda wanga usiku wonse.”​—YESAYA 21:8.

1. Kodi Yehova mwiniyo ali mboni ku malonjezo aakulu ati?

YEHOVA ndi Wachifuno Wamkulu. Mngelo wopandukayo yemwe anadzakhala Satana Mdyerekezi sangathe kuchita kanthu kalikonse kulepheretsa chifuno Chake chachikulu choyeretsa dzina Lake ndi kukhazikitsa Ufumu waulemerero kulamulira dziko lapansi la paradaiso. (Mateyu 6:9, 10) Pansi pa ulamuliro umenewo, mtundu wa anthu udzadalitsidwadi. Mulungu ‘adzameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse.’ Anthu okondwa, ogwirizanawo adzasangalala ndi mtendere ndi chitukuko kunthaŵi yomka muyaya. (Yesaya 25:8; 65:17-25) Yehova iye mwiniyo alitu mboni ku malonjezo aakulu ameneŵa!

2. Kodi ndi mboni zaumunthu ziti zomwe Yehova waziutsa?

2 Komabe, Mlengi Wamkuluyo alinso ndi mboni zaumunthu. Chikristu chisanakhaleko, ‘mtambo wa mboni,’ kuyambira pa Abele, kaŵirikaŵiri unali kuthamanga makaniwo a chipiriro pakatikati pa mikhalidwe yovuta zedi. Zitsanzo zawo zabwinozo zimalimbikitsa Akristu okhulupirika lerolino. Kristu Yesu ali chitsanzo chabwino koposa cha mboni yolimba mtima. (Ahebri 11:1–12:2) Mwachitsanzo, kumbukirani umboni wake wotsiriza kwa Pontiyo Pilato. Yesu anati: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.” (Yohane 18:37) Kuchokera m’chaka cha 33 C.E. kudzafika m’chaka chino cha 2000 C.E., Akristu akhama atsatira chitsanzo cha Yesu ndipo akupitirizabe kuchitira umboni, kulengeza “zazikulu za Mulungu” molimba mtima.​—Machitidwe 2:11.

Mpatuko wa Babulo

3. Kodi Satana watsutsa motani umboni wonena za Yehova ndi chifuno chake womwe ukuperekedwa?

3 Kwa zaka zambiri ndithu, Mdani wamkuluyo Satana Mdyerekezi, wayesetsa m’njira zoipa kwambiri kutsutsa umboni wa mboni za Mulungu. Monga “atate wake wa bodza,” “chinjoka chachikulu . . . , njoka yokalambayo” wakhala “wonyenga wa dziko lonse.” Iyeyu wamenya nkhondo mosatopa polimbana ndi awo amene “asunga malamulo a Mulungu,” makamaka m’masiku otsiriza ano.​—Yohane 8:44; Chivumbulutso 12:9, 17.

4. Kodi Babulo Wamkulu anakhalako motani?

4 Zaka ngati 4,000 zapitazo, pambuyo pa Chigumula cha m’tsiku la Nowa, Satana anautsa Nimrode, “mpalu wamphamvu pamaso pa [“wotsutsana ndi,” NW] Yehova.” (Genesis 10:9, 10) Mzinda waukulu kwambiri wa Nimrode, Babulo (Babele), unadzakhala chimake cha chipembedzo cha ziwanda. Yehova atasokoneza chinenero cha omanga nsanja ya Babele, anthu anamwazikana padziko lonse lapansi, ndipo chipembedzo chawo chonyengacho anapita nacho limodzi. Chotero Babulo anadzakhala gwero la ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga, chotchulidwa m’buku la Chivumbulutso kuti Babulo Wamkulu. Buku limeneli limalosera chiwonongeko cha dongosolo la chipembedzo chakale limeneli.​—Chivumbulutso 17:5; 18:21.

Mtundu wa Mboni

5. Kodi ndi mtundu uti umene Yehova anaupanga kukhala mboni yake, ndipo kodi n’chifukwa chiyani analola kuti utengeredwe kuukapolo?

5 Pafupifupi zaka 500 pambuyo pa nthaŵi ya Nimrode, Yehova anapanga mbadwa za Abrahamu wokhulupirikayo kukhala mtundu wa Israyeli ndikuti ukhale mboni Yake yapadziko lapansi. (Yesaya 43:10, 12) Anthu ambirimbiri a mtunduwo anatumikiradi Yehova mokhulupirika. Komabe, m’kupita kwa zaka mazana ambiri, zikhulupiriro zonyenga za mitundu yoyandikana nayo zinaipitsa Israyeli, ndipo anthu a pangano la Yehova analeka kum’lambira mwakuti anayamba kulambira milungu yonyenga. Choncho, m’chaka cha 607 B.C.E., gulu lankhondo la Babulo, motsogozedwa ndi Mfumu Nebukadinezara, linawononga Yerusalemu ndi kachisi wake ndi kugwira Ayuda ambiri kuwatengera kuukapolo mu Babulo.

6. Kodi ndi uthenga wabwino wotani umene mlonda waulosi wa Yehova analengeza, ndipo ndi liti pamene unakwaniritsidwa?

6 Chinalitu chipambano chosasimbika ku chipembedzo chonyenga chimenecho! Komabe, kulamulidwa ndi Ababulo kumeneku kunali kwa kanthaŵi kochepa chabe. Zaka ngati 200 zimenezi zisanachitike, Yehova analamula kuti: “Muka ika mlonda anene chimene achiona.” Kodi mlonda ameneyu anali kudzalengeza nkhani yoti chiyani? “Babulo wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yake asweka, nagwa pansi.” (Yesaya 21:6, 9) Zinachitikadi kuti m’chaka cha 539 B.C.E., chilengezo chaulosi chimenecho chinakwaniritsidwa. Babulo Wamphamvu anagwa, ndipo kenako anthu apangano la Mulungu analinso okhoza kubwerera ku dziko lawo.

7. (a) Kodi Ayudawo anaphunziranji pa chilango cha Yehova? (b) Pambuyo pa ukapolowo, kodi Ayuda anagwa m’misampha yotani, ndipo ndi zotsatira zotani?

7 Ayuda obwererawo anaphunzira zambiri zomwe zinawathandiza kulekeratu kulambira mafano ndi kupembedza mizimu. Komabe, m’kupita kwa zaka, anagwa m’misampha inanso. Ena anakodwa ndi misampha ya nthano zachigiriki. Ena anali kugogomezera miyambo ya anthu pa Mawu a Mulungu. Ndiponso ena ananyengedwa ndi utundu. (Marko 7:13; Machitidwe 5:37) Pomadzafika nthaŵi ya kubadwa kwa Yesu, mtunduwu unali utatembenuka kale kuchoka ku kulambira koyera. Pamene kuli kwakuti Ayuda ena anamvetsera uthenga wabwino wa Yesu, mtundu wonsewo unam’kana iye moteronso umenewu unakanidwa ndi Mulungu. (Yohane 1:9-12; Machitidwe 2:36) Mtundu wa Israyeli sunalinso mboni ya Mulungu, ndiyeno m’chaka cha 70 C.E., Yerusalemu kachiŵirinso anapasulidwa, panthaŵi ino ndi gulu lankhondo la Aroma.​—Mateyu 21:43.

8. Kodi ndani yemwe anadzakhala mboni ya Yehova, ndipo n’chifukwa chiyani chenjezo la Paulo kwa mboniyi linali lapanthaŵi yake?

8 Panthaŵiyi, “Israyeli wa Mulungu” wachikristu anali atabadwa, chotero iyeyu tsopano anadzakhala mboni ya Mulungu ku mitundu ya anthu. (Agalatiya 6:16) Mwamsanga ndithu, Satana anakonza zowononga mtundu wauzimu watsopanowu. Cha kumapeto a zaka zana loyamba, zisonkhezero zampatuko zinali kuonekera m’mipingo. (Chivumbulutso 2:6, 14, 20) Chenjezo la Paulo lapanthaŵi yake linali lakuti: “Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu.”​—Akolose 2:8.

9. Monga momwedi Paulo anachenjezera, kodi n’zochitika zotani zomwe zinachititsa kukhalako kwa Matchalitchi Achikristu?

9 Pang’ono ndi pang’ono, nthano zachigiriki, maganizo a chipembedzo cha Babulo, ndipo pambuyo pake “nzeru” za anthu monga chiphunzitso cha chisinthiko ndi maphunziro apamwamba ofufuza Baibulo zinaipitsa chipembedzo cha ambiri odzinenera kukhala Akristu. Zinalidi monga momwe Paulo analoserera kuti: “Ndidziŵa ine kuti, nditachoka ine, adzaloŵa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo; ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.” (Machitidwe 20:29, 30) Chotsatirapo chake cha mpatuko umenewu, Matchalitchi Achikristu anapangidwa.

10. Kodi n’zochitika zotani zimene zinasonyeza kuti si aliyense amene anagonjera ku kulambira koipitsidwa kochitidwa m’Matchalitchi Achikristu?

10 Awo amene anali odzipatulira kotheratu pa kulambira koyera anafunikira kuti ‘alimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chopatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.’ (Yuda 3) Kodi umboni wa kulambira koyera ndi wa Yehova unali kudzatha padziko lapansi? Ayi. Pamene nthaŵi ya chiwonongeko cha wopandukayo Satana ndi ntchito zake zonse inali kuyandikira, zinaonekeratu kuti si aliyense yemwe anagonjera ku kulambira kwa mpatuko kochitikira m’Matchalitchi Achikristu. Chakumapeto kwa zaka zana la 19, ku Pittsburgh, Pennsylvania, m’dziko la United States of America, gulu la ophunzira Baibulo okhulupirika linakhazikitsidwa ndipo pambuyo pake linadzakhala phata la gulu la mboni za Mulungu zamakono. Akristu ameneŵa anachita chidwi kwambiri ndi umboni wa m’Malemba wakuti mapeto a dongosolo la dziko lamakono lino ali pafupi. Mogwirizanadi ndi ulosi wa m’Baibulo, “mapeto” a dziko ili anayambadi m’chaka cha 1914, ndipo anasonyezedwa ndi kuulika kwa nkhondo yoyamba yapadziko lonse. (Mateyu 24:3, 7) Pali umboni wamphamvu wakuti Satana ndi khamu lake lonse la ziwanda anachotsedwa kumwamba pambuyo pa chaka chimenecho. Zaka zana la 20 lodzala ndi mavuto lino lapereka umboni woonekeratu wa zochita za Satana ndi kukwaniritsidwa kwa zizindikiro za kukhalapo kwa Yesu monga mfumu mu mphamvu ya Ufumu wakumwamba.​—Mateyu, machaputala 24 ndi 25; Marko, chaputala 13; Luka, chaputala 21; Chivumbulutso 12:10, 12.

11. Kodi Satana anayesa kuchitanji, komano kodi ndi motani mmene kuyesa kwakeko kunalepherera?

11 Mu June 1918, Satana anayesa mwaphuma kufafaniza ophunzira Baibulo amenewo, omwe panthaŵiyo anali akulalikira m’mayiko ambiri. Ndiponso iye ankafuna kuwononga bungwe lawo lalamulo la Watch Tower Bible and Tract Society. Akuluakulu a Sosaite anawaponya m’ndende, kuwaimba milandu yabodza youkira boma, monga momwe Yesu anam’chitira m’zaka zana loyamba. (Luka 23:2) Koma m’chaka cha 1919, akuluakulu ameneŵa anamasulidwa, kuwatheketsa kupitirizabe utumiki wawo. Pambuyo pake, anawauza kuti analibe mlandu wina uliwonse.

“Mlonda” Pantchito Yake

12. Ndani lerolino yemwe akupanga gulu la “mlonda” wa Yehova, ndipo kodi iwo amagwira motani ntchito yawo?

12 Choncho pamene “nthaŵi ya chimaliziro” inayamba, Yehova analinso ndi mlonda m’malo ake, kuchenjeza anthu za zochitika zokhudza kukwaniritsidwa kwa chifuno Chake. (Danieli 12:4; 2 Timoteo 3:1) Kufikira lerolino, mlonda ameneyo, amene ndi Akristu odzozedwa, Israyeli wa Mulungu, wakhala akuchita mogwirizana ndi mmene Yesaya analongosolera mlonda woloseredwayo kuti: “Iye adzamvetsera ndi khama mosamalitsa. Ndipo iye anafuulitsa ngati mkango, Ambuye inu, ine ndiimabe pamwamba pansanja nthaŵi ya usana, ndipo ndiikidwa mu ulonda wanga usiku wonse.” (Yesaya 21:7, 8) Ameneyu alidi mlonda yemwe amagwira ntchito yakeyo mosamalitsadi!

13. (a) Kodi mlonda wa Yehova walengeza uthenga wotani? (b) Kodi tinganene kuti Babulo Wamkulu wagwa m’lingaliro lotani?

13 Kodi mlonda ameneyu anaonanji? Kachiŵirinso, mlonda wa Yehova, gulu la mboni zake, linalengeza kuti: “Babulo wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yake asweka, nagwa pansi.” (Yesaya 21:9) Panthaŵi ino, pambuyo pa nkhondo yoyamba yapadziko lonse, ali Babulo Wamkulu, ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga, yemwe wagwetsedwa, kuchotsedwa pamalo ake aulamuliro apamwambawo. (Yeremiya 50:1-3; Chivumbulutso 14:8) Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti Nkhondo Yaikulu, monga momwe ankaitchulira panthaŵiyo, inayambira m’mayiko achikristu, momwe atsogoleri achipembedzo kumbali zonse ziŵiri ankakolezera nkhondo mwa kulimbikitsa anyamata awo anyongawo kupita kunkhondo. Chinalitu chochititsa manyazi zedi! M’chaka cha 1919, Babulo Wamkulu sanakhoze kulepheretsa Ophunzira Baibulo, monga momwe Mboni za Yehova zinkadziŵikira panthaŵiyo, kuthaŵa kuchoka m’chikhalidwe chawo chofookacho ndikuyamba ndawala yochitira umboni padziko lonse yomwe ikupitirizabe lerolino. (Mateyu 24:14) Chimenecho chinali chizindikiro chakuti Babulo Wamkulu anali atagwa, monganso momwe kumasulidwa kwa Israyeli m’zaka zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E. kunalili chizindikiro cha kugwa kwa Babulo wakaleyo.

14. Kodi ndi magazini iti yomwe gulu la Yehova la mlonda laigwiritsa ntchito kwambiri, ndipo kodi Yehova wadalitsa motani kugwiritsidwa ntchito kwakeko?

14 Gulu la mlonda limeneli nthaŵi zonse lachitadi ntchito yake mwakhama ndi kufunitsitsa kuchita chimene chili chabwino. Mu July 1879, Ophunzira Baibulo ameneŵa anayamba kufalitsa magazini ino, yomwe panthaŵiyo inkadziŵika ndi dzina lakuti Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence (Nsanja ya Olonda ya Ziyoni ndi Yolengeza Kukhalapo kwa Kristu). Kuyambira m’chaka cha 1879 kudzafika December 15, 1938, kope lililonse linali ndi mawu pachikuto chake chakutsogolo akuti “‘Mlonda, Nthaŵi Yanji ya Usiku?’​—Yesaya 21:11.” * Kwa zaka ngati 120, Nsanja ya Olonda mokhulupirika yakhala ikuyang’anira zochitika m’dzikoli ndi matanthauzo ake aulosi. (2 Timoteo 3:1-5, 13) Gulu la mlonda la Mulungu ndi anzake a “nkhosa zina” agwiritsa ntchito magazini imeneyi polengeza mwakhama ku mtundu wa anthu kuti nthaŵi yakuti Ufumu wa Kristu utsimikizire uchifumu wa Yehova yayandikira. (Yohane 10:16) Kodi umboni umenewu wadalitsidwa ndi Yehova? Eya, kuchokera pa kusindikizidwa kwa makope 6,000 a magazini yoyamba m’chaka cha 1879, makope a Nsanja ya Olonda oposa 22,000,000 afikira pa kufalitsidwa dziko lonse lapansi m’zinenero 132, ndipo 121 mwa zinenero zimenezi zimatuluka panthaŵi imodzi ndi Chingelezi. N’koyenereratu kwabasi kuti magazini yachipembedzo yofalitsidwa koposa padziko lapansi ikhaledi yomwe imakweza dzina la Mulungu woona, Yehova!

Kuyeretsa Kopita Patsogolo

15. Kodi ndi kuyeretsa kopita patsogolo kotani kumene kunayamba kale kwambiri ngakhale 1914 isanafike?

15 M’kati mwa zaka 40 n’kumabwerabe kudzafika pomwe Ufumu wakumwamba wa Kristu unayamba kulamulira m’chaka cha 1914, Ophunzira Baibulo anali atamasuka ku ziphunzitso zambiri za Matchalitchi Achikristu zomwe sizinali zozikidwa pa Baibulo, monga kubatiza makanda, kusafa kwa moyo wa munthu, purigatoriyo, chizunzo cha m’moto wa helo, ndi Utatu wa Mulungu. Koma panafunika nthaŵi yowonjezereka kuti achotseretu malingaliro onse olakwika. Mwachitsanzo, m’ma 1920 Ophunzira Baibulo ambiri ankavala naphini wokhala ndi zizindikiro za mtanda ndi korona, ndiponso ankachita nawo mapwando a Khirisimasi ndi matchuthi enanso achikunja. Komabe, kuti kulambira kukhale koyera, zinthu zonse zokhudza kupembedza mafano ziyenera kuchotsedwa. Mawu a Mulungu, Baibulo Lopatulika, n’lomwe liyenera kukhala maziko okhawo a chikhulupiriro ndi njira ya moyo ya Mkristu. (Yesaya 8:19, 20; Aroma 15:4) N’kulakwa kuwonjezera pa Mawu a Mulungu kapena kuchotsapo china chilichonse pa mawuwo.​—Deuteronomo 4:2; Chivumbulutso 22:18, 19.

16, 17. (a) Ndi malingaliro olakwika ati omwe gulu la mlonda linakhala likuwakhulupirira kwa zaka zambiri? (b) Kodi malongosoledwe olondola onena za “guwa la nsembe” ndi “choimiritsa” mu “Aigupto” n’ngotani?

16 Chitsanzo chimodzi chigogomeza kufunika kwa mfundo imeneyi. M’chaka cha 1886 pamene C. T. Russell analemba buku lomwe linadzatchedwa The Divine Plan of the Ages, buku limeneli linali ndi tchati chogwirizanitsa nyengo za mtundu wa anthu ndi Piramidi Yaikulu mu Aigupto. Panali malingaliro akuti chipilala cha chikumbutso cha Farao Khufu chimenechi chinali choimiritsa chonenedwa pa Yesaya 19:19, 20 kuti: “Tsiku limenelo padzakhala guwa la nsembe la Yehova pakati pa dziko la Aigupto, ndi choimiritsa cha Yehova m’malire ake. Ndipo chidzakhala chizindikiro ndi mboni ya Yehova wa makamu m’dziko la Aigupto.” Kodi chipilalacho chingagwirizane motani ndi Baibulo? Chabwino, mwachitsanzo, utali wa tinjira tina mu Piramidi Yaikuluyo akuti tinali kusonyeza nthaŵi ya kuyambika kwa ‘chisautso chachikulu’ chonenedwa pa Mateyu 24:21, monga momwe ankamvera panthaŵiyo. Ophunzira Baibulo ena anatanganidwa kwambiri ndi kuyeza zinthu zosiyanasiyana za mu piramidiyo kuti azindikire zinthu monga tsiku lomwe adzapita kumwamba!

17 Chinthu chimenechi chimene anachitcha kuti Baibulo Lamwala chinalemekezedwa kwa zaka zambiri, kufikira pamene Nsanja ya Olonda ya November 15 ndi ya December 1, 1928, zinamveketsa bwino kuti Yehova sanafunikire chipilala chamwala chomangidwa ndi afarao achikunjawo ndiponso chokhala ndi zizindikiro za ziwanda za kukhulupirira nyenyezi m’kati mwake kuti atsimikizire umboni woperekedwa m’Baibulo. M’malo mwake, ulosi wa Yesaya unaoneka kukhala uli ndi tanthauzo lauzimu. Monga momwe kwasonyezedwera pa Chivumbulutso 11:8, “Aigupto” ali dziko la Satana lophiphiritsira. “Guwa la nsembe la Yehova” limatikumbutsa za nsembe zolandirika zoperekedwa ndi Akristu odzozedwa adakali padziko lapansi pano kwa kanthaŵi kochepa. (Aroma 12:1; Ahebri 13:15,16) Choimiritsa “m’malire ake” a Aigupto chikusonya ku mpingo wa Akristu odzozedwa, womwe ndi “mzati ndi mchirikizo wa choonadi” womwenso uli ngati mboni mu “Aigupto,” dziko lomwe kwangotsala kanthaŵi kochepa chabe kuti achokemo.​—1 Timoteo 3:15.

18. (a) Kodi Yehova wapitiriza motani kumveketsa zinthu kwa Ophunzira Baibulo okhulupirika? (b) Ngati Mkristu sakumvetsa malongosoledwe a malemba, kodi ndi malingaliro anzeru ati omwe ayenera kukhala nawo?

18 Pamene zaka zikupita, Yehova akupitirizabe kutipatsa mafotokozedwe owonjezereka a choonadi, kuphatikizapo kumvetsa bwino mawu ake a ulosi. (Miyambo 4:18) M’zaka zaposachedwapa, talimbikitsidwa kuonanso momvetsa bwino zedi, mwa zina, za mbadwo womwe sudzatha kuchoka mapeto asanadze, za fanizo la nkhosa ndi mbuzi, za chonyansa ndi nthaŵi pamene chidzaima pamalo oyera, za pangano latsopano, za kusandulika, ndinso za masomphenya a kachisi a m’buku la Ezekieli. Kungakhaledi kovuta nthaŵi zina kumvetsa malongosoledwe atsopano otereŵa, koma zifukwa zoperekera mafotokozedwe atsopanowo zimakhala zomveka m’kupita kwa nthaŵi. Ngati Mkristu sakumvetsetsa malongosoledwe atsopano a malemba, adzachita bwino kunenanso modzichepetsa mawu a mneneri Mika akuti: “Ndidzadikira Mulungu wa chipulumutso changa.”​—Mika 7:7.

19. Kodi otsalira odzozedwa ndi anzawo a nkhosa zina asonyeza motani kulimba mtima ngati mkango m’masiku otsiriza ano?

19 Kumbukirani kuti mlonda ‘akufuulitsa ngati mkango kuti, Yehova inu, ine ndiimabe pamwamba pansanja nthaŵi ya usana, ndipo ndiikidwa mu ulonda wanga usiku wonse.’ (Yesaya 21:8) Otsalira odzozedwa asonyeza kulimba mtima ngati mkango povumbula chipembedzo chonyenga ndi kusonyeza anthu njira yopezera ufulu. (Chivumbulutso 18:2-5) Monga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” apereka mabaibulo, magazini, ndi zofalitsa zinanso zambiri m’zinenero zambirimbiri monga “zakudya panthaŵi yake.” (Mateyu 24:45) Atsogolera pa kusonkhanitsa “khamu lalikulu . . . ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” Ameneŵanso ayeretsedwa ndi magazi ansembe ya Yesu ndipo asonyeza kulimba kwawo mtima ngati mkango ‘potumikira [Mulungu] usana ndi usiku.’ (Chivumbulutso 7:9, 14, 15) Kodi n’chiyani chomwe chakhala chipatso chaka chathachi kwa gulu laling’ono la Mboni za Yehova zodzozedwa zomwe zidakalipobe ndi moyo padziko lapansi pano komanso kwa anzawo, a khamu lalikulu? Nkhani yathu yotsatira idzafotokoza.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Kuyambira January 1, 1939, mawuŵa anawasintha ndi kuikapo akuti “‘Adzadziŵa kuti Ine ndine Yehova.’​—Ezekieli 35:15.”

Kodi Mukukumbukira?

Kodi ndi mboni ziti zomwe Yehova waziutsa m’kupita kwa zaka?

Kodi chiyambi cha Babulo Wamkulu n’chotani?

Kodi n’chifukwa ninji Yehova analola Yerusalemu, likulu la mtundu wa mboni zake, kuwonongedwa mu 607 B.C.E.? ndiponso mu 70 C.E.?

Kodi a m’gulu la Yehova la mlonda ndi anzawo aonetsa mzimu wotani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 7]

“Ambuye inu, ine ndiimabe pamwamba pa nsanja”

[Zithunzi patsamba 10]

Gulu la Yehova la mlonda likugwira ntchito yake mosamalitsadi