Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukutsatira Khristu ndi Mtima Wonse?

Kodi Mukutsatira Khristu ndi Mtima Wonse?

Kodi Mukutsatira Khristu ndi Mtima Wonse?

“Momwedi mukuyendera, pitirizani kutero mowonjezereka.”​—1 ATES. 4:1.

1, 2. (a) Kodi anthu ambiri a m’nthawi ya Yesu anaona zinthu zapadera zotani? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti nthawi yathu ino ndi yapaderanso?

KODI munayamba mwaganiza mmene zikanakhalira zosangalatsa kukhala ndi moyo panthawi imene Yesu anali padziko lapansi? Mungamaganizire Yesu atakuchiritsani ndipo mulibenso nkhawa yakuti mukudwala matenda osautsa. Kapena mungalakelake kuphunzitsidwa ndi Yesu ndiponso kumuona akuchita zozizwitsa. (Maliko 4:1, 2; Luka 5:3-9; 9:11) Ukanakhala mwayi wapadera kwambiri kukhala ndi moyo pa nthawi imene Yesu ankachita zozizwitsa zimenezi. (Luka 19:37) Kuchokera nthawi imeneyo, palibenso anthu amene aonapo zinthu ngati zimenezo ndipo zimene Yesu anakwaniritsa padziko lapansi “kudzera mu nsembe ya iye mwini” sizidzachitidwanso.​—Aheb. 9:26; Yoh. 14:19.

2 Komabe, nthawi yathu ino ndi yapaderanso. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa tikukhala m’nthawi imene Malemba amati ndi “nthawi ya chimaliziro” ndiponso “masiku otsiriza.” (Dan. 12:1-4, 9; 2 Tim. 3:1) M’nthawi imeneyi Satana anachotsedwa kumwamba. Posachedwapa, adzamangidwa ndi kuponyedwa “m’phompho.” (Chiv. 12:7-9, 12; 20:1-3) Pa nthawi imeneyi tilinso ndi mwayi waukulu wolengeza ‘uthenga wabwino wa ufumu’ padziko lonse, kuwauza anthu za Paradaiso amene tikuyembekezera. Ntchito imeneyi sidzachitikanso.​—Mat. 24:14.

3. Atangotsala pang’ono kupita kumwamba, kodi Yesu anauza ophunzira ake kugwira ntchito iti, ndipo kodi ntchito imeneyi inali yoti idzaphatikizapo chiyani?

3 Atangotsala pang’ono kupita kumwamba, Yesu anauza otsatira ake kuti: “Mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Ntchito imeneyi inali yoti idzaphatikizapo kuphunzitsa anthu padziko lonse. Kodi cholinga cha ntchitoyi n’chiyani? Cholinga chake ndi kuphunzitsa anthu kuti akhale otsatira a Khristu mapeto asanafike. (Mat. 28:19, 20) Kodi tingatani kuti tikwaniritse bwinobwino lamulo la Khristu limeneli?

4. (a) Kodi malangizo a Petulo opezeka pa 2 Petulo 3:11, 12 akutsindika mfundo iti? (b) Kodi tiyenera kusamala kwambiri ndi zinthu ziti?

4 Taonani malangizo a mtumwi Petulo awa: “Lingalirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala pa khalidwe loyera ndi pa ntchito za kudzipereka kwanu kwa Mulungu. Teroni poyembekezera ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.” (2 Pet. 3:11, 12) Mawu a Petulo amenewa akutsindika mfundo yakuti tiyenera kukhala maso m’masiku otsiriza ano n’kumaonetsetsa kuti ntchito za kudzipereka kwa Mulungu zikukhala pamalo oyamba pa moyo wathu. Ntchito zimenezi zikuphatikizapo kulalikira uthenga wabwino. Ndiyetu n’zosangalatsa kwambiri kuona kuti abale athu padziko lonse lapansi akugwira mwachangu ntchito yolalikira potsatira lamulo la Khristu. Komanso timadziwa kuti tifunika kusamala kwambiri kuti mavuto amene dziko la Satanali limatibweretsera ndiponso chibadwa chathu chokonda zinthu zakuthupi, zisatichititse kuchepetsa changu chathu potumikira Mulungu. Tiyeni tikambirane zimene tiyenera kuchita kuti tizitsatirabe Khristu.

Landirani Mosangalala Udindo Wochokera kwa Mulungu

5, 6. (a) Kodi Paulo anayamikira Akhristu a ku Yerusalemu pa nkhani iti, nanga anawachenjeza za chiyani? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kupeputsa maudindo amene Mulungu watipatsa?

5 M’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Yerusalemu, mtumwi Paulo anayamikira Akhristuwo chifukwa chakuti anapirira mokhulupirika pa nthawi imene ankazunzidwa. Iye anati: “Pitirizani kukumbukira masiku akale pamene munapirira mpikisano waukulu m’masautso, mutaunikiridwa.” Yehova ankakumbukira kukhulupirira kwawo. (Aheb. 6:10; 10:32-34) Mawu a Paulo amenewa ayenera kuti anawalimbikitsa kwambiri Akhristu achiheberi. Koma m’kalata yomweyo Paulo anawachenjezanso za chizolowezi choipa chomwe ngati atachilekerera chikanachititsa kuti changu chawo potumikira Mulungu chichepe. Iye ananena kuti Akhristu ayenera kusamala kuti asamapereke zifukwa zokanira kutsatira malamulo a Mulungu.​—Aheb. 12:25.

6 Chenjezo limeneli lokhudza chizolowezi chopereka zifukwa zokanira udindo wochokera kwa Mulungu likugwiranso ntchito kwa Akhristu masiku ano. Tiyenera kuyesetsa kwambiri kuti tisapeputse udindo wathu monga Akhristu ndiponso kuti changu chathu potumikira Mulungu chisachepe. (Aheb. 10:39) Ndipotu kutumikira Mulungu ndi nkhani ya moyo kapena imfa.​—1 Tim. 4:16.

7, 8. (a) Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhalebe achangu potumikira Mulungu? (b) Ngati changu chimene tinali nacho chazirala, kodi tiyenera kukumbukira chiyani za Yehova ndi Yesu?

7 Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisamapereke zifukwa zokanira kukwaniritsa maudindo amene Mulungu watipatsa? Chinthu chimodzi chimene chingatithandize ndi kuganizira nthawi zonse zimene tinalonjeza pamene tinkadzipereka kwa Mulungu. Popeza kuti tinalonjeza kuti tidzaika chifuniro cha Yehova pamalo oyamba pa moyo wathu, timafunitsitsa kukwaniritsa lonjezo limeneli. (Werengani Mateyo 16:24.) Choncho nthawi zina tiyenera kufatsa n’kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikukhalabe ndi moyo wosonyeza kuti ndinadzipereka kwa Mulungu ngati mmene ndinkachitira nditangobatizidwa kumene? Kapena kodi changu changa chakhala chikuzirala?’

8 Ngati tadzifufuza moteremu n’kuona kuti changu chathu potumikira Yehova chazirala, tingachite bwino kukumbukira mawu olimbikitsa amene mneneri Zefaniya ananena. Iye anati: “Manja anu asakhale olefuka. Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe.” (Zef. 3:16, 17) Mawu amenewa analimbikitsa kwambiri Aisiraeli amene anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo ku Babulo. Koma ndi olimbikitsanso kwa anthu a Mulungu masiku ano. Popeza ntchito imene tikugwira ndi ya Yehova, tiyenera kukumbukira kuti Yehova ndi Mwana wake amatithandiza ndi kutilimbitsa kuti tikwaniritse udindo umene Mulungu watipatsa. (Mat. 28:20; Afil. 4:13) Tikamayesetsa kupitiriza kugwira ntchito ya Mulungu mwachangu adzatidalitsa ndipo adzatithandiza kuti tizipitabe patsogolo mwauzimu.

“Kufuna Ufumu Choyamba” Mwachangu

9, 10. Kodi mfundo yaikulu m’fanizo la Yesu la phwando lalikulu la chakudya chamadzulo ndi yotani, ndipo kodi tingaphunzirepo chiyani?

9 Pamene Yesu ankadya m’nyumba ya mkulu wa Afarisi, anapereka fanizo la phwando lalikulu la chakudya chamadzulo. M’fanizo limeneli iye anafotokoza mwayi umene anthu osiyanasiyana anapatsidwa woti adzalowe mu Ufumu wa kumwamba. Iye anafotokozanso tanthauzo la kupereka zifukwa zokanira. (Werengani Luka 14:16-21.) M’fanizo la Yesu limeneli, anthu amene anaitanidwa anapereka zifukwa zokanira kupita kuphwando. Wina anati akupita kukaona munda umene anali atangogula kumene. Winanso ananena kuti wagula ng’ombe ndipo akupita kukaziyesa. Pomwe wina anati: “Ine ndangokwatira kumene, choncho sindingathe kubwera.” Zifukwa zonsezi zinali zosamveka. Munthu asanagule munda amayamba wauona kaye ndipo asanagule ng’ombe amayamba waziyesa, choncho sipangakhale chifukwa chenicheni cholepherera kuchita zinthu zina chifukwa choti wangogula kumene munda kapena ng’ombe. Ndipo ukwati watsopano suyenera kulepheretsa munthu kulandira mwayi wamtengo wapatali umenewu. Mpake kuti woitana anthuyo anakwiya kwambiri.

10 Anthu a Mulungu onse angaphunzirepo pa fanizo la Yesu limeneli. Kodi angaphunzirepo chiyani? Sitiyenera kulola zinthu ngati zimene zatchulidwa m’fanizo la Yesu kukhala zofunika kuposa kutumikira Mulungu. Ngati Mkhristu saona zinthu zakuthupi moyenera, changu chake mu utumiki chingayambe kuchepa. (Werengani Luka 8:14.) Kuti zimenezi zisatichitikire, tiyenera kutsatira malangizo a Yesu akuti: “Pitirizani kufuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake.” (Mat. 6:33) N’zolimbikitsa kuona kuti atumiki a Mulungu, ana ndi achikulire omwe, akutsatira malangizo ofunika amenewa. Ndipotu ena asintha moyo wawo kuti ukhale wosalira zambiri n’cholinga choti akhale ndi nthawi yochuluka yochita utumiki. Iwo adzionera okha kuti munthu akamayesetsa mwachangu “kufuna Ufumu choyamba,” amakhala wosangalala ndiponso wokhutira.

11. Kodi ndi nkhani iti ya m’Baibulo imene imasonyeza kuti tifunika kutumikira Mulungu mwakhama ndiponso ndi mtima wonse?

11 Kuti timvetse kufunika kokhala achangu potumikira Mulungu, tiyeni tione zimene zinachitika pa moyo wa Mfumu Yoasi ya Isiraeli. Iye anada nkhawa kuti mwina Aaramu agonjetsa Aisiraeli, choncho anapita kwa Elisa akulira. Mneneriyu anamuuza kuti aponye muvi wake kumene kunali Suriya kudzera pa zenera, posonyeza kuti iwo adzagonjetsa mtunduwo mothandizidwa ndi Yehova. Zimenezi ziyenera kuti zinalimbikitsa mfumuyi. Kenako Elisa anauza Yoasi kuti atenge mivi yake n’kukwapula pansi. Yoasi anangokwapula katatu kokha. Elisa anakwiya kwambiri ndi zimenezi chifukwa chakuti akanakwapula ka 5 kapena 6, ‘akadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha.’ Choncho, Yoasi anangopambana katatu kokha chifukwa chakuti anachita zinthu mwamphwayi. (2 Maf. 13:14-19) Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhani imeneyi? Yehova adzatidalitsa kwambiri ngati tigwira ntchito yake mwakhama ndiponso ndi mtima wonse.

12. (a) Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe achangu potumikira Mulungu ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto? (b) Kodi inuyo mwapindula bwanji chifukwa chokhala achangu mu utumiki?

12 Mavuto amene timakumana nawo angayese changu ndiponso kudzipereka kwathu potumikira Mulungu. Abale ndi alongo ambiri akulimbana ndi mavuto a zachuma. Ena amakhumudwa chifukwa chakuti matenda aakulu akuwalepheretsa kuchita zambiri potumikira Yehova. Ngakhale zili choncho, aliyense angachite zinthu zimene zingamuthandize kukhalabe wachangu komanso kupitirizabe kutsatira Khristu ndi mtima wonse. Onani mfundo ndiponso malemba amene ali m’bokosi lakuti, “Kodi N’chiyani Chingakuthandizeni Kupitirizabe Kutsatira Khristu?” Ganizirani zimene mungachite kuti mutsatire bwinobwino malangizo amenewa. Mukatero mudzapindula kwambiri. Kuchita zambiri mu utumiki kumatithandiza kuti tiziona zinthu moyenera, moyo wathu umakhala wabwino ndipo timakhala ndi mtendere wochuluka komanso timakhala osangalala kwambiri. (1 Akor. 15:58) Kutumikira Mulungu ndi mtima wonse kumatithandiza “kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.”​—2 Pet. 3:12.

Onaninso Bwinobwino Mmene Zinthu Zilili Pamoyo Wanu

13. Kodi aliyense payekha angadziwe bwanji ngati akutumikira Mulungu ndi mtima wonse?

13 Komabe, ndi bwino kukumbukira kuti si nthawi zonse pamene kutumikira ndi mtima wonse kumatanthauza kuthera nthawi yochuluka mu utumiki. Zochitika pa moyo wa anthu zimakhala zosiyanasiyana. Munthu amene amathera ola limodzi kapena awiri mwezi uliwonse akhoza kusangalatsa Yehova kwambiri ngati izi ndi zonse zimene angathe kuchita malinga ndi mmene thanzi lake lilili. (Yerekezani ndi Maliko 12:41-44.) Choncho tiyenera kuona bwinobwino mmene zinthu zilili pa moyo wathu, kuti tidziwe ngati tikutumikiradi Mulungu ndi mtima wathu wonse. Popeza ndife otsatira a Khristu, tiyeneranso kuona zinthu mmene iye amazionera. (Werengani Aroma 15:5; 1 Akor. 2:16) Kodi n’chiyani chinali chofunika kwambiri pa moyo wa Yesu. Iye anauza khamu la anthu ochokera ku Kapernao kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso, chifukwa ndizo anandituma kudzachita.” (Luka 4:43; Yoh. 18:37) Ganizirani mmene Yesu analili wachangu mu utumiki wake, ndiye muonenso bwinobwino mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti mudziwe ngati mungathe kuwonjezera zimene mumachita mu utumiki.​—1 Akor. 11:1.

14. Kodi tingawonjezere utumiki wathu m’njira ziti?

14 Kuona bwinobwino mmene zinthu zilili pa moyo wathu kungatithandize kuona kuti tingathe kuwonjezera nthawi imene timathera mu utumiki. (Mat. 9:37, 38) Mwachitsanzo, achinyamata ambiri amene angomaliza kumene sukulu awonjezera utumiki wawo mwa kuchita upainiya ndipo akusangalala kwambiri. Kodi inunso mukufuna kukhala osangalala mwa kuchita zimenezi? Abale ndi alongo ena ataona bwinobwino mmene zinthu zilili pa moyo wawo, aganiza zosamukira kudera kumene kukufunika olengeza Ufumu m’dziko lawo kapena kunja kwa dziko lawo. Enanso aphunzira chinenero china pofuna kuthandiza anthu olankhula chinenerocho. Ngakhale kuti pamakhala mavuto ena kuti munthu awonjezere utumiki, kuchita zimenezi kumabweretsa madalitso ambiri ndipo kumachititsa kuti tithe kuthandiza anthu ena ‘kudziwa choonadi molondola.’​—1 Tim. 2:3, 4; 2 Akor. 9:6.

Zitsanzo za M’Baibulo Zofunika Kutengera

15, 16. Kodi tingatengere zitsanzo za ndani pa nkhani yokhala otsatira a Khristu achangu?

15 Kodi anthu ena omwe anakhala atumwi anatani Khristu atawaitana kuti akhale otsatira ake? Ponena za Mateyo, Baibulo limati: “Pamenepo atasiya zonse, ananyamuka ndi kumutsatira.” (Luka 5:27, 28) Komanso ponena za Petulo ndi Andireya omwe anali asodzi, timawerenga kuti: “Nthawi yomweyo anasiya maukonde awo namutsatira.” Kenako Yesu anaona Yakobe ndi Yohane akukonza maukonde limodzi ndi bambo awo. Kodi iwo anatani Yesu atawaitana? “Nthawi yomweyo anasiya ngalawa ija ndi bambo wawo namutsatira.”​—Mat. 4:18-22.

16 Chitsanzo china chabwino ndi Saulo yemwe anadzakhala mtumwi Paulo. Ngakhale kuti iye ankazunza mwankhanza otsatira a Khristu, anasintha n’kukhala ‘chiwiya chosankhika’ kuti achitire umboni za Khristu. “Nthawi yomweyo [Paulo] anayamba kulalikira za Yesu m’masunagoge, kuti Ameneyo ndiye Mwana wa Mulungu.” (Mac. 9:3-22) Ngakhale kuti anakumana ndi mavuto ambiri ndiponso kuzunzidwa, Paulo sanasiye kutumikira Mulungu mwachangu.​—2 Akor. 11:23-29; 12:15.

17. (a) Kodi cholinga chanu n’chiyani pa nkhani yotsatira Khristu? (b) Kodi timapeza madalitso otani tikamachita chifuniro cha Yehova ndi mtima wathu wonse komanso mphamvu zathu zonse?

17 Tikufunitsitsa kutengera chitsanzo cha ophunzira amenewa n’kuvomera kukhala otsatira a Khristu popanda kukayikira. (Aheb. 6:11, 12) Kodi ndi madalitso ati amene timapeza tikamayesetsabe kutsatira Khristu mwachangu ndiponso ndi mtima wonse? Timasangalala kwambiri pochita chifuniro cha Mulungu ndipo timakhala okhutira chifukwa cholandira utumiki wowonjezereka ndiponso maudindo mumpingo. (Sal. 40:8; werengani 1 Atesalonika 4:1.) Inde, tikamayesetsa kutsatira Khristu mwachangu timapeza madalitso ochuluka monga mtendere wa mumtima, kukhala okhutira, kuyanjidwa ndi Mulungu ndiponso timakhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.​—1 Tim. 4:10.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi ndi ntchito yofunika iti imene tapatsidwa, ndipo tiyenera kuiona motani?

• Kodi ndi chizolowezi chiti timene tiyenera kupewa, ndipo n’chifukwa chiyani?

• Kodi n’chiyani chimene tiyenera kuona bwinobwino?

• Kodi n’chiyani chingatithandize kupitirizabe kutsatira Khristu?

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 27]

Kodi N’chiyani Chingakuthandizeni Kupitirizabe Kutsatira Khristu?

▪ Muziwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse ndipo muzisinkhasinkha zimene mwawerenga.​—Sal. 1:1-3; 1 Tim. 4:15.

▪ Muzipemphera nthawi zonse kuti mzimu wa Mulungu ukuthandizeni ndi kukutsogolerani.​—Zek. 4:6; Luka 11:9, 13.

▪ Muzicheza ndi anthu omwe amasonyeza kuti ali ndi mtima wofuna kulalikira mwakhama.​—Miy. 13:20; Aheb. 10:24, 25.

▪ Zindikirani kuti tikukhala m’nthawi yofunika kuchita zinthu mwachangu.​—Aef. 5:15, 16.

▪ Zindikirani kuopsa kopereka zifukwa zokanira pa nkhani yotumikira Mulungu.​—Luka 9:59-62.

▪ Muzikumbukira nthawi zonse zimene munalonjeza podzipereka kwa Mulungu ndiponso madalitso amene mungapeze chifukwa chotumikira Yehova ndiponso kutsatira Khristu ndi mtima wonse.​—Sal. 116:12-14; 133:3; Miy. 10:22.