Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mamembala Atsopano a Bungwe Lolamulira

Mamembala Atsopano a Bungwe Lolamulira

Mamembala Atsopano a Bungwe Lolamulira

LOŴERUKA, pa October 2, 1999, Msonkhano wa Pachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylavia unatha ndi chilengezo chimene anthu sanachiyembekezere. Anthu okwana 10,594 amene anapezekapo kapena kulunzanitsidwa kudzera m’matelefoni anadzazidwa ndi chisangalalo kumva kuti Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova lili ndi mamembala anayi atsopano. Mamembala atsopanoŵa, omwe onse ndi Akristu odzozedwa, mayina awo ndi, Samuel F. Herd; M. Stephen Lett; Guy H. Pierce; ndi David H. Splane.

• Samuel Herd anayamba upainiya m’chaka cha 1958 ndipo kuyambira chaka cha 1965 mpaka 1997 anali woyang’anira dera komanso woyang’anira chigawo. Kenako iye pamodzi ndi mkazi wake, Gloria, anakakhala m’banja la Beteli la ku United States kumene Mbale Herd wakhala akutumikira mu Dipatimenti ya Utumiki. Iye analinso kuthandiza mu Komiti ya Utumiki.

• Stephen Lett anayamba upainiya mu December 1966, ndiye kuyambira chaka cha 1967 mpaka 1971 anali kutumikira pa Beteli ku United States. Mu October 1971, anakwatira mkazi wake, Susan, n’kupita kukatumikira monga mpainiya wapadera. Kuchokera m’chaka cha 1979 mpaka 1998 anali woyang’anira dera. Kuyambira mu April 1998, iye pamodzi ndi Susan akhala ali m’banja la Beteli la ku United States. Kumeneko anali kugwira ntchito mu Dipatimenti ya Utumiki komanso anali kuthandiza mu Komiti Yophunzitsa.

• Guy Pierce anali kusamalira banja ndiyeno pamodzi ndi mkazi wake anayamba upainiya mu April 1982. Anatumikira monga woyang’anira dera kuyambira chaka cha 1986 kufikira 1997, pamene iye ndi mkazi wake, Penny, anakakhala m’banja la Beteli la ku United States. Mbale Pierce anali kuthandiza mu Komiti ya Ogwira Ntchito.

• David Splane anayamba upainiya mu September 1963. Iye anamaliza maphunziro la Gileadi a kalasi la 42 ndipo anali mmishonale ku Senegal mu Afirika, ndiyeno kwa zaka 19 anali mu ntchito yoyang’anira dera ku Canada. Iye pamodzi ndi mkazi wake Linda akhala pa Beteli ya ku United States kuyambira chaka cha 1990, kumene Mbale Splane wakhala akugwira ntchito mu Dipatimenti ya Utumiki komanso mu Dipatimenti Yolemba. Kuyambira mu 1998, anali kuthandiza mu Komiti Yolemba.

Kuwonjezera pa mamembala anayi atsopanoŵa, m’Bungwe Lolamulira tsopano muli, C. W. Barber, J. E. Barr, M. G. Henschel, G. Losch, T. Jaracz, K. F. Klein, A. D. Schroeder, L. A. Swingle, ndi D. Sydlik. Lili pemphero lathu tonse kuti Yehova apitirize kudalitsa ndi kulimbikitsa Bungwe Lolamulira, lomwe tsopano lakuzidwa, pamene likupitiriza kuyang’anira ntchito ya anthu a Mulungu padziko lonse lapansi ndi kukwaniritsa zosoŵa zawo zauzimu.