Samalani ndi Zolinga za Mtima Wanu
Baibulo limati: “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa.” (Yer. 17:9) Mtima wathu ukamalakalaka chinachake, timayesetsa kuchichita.
Koma Malemba amatichenjezanso kuti: “Maganizo oipa, za kupha anthu, za chigololo, za dama, za kuba, maumboni onama, ndi zonyoza Mulungu, zimachokera mumtima.” (Mat. 15:19) Mtima wathu ukhoza kutisocheretsa n’kutichititsa kuti tipeze zifukwa zochitira zinthu zina zimene Mulungu amadana nazo. Mwina sitingadziwenso kuti tikusochera mpaka titachita zoipazo. Ndiyeno kodi n’chiyani chingatithandize kudziwa zolinga za mtima wathu tisanachite zolakwika?
KODI MUNGADZIWE BWANJI ZOLINGA ZA MTIMA WANU?
Muziwerenga Baibulo tsiku lililonse n’kumasinkhasinkha zimene mwawerengazo.
Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu, ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse. Amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu, komanso mfundo za mafupa ndi mafuta a m’mafupa. Mawu a Mulungu amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.” (Aheb. 4:12) Kudzifufuza pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu kungatithandize kwambiri kudziwa zolinga za mtima wathu. Choncho tiyeni tiziwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse. Tikamatero timayamba kukhala ndi maganizo a Yehova n’kumaona zinthu mmene iye amazionera.
Kutsatira malangizo a m’Malemba ndiponso mfundo za m’Baibulo kungatithandize kukhala ndi chikumbumtima chabwino, chomwe ndi munthu wamkati amene amatichitira umboni. (Aroma 9:1) Zimene chikumbumtima chathu chingatiuze zingatithandize kuti tisachite zinthu zoipa. M’Baibulo mulinso nkhani zomwe “zinalembedwa kuti zitichenjeze.” (1 Akor. 10:11) Kuphunzira nkhani zoterezi kungatithandize kuti tipewe njira yolakwika. Kodi tingatani kuti zimenezi zitheke?
Muzipempha Mulungu kuti akuthandizeni kudziwa zolinga za mtima wanu.
Yehova ‘amasanthula mitima.’ (1 Mbiri 29:17) Iye “ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.” (1 Yoh. 3:20) Mulungu sangapusitsidwe. Iye angatithandize kudziwa zolinga za mtima wathu ngati timamuuza nkhawa zathu, mmene tikumvera mumtima mwathu komanso zimene tikulakalaka. Tingachite bwino kupempha Mulungu kuti ‘alenge mtima wolungama mkati mwathu.’ (Sal. 51:10) N’zoonekeratu kuti pemphero ndi lofunika kwambiri ngati tikufuna kudziwa zolinga za mtima wathu.
Muzimvetsera mwatcheru mukakhala pa misonkhano.
Kumvetsera mwatcheru pa misonkhano kungatithandize kudziwa bwinobwino mtima wathu kapena kuti munthu wathu wamkati. N’zoona kuti si nthawi zonse pamene timamva zinthu zatsopano pa misonkhano. Koma tikapezekapo timamvetsa bwino mfundo za m’Baibulo komanso timakumbutsidwa zinthu zina zimene zingatithandize kudziwa zolinga za mtima wathu. Ndemanga zimene abale ndi alongo amapereka zingatithandizenso kukonza munthu wathu wamkati. (Miy. 27:17) Kujomba dala ku misonkhano n’koopsa chifukwa siticheza ndi Akhristu anzathu. Zimenezi zingachititse kuti tiyambe ‘kufunafuna zolakalaka zathu zosonyeza kudzikonda.’ (Miy. 18:1) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ine ndimakondadi kupezeka pa misonkhano yonse? Kodi ndimapindula nayodi?’—Aheb. 10:24, 25.
KODI MTIMA WATHU UKUTITSOGOLERA KUTI?
Mtima wathu wonyengawu ukhoza kutisocheretsa m’njira zambiri. Tiyeni tikambirane njira zinayi izi: Kufunafuna chuma, kumwa mowa, anthu amene timacheza nawo komanso zosangalatsa.
Kufunafuna chuma.
Anthufe mwachibadwa timafuna kukhala ndi zinthu. Koma Yesu anapereka chenjezo pa nkhani yodalira kwambiri chuma. M’fanizo lina, Yesu ananena za munthu wina wachuma amene nkhokwe zake zinali zodzaza ndi zokolola. Iye analibe malo osungira zokolola zina zatsopano. Munthuyo anaganiza zopasula nkhokwe zakezo n’kumanga zina zazikulu. Ankadziuza kuti: “Tirigu wanga yense ndi zinthu zanga zonse zabwino ndidzazitutira mmenemo. Ndipo ndidzauza moyo wanga kuti: ‘Moyo wangawe, uli ndi zinthu zambiri zabwino mwakuti zisungika kwa zaka zambiri. Ungoti phee tsopano, ndipo udye, umwe ndi kusangalala.’” Koma munthuyu anaiwala mfundo yakuti akhoza kumwalira usiku womwewo.—Luka 12:16-20.
Pamene tikukula, tikhoza kumaganizira zosunga katundu wina n’cholinga choti adzatithandize tikadzakalamba. Mwina tingayambe kuona kuti palibe vuto ngati tikugwira ovataimu m’masiku a misonkhano kapena kusiya kuchita zinthu zina zokhudza kulambira. Kodi sitifunika kusamala ndi maganizo amenewa? Mwina ndife achinyamata ndipo tikudziwa kuti palibe ntchito ina iliyonse yomwe ndi yabwino kuposa utumiki wa nthawi zonse. Koma kodi timalephera kuyamba upainiya poganiza kuti tipeze kaye chuma? Komatu ndi bwino kuyesetsa panopa kuti tikhale olemera kwa Mulungu. Kodi mukudziwa ngati mawa mudzakhaledi ndi moyo?
Kumwa mowa.
Pa Miyambo 23:20, timawerenga kuti: “Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambiri.” Ngati munthu amalakalaka kwambiri kumwa mowa angamaganize kuti palibe vuto ngati amamwa kawirikawiri. Akhoza kumanena kuti amangomwa kuti asangalale osati kuti aledzere. Ngati timafunika kumwa mowa kuti tisangalale ndi bwino kuganizira bwino nkhaniyi kuti tidziwe zolinga za mtima wathu.
Anthu amene timacheza nawo.
Anthufe sitingapewe kukumana ndi anthu osakhulupirira kusukulu, kuntchito kapena mu utumiki. Koma kucheza kwambiri ndi anthu osakhulupirira ndi nkhani ina. Kodi timadzikhululukira pocheza ndi osakhulupirira n’kumanena kuti iwo ali ndi makhalidwe ambiri abwino? Komatu Baibulo limatichenjeza kuti: “Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akor. 15:33) Zinthu zonyansa zochepa kwambiri zikhoza kuwonongeratu madzi abwino. N’chimodzimodzi ndi kucheza ndi anthu osakhulupirira. Kukhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova komanso kutichititsa kusintha kaganizidwe, kavalidwe, kalankhulidwe ndiponso khalidwe lathu.
Zosangalatsa.
Masiku ano zipangizo zamakono zimachititsa kuti tikhale ndi mwayi wopeza zosangalatsa zambirimbiri. Koma vuto ndi lakuti zosangalatsa zambiri n’zokayikitsa ndipo zina n’zosayenera. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Chonyansa chamtundu uliwonse chisatchulidwe n’komwe pakati panu.’ (Aef. 5:3) Koma bwanji ngati mtima wathu umalakalaka kuonera kapena kumvetsera zinthu zosayenera? Mwina tikhoza kumaganiza kuti munthu amafunika kusangalala ndipo aliyense ali ndi ufulu wosankha zosangalatsa. Koma tiyenera kutsatira malangizo a Paulo ndipo tisalole kuonera kapena kumvetsera chonyansa chilichonse.
N’ZOTHEKA KUSINTHA
Ngati tasocheretsedwa ndi mtima wathu ndipo timaona kuti palibe vuto kuchita zinthu zina zosayenera, n’zotheka kusintha. (Aef. 4:22-24) Tiyeni tikambirane zitsanzo ziwiri.
Miguel * anafunika kusintha maganizo pa nkhani ya chuma. Iye anati: “Ine, mkazi wanga komanso mwana wanga wamwamuna timachokera m’dziko limene anthu amaona kuti kukhala ndi zipangizo zamakono n’kofunika kwambiri. Pa nthawi ina, ndinkachita khama kwambiri kuti ndipeze zonse zimene ndingathe, ndipo ndinkaganiza kuti sindingayambe mtima wokonda chuma. Koma ndinadzazindikira kuti kufunafuna chuma kuli ngati msewu wopanda malire. Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kudziwa maganizo anga komanso zolinga za mtima wanga. Ndinamufotokozera kuti ine ndi banja langa tikufuna kumutumikira ndi mtima wonse. Tinakwanitsa kusintha moyo wathu n’kuyamba kukhala moyo wosalira zambiri ndipo tinasamukira kudera kumene kunkafunika ofalitsa ambiri. Pasanapite nthawi tinayamba kuchita upainiya. Panopa tazindikira kuti kukhala ndi moyo wosangalala sikudalira kukhala ndi chuma chochuluka.”
Kudzifufuza moona mtima kunathandiza Lee kusiya kugwirizana ndi anthu oipa. Iye anati: “Bizinezi imene ndinkachita, inkachititsa kuti ndizicheza kwambiri ndi abizinezi anzanga omwe si Mboni. Nthawi zambiri tikakumana kuti tikambirane za bizinezi, tinkamwa mowa kwambiri. Ngakhale kuti ndinkadziwa kuti zimenezi si zabwino, ndinkasangalala kukhalapo. Nthawi zambiri ndinkamwa mpaka kutsala pang’ono kuledzera pambuyo pake n’kumadziimba mlandu. Ndiyeno ndinayamba kudzifufuza kuti ndidziwe bwino mtima wanga. Malangizo a m’Mawu a Mulungu komanso a akulu anandithandiza kudziwa kuti ndimalakalaka kwambiri kucheza ndi anthu omwe sakonda Yehova. Panopa anthu amenewa ndimangokambirana nawo pafoni kuti ndisamacheze nawo kwambiri.”
Timafunika kudzifufuza moona mtima kuti tidziwe zolinga za mtima wathu. Tikamatero, tizipempha Yehova kuti atithandize popeza “iye amadziwa zinsinsi za mumtima.” (Sal. 44:21) Mulungu watipatsanso Mawu ake omwe ali ngati galasi loti tizidziyanganirapo. (Yak. 1:22-25) Malangizo ena othandiza timawapeza m’mabuku athu komanso pa misonkhano. Zinthu zonsezi zikhoza kutithandiza kuteteza mtima wathu komanso kuyenda m’njira ya chilungamo.
^ ndime 18 Mayina asinthidwa.