“Mzimu ndi Mkwatibwi Akunenabe Kuti: ‘Bwera!’”
“Mzimu ndi Mkwatibwi Akunenabe Kuti: ‘Bwera!’”
“Mzimu ndi mkwatibwi akunenabe kuti: “Bwera!” . . . Aliyense wakumva ludzu abwere. Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere.”—CHIV. 22:17.
1, 2. Kodi zinthu za Ufumu tiyenera kuziona motani pamoyo wathu, ndipo n’chifukwa chiyani?
KODI zinthu za Ufumu tiyenera kuziona motani pa moyo wathu? Yesu anauza otsatira ake kuti ‘apitirize kufuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo anawatsimikizira kuti ngati atachita zimenezi, Mulungu adzawapatsa zimene akufunikira. (Mat. 6:25-33) Iye anayerekezera Ufumu wa Mulungu ndi ngale ya mtengo wapatali imene wamalonda wina woyendayenda ataipeza, anapita ‘kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo ndi kugula ngaleyo.’ (Mat. 13:45, 46) Ifenso tiyenera kuona ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira kuti ndi yofunika kwambiri.
2 Monga tinaonera mu nkhani yoyamba ndi yachiwiri ija, tikamalankhula molimba mtima ndiponso kugwiritsa ntchito mwaluso Mawu a Mulungu mu utumiki, zimasonyeza kuti mzimu wa Mulungu ukutitsogolera. Mzimu umenewu umatithandizanso kwambiri kuti tizigwira nawo ntchito yolalikira Ufumu nthawi zonse. Tiyeni tione mmene umachitira zimenezi.
Anthu Onse Akuitanidwa
3. Kodi ndi madzi otani amene anthu onse akuitanidwa kuti ‘abwere’ kudzamwa?
3 Anthu onse akuitanidwa kudzera mwa mzimu woyera. (Werengani Chivumbulutso 22:17.) Cholinga cha kuitanaku n’choti anthu ‘abwere’ kudzapha ludzu ndi madzi apadera kwambiri. Amenewa si madzi enieni amene timamwa nthawi zonse ayi. Ngakhale kuti madzi enieni ndi ofunika kuti padzikoli pakhale zamoyo, Yesu sankanena madzi amenewa pamene anauza mkazi wachisamariya uja pachitsime kuti: “Amene adzamwa madzi amene ine ndidzam’patse sadzamvanso ludzu mpang’ono pomwe, ndipo madzi amene ndidzam’patse, adzasanduka kasupe wa madzi otumphuka mwa iye opatsa moyo wosatha.” (Yoh. 4:14) Madzi apadera amenewa, amene anthu onse akuitanidwa kuti adzamwe, amapatsa moyo wosatha.
4. N’chiyani chinachititsa kuti madzi amoyo akhale ofunika, ndipo kodi madzi amenewa amaimira chiyani?
4 Madzi amoyo amenewa anayamba kufunika pamene Adamu, munthu woyamba kulengedwa, limodzi ndi mkazi wake Hava sanamvere Yehova Mulungu amene anawalenga. (Gen. 2:16, 17; 3:1-6) Anthu awiri oyambirirawa anathamangitsidwa m’munda umene ankakhala “kuti [Adamu] asatambasule dzanja lake ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthawi zonse.” (Gen. 3:22) Popeza Adamu ndi kholo la anthu onse, zochita zake zinapangitsa kuti anthu onse azifa. (Aroma 5:12) Madzi amoyo amaimira zinthu zonse zimene Mulungu wapereka pofuna kuthandiza anthu omvera kumasuka ku uchimo ndi imfa ndiponso kuwapatsa moyo wangwiro ndi wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. Zinthu zimenezi zikutheka chifukwa cha nsembe ya dipo ya Yesu Khristu.—Mat. 20:28; Yoh. 3:16; 1 Yoh. 4:9, 10.
5. Kodi ndani kwenikweni amene akuitana anthu kuti abwere ‘adzamwe madzi a moyo kwaulere’? Fotokozani.
5 Kodi ndani kwenikweni akuitana anthu kuti abwere ‘adzamwe madzi a moyo kwaulere’? Zinthu zonse zokhudza moyo zimene Mulungu wapereka kudzera mwa Yesu zikadzakwaniritsidwa pa anthu mu Ulamuliro wa Khristu wa zaka 1,000, Baibulo limati zinthuzi zidzakhala ngati “mtsinje wa madzi a moyo, oyera ngati kulusitalo.” Mtsinje umenewu “ukuyenda kuchokera ku mpando wachifumu wa Mulungu, ndi wa Mwanawankhosa.” (Chiv. 22:1) Choncho, Yehova yemwe ndi Wopatsa moyo ndi amene akupereka madzi a moyowa. (Sal. 36:9) Iye akupereka madzi amenewa kudzera mwa Yesu Khristu yemwe ndi “Mwanawankhosa.” (Yoh. 1:29) Mtsinje wophiphiritsa umenewu ndi njira imene Yehova akugwiritsa ntchito kuchotsa mavuto onse a anthu amene anayamba chifukwa cha kusamvera kwa Adamu. Ndithudi, Yehova Mulungu ndi amene kwenikweni akuitana anthu kuti ‘abwere.’
6. Kodi “mtsinje wa madzi a moyo” unayamba kuyenda liti?
6 Ngakhale kuti “mtsinje wa madzi a moyo” udzayenda mokwanira mu Ulamuliro wa Khristu wa zaka 1,000, mtsinjewu unayamba kuyenda “m’tsiku la Ambuye” limene linayamba mu 1914 pamene “Mwanawankhosa” anakhala mfumu. (Chiv. 1:10) Choncho, zimenezi zitachitika anthu anayamba kulandira zinthu zopatsa moyo, kuphatikizapo uthenga wa m’Baibulo womwe umatchedwanso kuti “madzi.” (Aef. 5:26) Anthu onse akuitanidwa kuti ‘adzamwe madzi a moyo’ mwa kumvetsera Uthenga wabwino wa Ufumu ndi kutsatira zimene Uthengawo ukunena. Koma kodi ndani akugwira ntchito yoitana anthu m’tsiku la Ambuye?
“Mkwatibwi” Akunena Kuti, “Bwera!”
7. “M’tsiku la Ambuye,” kodi ndani oyambirira kugwira ntchito yoitana anthu kuti ‘abwere,’ ndipo akuitana anthu ake ati?
7 Anthu amene ali m’gulu la mkwatibwi, omwe ndi Akhristu odzozedwa, ndiye oyambirira kugwira ntchito yoitana anthu kuti ‘abwere.’ Kodi anthu ake ndani? Apa Akhristu odzozedwawa sakuitana anthu a m’gulu lawo lomweli. Iwo akuitana anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi, “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” ikadzatha.—Werengani Chivumbulutso 16:14, 16.
8. N’chiyani chikusonyeza kuti kuyambira kale m’chaka cha 1918, Akhristu odzozedwa akhala akugwira ntchito yoitana anthu imene Yehova anayambitsa?
8 Otsatira Khristu odzozedwa akhala akugwira ntchito yoitana anthu kuyambira kale mu chaka cha 1918. M’chaka chimenechi, nkhani ya onse yakuti, “Anthu Mamiliyoni Ambiri Amene Ali ndi Moyo Sadzafa,” inathandiza anthu kukhala ndi chiyembekezo chakuti ambiri adzakhala ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi nkhondo ya Armagedo ikadzatha. Nkhani ina imene inakambidwa pa msonkhano wa Ophunzira Baibulo umene unachitika ku Cedar Point, Ohio, ku America, mu chaka cha 1922, inalimbikitsa omvera kuti ‘alengeze za Mfumu ndi ufumu wake.’ Zimenezi zinathandiza otsalira a m’gulu Chivumbulutso 22:17. Mwa zina nkhaniyi inati: “Nawonso otsalira odzozedwa okhulupirika anayamba kugwira ntchito imeneyi yoitana anthu kuti ‘abwere’ ndipo akuigwira limodzi ndi [Wam’mwambamwamba]. Uthenga umenewu uyenera kulengezedwa kwa anthu amene akufuna chilungamo ndi choonadi. Ndipo zimenezi ziyenera kuchitika panopa.” Gulu la mkwatibwi limeneli likupitirizabe kuitana anthu mpaka pano.
la mkwatibwi kuti ayesetse kuitana anthu ambiri. Mu chaka cha 1929, Nsanja ya Olonda yachingelezi ya March 15, inali ndi nkhani yakuti, “Kuitana Anthu Chifukwa Chokoma Mtima,” ndipo lemba lotsogolera nkhaniyi linali“Aliyense Wakumva Anene Kuti: ‘Bwera!’”
9, 10. Kodi anthu amene amva kuitana kuti, “Bwera!” nawonso akupemphedwa kuchita chiyani?
9 Kodi anthu amene amva kuitana kuti ‘abwere,’ ayenera kuchita chiyani? Nawonso ayenera kunena kuti, “Bwera!” Mwachitsanzo, Nsanja ya Olonda ya August 1, 1932, patsamba 232, inanena kuti: “Odzozedwa ayenera kulimbikitsa anthu onse amene adzagwira nawo ntchito youza ena uthenga wabwino wa Ufumu. Sikuti n’zochita kulira kuti munthu akhale wodzozedwa wa Ambuye kuti azilengeza uthengawu. N’zolimbikitsa kwambiri kwa mboni za Yehova kudziwa kuti iwonso ndi ovomerezedwa kugawira madzi amoyo kwa anthu amene angadzapulumuke pa Armagedo ndi kukhala ndi moyo wosatha padziko lapansi pano.”
10 Posonyeza udindo woitana anthu kuti ‘abwere,’ umene anthu amene aitanidwa ali nawo, Nsanja ya Olonda ya August 15, 1934, patsamba 249, inati: “A gulu la Yonadabu ayenera kupitira limodzi ndi a kagulu ka Yehu kophiphiritsa, komwe ndi odzozedwa, kulengeza uthenga wa ufumu, ngakhale kuti sali mboni zodzozedwa za Yehova.” Mu 1935, “khamu lalikulu” lotchulidwa pa Chivumbulutso 7:9-17, linadziwika bwinobwino. Zimenezi zinathandiza kwambiri kuti ntchito ya Mulungu yoitanira anthu ipite patsogolo kwambiri. Kuyambira nthawi imeneyo, anthu ambiri a khamu lalikulu la olambira oona, omwe masiku ano ndi oposa 7 miliyoni ayankha kuitana kumeneku. Atamvetsera ndi kukhutira ndi uthenga umenewu, adzipereka kwa Mulungu ndi kubatizidwa m’madzi ndipo iwonso ayamba kuitana anthu ena kuti ‘adzamwe madzi amoyo kwaulere.’ Iwo akugwira ntchito imeneyi limodzi ndi a m’gulu la mkwatibwi.
“Mzimu” Ukunena Kuti, “Bwera!”
11. M’nthawi ya atumwi, kodi mzimu woyera unathandiza bwanji pa ntchito yolalikira?
11 Pamene Yesu ankalalikira m’sunagoge ku Nazareti, iye anafunyulula mpukutu wa mneneri Yesaya n’kuwerenga kuti: “Mzimu wa Yehova uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi za kuchiritsidwa kwa akhungu. Inde, kudzamasula oponderezedwa kuti apite monga mfulu, kudzalalikira chaka chokomera Yehova.” Kenako Yesu anasonyeza kuti mawuwo akunena za iyeyo pamene anati: “Lero lemba ili limene mwangolimva kumeneli lakwaniritsidwa.” (Luka 4:17-21) Iye asanabwerere kumwamba anauza ophunzira ake kuti: “Mudzalandira mphamvu pamene mzimu woyera udzafika pa inu. Pamenepo mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) M’nthawi ya atumwi, mzimu woyera unathandiza kwambiri pa ntchito yolalikira.
12. Kodi masiku ano mzimu wa Mulungu umatithandiza bwanji pa ntchito yoitana anthu?
12 Kodi masiku ano mzimu woyera wa Mulungu umathandiza bwanji pa ntchito yoitana anthu? Yehova ndi amene amapereka mzimu woyera. Iye amagwiritsa ntchito mzimuwu kuthandiza kagulu ka mkwatibwi kumvetsa Baibulo, lomwe ndi Mawu ake. Mzimuwu umawathandizanso kugwira ntchito yoitana anthu ndi kufotokozera Malemba kwa anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. Nanga bwanji anthu amene avomera ataitanidwa, kukhala ophunzira a Yesu Khristu, kenaka n’kuyamba kuitananso anthu ena? Iwonso mzimuwu umawathandiza. Popeza amabatizidwa ‘m’dzina la mzimu woyera,’ iwo amachita zinthu mogwirizana ndi mzimu woyera ndipo amadalira mzimuwu kuti uziwathandiza. (Mat. 28:19) Nanga bwanji za uthenga umene umalalikidwa ndi odzozedwa ndiponso khamu lalikulu limene likuwonjezerekabe? Uthengawu umachokera m’Baibulo, lomwe mzimu wa Mulungu unatsogolera kuti lilembedwe. Choncho, ntchito yoitana anthu imeneyi ikuchitika chifukwa cha mzimu woyera. Ndipotu, mzimu umenewu ndi umene ukutitsogolera. Kodi si zoona kuti zimenezi zikusonyeza kuti tiyenera kuthera nthawi yochuluka pa ntchito yoitana anthu?
Iwo “Akunenabe Kuti: ‘Bwera!’”
13. Kodi mawu akuti “Mzimu ndi mkwatibwi akunenabe kuti: ‘Bwera!’” akusonyeza chiyani?
13 “Mzimu ndi mkwatibwi” sananene kamodzi kokha kuti “Bwera!” Mawu a Chigiriki amene anagwiritsa ntchito pomasulira mawu amenewa amatanthauza kuchita zinthu mosalekeza. Poganizira mfundo imeneyi, Baibulo la Dziko Latsopano limati: “Mzimu ndi mkwatibwi akunenabe kuti: ‘Bwera!’” Zimenezi zikusonyeza kuti ntchito yoitana anthu iyenera kumachitika nthawi zonse. Kodi anthu amene amamva kuitanaku kenako n’kubweradi, amayenera kuchita chiyani? Iwonso amanena kuti, “Bwera!” Baibulo limanena kuti olambira oona a khamu lalikulu “akum’chitira [Yehova] utumiki wopatulika usana ndi usiku m’kachisi wake.” (Chiv. 7:9, 15) Kodi akutanthauza chiyani ponena kuti ‘akum’tumikira usana ndi usiku’? (Werengani Luka 2:36, 37; Machitidwe 20:31; 2 Atesalonika 3:8.) Zimene mtumwi Paulo ndiponso mneneri wamkazi dzina lake Anna, yemwe anali wokalamba ankachita, zikusonyeza kuti ‘kutumikira usana ndi usiku’ kumatanthauza kutumikira nthawi zonse komanso mwa khama.
14, 15. Kodi Danieli anachita chiyani chosonyeza kuti m’pofunika kulambira Mulungu mosalekeza?
14 Mneneri Danieli nayenso anasonyeza kuti m’pofunika kulambira Mulungu nthawi zonse. (Werengani Danieli 6:4-10, 16.) Iye sanasinthe chizolowezi chake chopemphera kwa Mulungu “tsiku limodzi katatu, . . . monga umo amachitira kale lonse.” Ndipo iye sakanalola kusintha chizolowezi chakechi ngakhale kwa mwezi umodzi wokha, ngakhale kuti chilango chochita zimenezo chinali kuponyedwa m’dzenje la mikango. Zimene anachitazi zinasonyezeratu kwa anthu onse kuti panalibe chimene chinali chofunika kwambiri kwa iye, kuposa kulambira Yehova nthawi zonse.—Mat. 5:16.
15 Danieli atakhala m’dzenje la mikango usiku wonse, mfumu inapita komweko, ndipo inafuula kuti: “Danieli, mnyamata wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako, amene um’tumikira kosalekeza, wakhoza kukulanditsa kwa mikango?” Nthawi yomweyo Danieli anayankha kuti: “Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire. Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, chifukwa anandiona wosachimwa pamaso pake, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwa.” Yehova anam’dalitsa Danieli chifukwa chakuti ankam’tumikira ‘mosalekeza.’—Dan. 6:19-22.
16. Kodi chitsanzo cha Danieli chikutipangitsa kufunsa mafunso otani pa nkhani yokhudza mmene timachitira utumiki?
16 Danieli analolera kufa m’malo moti asiye chizolowezi chake cha kulambira Mulungu mosalekeza. Nanga ifeyo timatani? Kodi mungalolere kudzimana chiyani kuti muzilengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu mosalekeza? Ndithudi, sitiyenera kulola ngakhale mwezi umodzi kudutsa popanda kuuza ena za Yehova. Ngati n’kotheka, tiyenera kumayesetsa kulalikira nawo mlungu uliwonse. Ngakhale titakhala kuti sitingachite zambiri chifukwa cha thanzi lathu ndipo tingangokwanitsa kulalikira mphindi 15 zokha pa mwezi, tiyenera kuperekabe lipoti. Tiyenera kuchita zimenezi chifukwa ifenso tikufuna kugwirizana ndi mzimu ndi mkwatibwi ponenabe kuti, “Bwera!” Inde, tifunika kuchita zonse zimene tingathe kuti tikhalebe ofalitsa Ufumu okhazikika.
17. Kodi ndi nthawi ina iti imene tingagwire nawo ntchito ya Yehova yoitana anthu?
17 Tiyenera kuyesetsa kugwira nawo ntchito ya Yehova yoitana anthu nthawi iliyonse imene tapeza mpata, osati chabe pa nthawi imene tinakonza yoti tizilowa mu utumiki. Tikamakagula zinthu, tikakhala paulendo, kutchuthi, kuntchito, kapena kusukulu, tingakhale ndi mwayi wapadera kwambiri kugwira nawo ntchito yoitana anthu aludzu kuti ‘abwere adzamwe madzi amoyo kwaulere.’ Ngakhale akuluakulu aboma ataletsa ntchito yolalikira, timapitirizabe kulalikira koma mosamala. Timachita zimenezi mwina mwa kuchepetsa kulalikira khomo ndi khomo m’dera limene timakhala kapena kuwonjezera mipata yolalikira mwamwayi.
Pitirizanibe Kunena Kuti, “Bwera!”
18, 19. Kodi mumachita chiyani kuti musonyeze kuti mwayi wokhala antchito anzake a Mulungu mumauona kuti ndi wofunika kwambiri?
18 Kwa zaka zoposa 90 tsopano, mzimu ndi mkwatibwi akhala akunena kuti, “Bwera!” kwa aliyense yemwe ali ndi ludzu kuti adzamwe madzi a moyo. Kodi mwamva kuitana kwawo kosangalatsaku? Ngati zili choncho, inunso mukupemphedwa kuitana anthu ena kuti abwere.
19 Sitikudziwa kuti ntchito ya Yehova yoitana anthu igwiridwa kwa nthawi yaitali bwanji, koma tikamagwira nawo ntchito imeneyi mwa kunena kuti, “Bwera!” timakhala “antchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:6, 9) Uwutu ndi mwayi wapadera kwambiri. Tiyeni zochita zathu zizisonyeza kuti timaona mwayi umenewu kukhala wofunika kwambiri ndipo “nthawi zonse tipereke kwa Mulungu nsembe ya chitamando” mwa kugwira nawo ntchito yolalikira nthawi zonse. (Aheb. 13:15) Ife tonse amene tili ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo padziko lapansi, tiyeni tipitirize kunena kuti, “Bwera!” ndipo tizichita zimenezi limodzi ndi a m’gulu la mkwatibwi. Ndipo tikulakalaka kuti anthu ambiri abwere ‘adzamwe madzi a moyo kwaulere.’
Kodi Mwaphunzira Chiyani?
• Kodi ndani akuitanidwa kuti ‘abwere’?
• N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi amene anayambitsa ntchito yoitana anthu kuti ‘abwere’?
• Kodi mzimu woyera umathandiza bwanji pa ntchito yoitana anthu kuti ‘abwere’?
• N’chifukwa chiyani tifunika kuyesetsa kuti tizilalikira nthawi zonse?
[Mafunso]
[Tchati/Chithunzi patsamba 16]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Pitirizanibe Kunena Kuti, “Bwera!”
1914
Ofalitsa 5,100
1918
Anthu ambiri adzakhala ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi
1922
“Lengezani, lengezani, lengezani, Mfumu ndi ufumu wake”
1929
Otsalira odzozedwa okhulupirika akunena kuti, “Bwera!”
1932
Anthu enanso osati odzozedwa okha, akugwira nawo ntchito yoitana anthu kuti, ‘abwere’
1934
A gulu la Yehonadabu akupemphedwa kulalikira nawo
1935
“Khamu lalikulu” ladziwika
2009
Ofalitsa okwana 7,313,173