Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Fufuzani Chuma Chimene ‘Chinabisidwa Mosamala mwa Iye’

Fufuzani Chuma Chimene ‘Chinabisidwa Mosamala mwa Iye’

Fufuzani Chuma Chimene ‘Chinabisidwa Mosamala mwa Iye’

“Mwa iye, chuma chonse cha nzeru ndi kudziwa zinthu chinabisidwa mosamala.”​—AKOL. 2:3.

1, 2. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zinapezeka mu 1922, ndipo kodi panopa zili kuti? (b) Kodi Mawu a Mulungu amalimbikitsa aliyense kuchita chiyani?

ANTHU ambiri amaona kuti kupeza chuma chobisika ndi nkhani yofunika kwambiri. Mwachitsanzo, mu 1922, katswiri wina wa mbiri ya zinthu zakale zokumbidwa pansi wa ku Britain, dzina lake Howard Carter, anafukula zinthu zochititsa chidwi kwambiri pambuyo pogwira ntchito ya kalavulagaga kwa zaka zambiri. Iye anafukula manda achifumu a Farao Tutankhamen ndipo mandawa anali ndi zinthu pafupifupi 5,000.

2 Zinthu zimene Carter anafukula zinali zochititsa chidwi kwambiri koma zambiri mwa izo zinangosungidwa m’nyumba zosungiramo zinthu zochititsa chidwi ndipo zina zinangosungidwa ndi anthu ena basi. Ngakhale kuti zinthu zimenezi ndi zothandiza kudziwa mbiri yakale ndiponso ndi zokongola, n’zosathandiza kwenikweni pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Koma Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kufufuza chuma chimene chingathandizedi tonsefe. Aliyense akulimbikitsidwa kufufuza chuma chimenechi ndipo phindu lake limaposa la chuma chilichonse chakuthupi.​—Werengani Miyambo 2:1-6.

3. Kodi chuma chimene Yehova akulimbikitsa anthu amene amamulambira kuchifufuza n’chothandiza motani?

3 Taganizirani phindu la chuma chimene Yehova akulimbikitsa anthu amene amamulambira kuti achifufuze. China mwa chuma chimenechi ndicho “kuopa Yehova,” kumene kungatiteteze m’masiku ovuta ano. (Sal. 19:9) “Kum’dziwadi Mulungu” kungathandize munthu kukhala pa ubwenzi ndi Wam’mwambamwamba ndipo ubwenzi umenewu ndi wofunika kuposa chilichonse chimene munthu angakhale nacho. Ndipo ngati tili ndi chuma chimene Mulungu amapereka monga nzeru, kudziwa ndi kuzindikira, tidzatha kupirira bwinobwino mavuto amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku. (Miy. 9:10, 11) Kodi tingatani kuti tipeze chuma chamtengo wapatali chimenechi?

Fufuzani Chuma Chauzimu

4. N’chiyani chingatithandize kupeza chuma chauzimu?

4 Akatswiri a mbiri ya zinthu zakale zokumbidwa pansi komanso anthu ena ofufuza zinthu zochititsa chidwi, amayendayenda uku ndi uku kuti apeze zomwe akufunazo. Koma ife timadziwa kumene tingapeze chuma chauzimu. Mawu a Mulungu ali ngati mapu ndipo amatisonyeza kumene tingapeze chuma chimene Mulungu walonjeza. Ponena za Khristu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Mwa iye, chuma chonse cha nzeru ndi kudziwa zinthu chinabisidwa mosamala.” (Akol. 2:3) Tikamawerenga mawu amenewa, mwina tingadzifunse kuti: ‘N’chifukwa chiyani tiyenera kufufuza chuma chimenechi? Kodi “chinabisidwa” bwanji mwa Khristu? Nanga tingachipeze bwanji?’ Kuti tipeze mayankho tiyeni tione bwinobwino mawu a mtumwi amenewa.

5. N’chifukwa chiyani Paulo analemba za chuma chauzimu?

5 Paulo analemba mawu amenewa m’kalata yake yopita kwa Akhristu anzake a ku Kolose. Iye anawauza kuti akuwamenyera nkhondo yaikulu n’cholinga choti “mitima yawo itonthozedwe, [komanso] kuti akhale olumikizana bwino m’chikondi.” (Werengani Akolose 2:1, 2.) N’chifukwa chiyani Paulo anali ndi maganizo amenewa? Zikuoneka kuti Paulo ankadziwa kuti abale akumeneku anakhudzidwa ndi zonena za anthu amene ankalimbikitsa nzeru za Agiriki komanso amene ankafuna kuti anthu azitsatirabe Chilamulo cha Mose. Iye anawachenjeza mwamphamvu abalewo kuti: “Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu, malinga ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli, osati malinga ndi Khristu.”​—Akol. 2:8.

6. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita chidwi ndi malangizo a Paulo?

6 Masiku ano, ifenso timakumana ndi zinthu ngati zimenezi kuchokera kwa Satana ndi dongosolo lake loipali. Nzeru za m’dzikoli, zomwe zikuphatikizapo kusakhulupirira kuti kuli Mulungu ndiponso chiphunzitso chakuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina, zimasokoneza kwambiri maganizo, makhalidwe, zolinga komanso moyo wa anthu. Maholide ambiri otchuka amene anthu amakondwerera amakhala okhudzana ndi chipembedzo chonyenga. Mapulogalamu a pa TV, masewero komanso nyimbo zambiri zimalimbikitsa zilakolako zoipa ndipo zinthu zambiri zimene zimapezeka pa Intaneti zingawononge kwambiri ana ndi akulu omwe. Kuonera kapena kumvera zinthu zimenezi nthawi ndi nthawi kungasokoneze kwambiri maganizo athu. Kungasinthenso mmene timaonera malangizo amene Yehova amatipatsa moti tingayambe kusiya kugwira zolimba moyo weniweniwo. (Werengani 1 Timoteyo 6:17-19.) M’pake kuti tiyenera kumvetsa tanthauzo la mawu amene Paulo anauza Akolose n’kusunga mumtima malangizo ake. Izi zidzatithandiza kuti tisakopeke ndi misampha ya Satana.

7. Kodi ndi zinthu ziwiri ziti zimene Paulo ananena kuti zikanathandiza Akolose?

7 Tikaonanso mawu a Paulo kwa Akolose, tidzapeza kuti iye atafotokoza zimene zinkamudetsa nkhawa, anatchulanso zinthu ziwiri zimene zikanawathandiza kuti atonthozedwe komanso kuti akhale olumikizana bwino m’chikondi. Choyamba, iye ananena za “kumvetsa zinthu motsimikiza.” Iwo anafunika kutsimikizira kuti akumvetsa Malemba n’cholinga choti chikhulupiriro chawo chikhale ndi maziko olimba. (Aheb. 11:1) Kenako ananenanso za ‘kudziwa molondola chinsinsi chopatulika cha Mulungu.’ Iwo sanafunike kungodziwa mfundo zoyambirira za choonadi koma anafunikanso kumvetsa bwino zinthu zozama za Mulungu. (Aheb. 5:13, 14) Malangizo amenewatu anali ofunika kwambiri kwa Akolose komanso ndi ofunika kwa ifeyo. Ndiyeno kodi tingatani kuti tikhale otsimikiza komanso kuti tidziwe zinthu molondola? Mfundo yofunika kwambiri yokhudza Yesu Khristu imene Paulo anatchula, imayankha funso limeneli. Iye anati: “Mwa iye, chuma chonse cha nzeru ndi kudziwa zinthu chinabisidwa mosamala.”

Chuma Chimene “Chinabisidwa” mwa Khristu

8. Kodi mawu akuti “chinabisidwa” mwa Khristu amatanthauza chiyani?

8 Mawu akuti chuma chonse cha nzeru ndi kudziwa zinthu “chinabisidwa” mwa Khristu, sakutanthauza kuti chumacho chinatsekeredwa mwa iye moti palibe angachipeze. Mawuwa amatanthauza kuti tifunika kuchita khama kwambiri kuti tipeze chumacho ndipo chidwi chathu chonse chiyenera kukhala pa Yesu Khristu. Izi zikugwirizana ndi mawu amene Yesu ananena pofotokoza za iye mwini. Iye anati: “Ine ndine njira ndi choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yoh. 14:6) Kuti tidziwe bwino Mulungu, tiyenera kulandira thandizo komanso malangizo amene Yesu akutipatsa.

9. Tchulani udindo umene Yesu wapatsidwa.

9 Kuwonjezera pa kukhala “njira,” Yesu anati iye ndi “choonadi ndi moyo.” Izi zikusonyeza kuti iye alinso ndi udindo wina kuwonjezera pa kutithandiza kuti tizitha kufikira Atate. Yesu alinso ndi udindo wotithandiza kuti timvetse bwino choonadi cha m’Baibulo komanso kuti tipeze moyo wosatha. Apatu zikuonekeratu kuti chuma chauzimu chamtengo wapatali kwambiri chinabisidwadi mwa Yesu ndipo anthu amene amaphunzira Baibulo mwakhama, ndi amene angachipeze. Tsopano tiyeni tione chuma chimene chimakhudza chiyembekezo chathu komanso ubwenzi wathu ndi Mulungu.

10. Kodi Akolose 1:19 ndi 2:9, akutiphunzitsa chiyani za Yesu?

10 “Kudzala konse kwa umulungu kumakhala mwa Khristuyo.” (Akol. 1:19; 2:9) Popeza anakhala ndi Atate wake wakumwamba kwa zaka zankhaninkhani, Yesu amadziwa bwino makhalidwe ndi cholinga cha Mulungu kuposa wina aliyense. Pa nthawi yonse ya utumiki wake padziko lapansi, Yesu anaphunzitsa anthu zinthu zimene Atate wake anamuphunzitsa ndipo ankasonyeza makhalidwe amene iye anatengera kwa Atate wake. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9) Nzeru zonse ndi kudziwa Mulungu zinabisidwa kapena kuti zili mwa Khristu. Choncho tiyenera kuchita khama kuti tim’dziwe bwino Yesu ndipo iyi ndi njira yokhayo imene tingaphunzirire za Yehova.

11. Fotokozani mgwirizano umene ulipo pakati pa Yesu ndi maulosi a m’Baibulo.

11 “Kuchitira umboni za Yesu ndiko cholinga cha kunenera.” (Chiv. 19:10) Mawu amenewa akusonyeza kuti kukwaniritsidwa kwa maulosi ambiri a m’Baibulo kumadalira Yesu. Munthu angamvetse maulosi onse a m’Baibulo, kuchokera pa ulosi woyamba umene Yehova ananena pa Genesis 3:15 mpaka masomphenya aulemerero a m’buku la Chivumbulutso, kokha ngati atazindikira udindo umene Yesu ali nawo wokhudza Ufumu wa Mesiya. N’chifukwa chake anthu ambiri amene savomereza zoti Yesu ndi Mesiya wolonjezedwa, samvetsa maulosi ambiri a m’Malemba a Chiheberi. N’chifukwa chakenso anthu amene salemekeza Malemba a Chiheberi, amene ali ndi maulosi ambiri onena za Mesiya, amangoona kuti Yesu ndi munthu wamba basi. Kum’dziwa bwino Yesu, kumathandiza anthu a Mulungu kuti amvetse matanthauzo a maulosi a m’Baibulo amene adzakwaniritsidwe m’tsogolo.​—2 Akor. 1:20.

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani Yesu ndi “kuwala kwa dziko”? (b) Popeza Akhristu amasulidwa ku mdima wa chipembedzo, kodi ayenera kuchita chiyani?

12 “Ine ndine kuwala kwa dziko.” (Werengani Yohane 8:12; 9:5.) Yesu asanabadwe padzikoli, mneneri Yesaya analosera kuti: “Anthu amene anayenda mumdima, aona kuwala kwakukulu; iwo amene anakhala m’dziko la mthunzi wa imfa, kuwala kwatulukira kwa iwo.” (Yes. 9:2) Mtumwi Mateyo anafotokoza kuti Yesu anakwaniritsa ulosi umenewu pamene anayamba kulalikira kuti: “Lapani, anthu inu, pakuti ufumu wa kumwamba wayandikira.” (Mat. 4:16, 17) Utumiki wa Yesu unathandiza kuti anthu aone kuwala kwauzimu komanso kuti amasuke ku ziphunzitso za chipembedzo chonyenga. Yesu ananena kuti: “Ndabwera monga kuwala m’dziko, kuti aliyense wokhulupirira ine asakhalebe mu mdima.”​—Yoh. 1:3-5; 12:46.

13 Patapita zaka zambiri, mtumwi Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Poyamba munali mdima, koma tsopano ndinu kuwala mogwirizana ndi Ambuye. Yendanibe ngati ana a kuwala.” (Aef. 5:8) Popeza Akhristu amasulidwa ku mdima wa chipembedzo, iwo ayenera kuyenda monga ana a kuwala. Izi n’zogwirizana ndi zimene Yesu anauza otsatira ake pa ulaliki wapaphiri. Iye anati: “Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wa kumwamba.” (Mat. 5:16) Kodi mumayamikira kwambiri chuma chauzimu chimene mwachipeza mwa Yesu moti mumasonyeza ena ubwino wa chumacho kudzera m’mawu anu komanso khalidwe lanu labwino lachikhristu?

14, 15. (a) Kodi nkhosa ndiponso nyama zina, zinkagwiritsidwa ntchito motani pa kulambira koona m’nthawi za m’Baibulo? (b) N’chifukwa chiyani Yesu ndi chuma choposa chuma china chilichonse pa udindo wake monga “Mwanawankhosa wa Mulungu”?

14 Yesu ndi “Mwanawankhosa wa Mulungu.” (Yoh. 1:29, 36) Baibulo lonse limasonyeza kuti nkhosa zinkathandiza kwambiri kuti munthu akhululukidwe machimo komanso kuti amufikire Mulungu. Mwachitsanzo, Abulahamu atasonyeza kuti anali wokonzeka kupereka nsembe mwana wake Isake, iye anauzidwa kuti asaphe mwana wakeyo. M’malomwake anapatsidwa nkhosa yamphongo kuti aipereke nsembe. (Gen. 22:12, 13) Pa nthawi imene Aisiraeli ankapulumutsidwa ku Iguputo, anagwiritsanso ntchito nkhosa pochita ‘pasika wa Yehova.’ (Eks. 12:1-13) Nachonso Chilamulo cha Mose chinauza Aisiraeli kuti azipereka nsembe za nyama zosiyanasiyana, kuphatikizapo nkhosa ndi mbuzi.​—Eks. 29:38-42; Lev. 5:6, 7.

15 Ngakhale zinali choncho, nsembe za nyamazo, komanso zilizonse zimene anthu akanapereka, sizikanatha kuwamasuliratu ku uchimo ndi imfa. (Aheb. 10:1-4) Koma Yesu ndiye “Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko.” Chifukwa cha mfundo yokhayi, Yesu ndi chuma choposa chuma china chilichonse chimene anthu achipeza. Motero ndi bwino kuphunzira mosamala nkhani ya dipo komanso kukhulupirira dipolo chifukwa ndi mphatso yamtengo wapatali. Tikatero, tidzalandira madalitso osaneneka. Kwa “kagulu ka nkhosa,” madalitso amenewa akutanthauza kukhala ndi Khristu mu ulemerero wakumwamba koma a “nkhosa zina” adzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi.​—Luka 12:32; Yoh. 6:40, 47; 10:16.

16, 17. N’chifukwa chiyani tifunika kumvetsa udindo wa Yesu monga “Mtumiki Wamkulu ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu”?

16 Yesu ndi “Mtumiki Wamkulu ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu.” (Werengani Aheberi 12:1, 2.) M’chaputala 11 cha buku la Aheberi, Paulo anafotokoza bwino za chikhulupiriro. Iye ananena tanthauzo la chikhulupiriro ndipo anatchula anthu amene anasonyeza chikhulupiriro monga Nowa, Abulahamu, Sara, Rahabi ndi ena. Poganizira zonsezi, Paulo analimbikitsa Akhristu anzake “kuyang’anitsitsa Mtumiki Wamkulu ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu, Yesu.” N’chifukwa chiyani anatero?

17 Ngakhale kuti amuna ndi akazi amene atchulidwa m’chaputala 11 cha buku la Aheberi ankakhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu, iwo sankadziwa tsatanetsatane wa mmene Mulungu adzakwaniritsire malonjezo ake kudzera mwa Mesiya ndi Ufumu wake. Motero tingati chikhulupiriro chawo chinali chosakwanira. Ndipotu ngakhale anthu amene anauziridwa ndi Yehova kulemba maulosi ambiri okhudza Mesiya, sankadziwa bwinobwino tanthauzo la zimene analembazo. (1 Pet. 1:10-12) Motero chikhulupiriro chingakhale chokwanira kokha kudzera mwa Yesu. Izi zikungosonyezeratu kuti kumvetsa ndi kuzindikira udindo wa Yesu monga “Mtumiki Wamkulu ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu,” n’kofunika kwambiri.

Funafunanibe

18, 19. (a) Tchulani chuma china chauzimu chobisidwa mwa Khristu. (b) Kuti tipeze chuma chauzimu, n’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kuyang’ana kwa Yesu?

18 Zimene takambiranazi ndi zinthu zochepa chabe zokhudza udindo wapadera umene Yesu ali nawo pokwaniritsa cholinga cha Mulungu chopulumutsa anthu. Palinso chuma chauzimu china chobisidwa mwa Khristu. Tikachipeza, timakhala osangalala komanso timapindula. Mwachitsanzo, mtumwi Petulo ananena kuti Yesu ndi “Mtumiki Wamkulu wa moyo” ndiponso “nthanda” imene ituluka. (Mac. 3:15; 5:31; 2 Pet. 1:19) Baibulo limagwiritsanso ntchito mawu oti “Amen” ponena za Yesu. (Chiv. 3:14) Kodi mukudziwa tanthauzo ndiponso kufunika kwa maudindo amenewa? Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, “funafunanibe, ndipo mudzapeza.”​—Mat. 7:7.

19 Kuyambira kale, palibe munthu amene moyo wake ndi wofunika kwambiri kwa ife komanso umakhudza tsogolo lathu mofanana ndi moyo wa Yesu. Mwa iye muli chuma chauzimu chomwe aliyense akhoza kuchipeza ngati atachifufuza ndi mtima wonse. Motero muzisangalala ndi kufufuza chuma chimene “chinabisidwa mosamala” mwa iye, ndipo mukatero, mudzadalitsidwa.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi Akhristu akulimbikitsidwa kufufuza chuma chiti?

• N’chifukwa chiyani malangizo a Paulo kwa Akolose ali ofunika kwa ife?

• Tchulani ndiponso fotokozani chuma chauzimu chimene “chinabisidwa” mwa Khristu.

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 5]

Baibulo lili ngati mapu otithandiza kupeza chuma chimene “chinabisidwa mosamala” mwa Khristu