Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Mexico

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Mexico

ZIMAKHALA zolimbikitsa kuona achinyamata ambiri akusintha n’kuyamba kukhala moyo wosalira zambiri n’cholinga choti awonjezere zimene amachita mu utumiki. (Mat. 6:22) Kodi iwo amasintha zinthu ziti? Kodi amakumana ndi mavuto otani? Kuti tipeze mayankho, tiyeni tikambirane za abale ndi alongo oterewa amene akutumikira ku Mexico.

“TINAFUNIKA KUSINTHA”

Dustin ndi Jassa a ku United States anakwatirana mu January 2007. Iwo ankafunitsitsa kupeza boti kuti azikhala m’menemo kwa chaka chonse. Pasanapite nthawi yaitali, anapeza botilo ndipo analikocheza pafupi ndi kutauni ya Astoria, m’dera la Oregon ku United States. Malowa anali pafupi ndi nyanja ya Pacific ndipo ndi okongola kwambiri chifukwa kuli mitengo ndiponso mapiri. Dustin anati: “Ukakhala pamalowa, kulikonse kumene ungayang’ane n’kokongola kwambiri.” Dustin ndi mkazi wake ankaganiza kuti akukhala moyo wosalira zambiri ndipo akudalira Yehova. Ankadziuza kuti: ‘Anthufe tikungokhala m’kaboti kakang’ono, tikugwira ntchito nthawi yochepa, tili mu mpingo wa chinenero china ndipo nthawi zina timachita upainiya wothandiza.’ Koma kenako anazindikira kuti akungodzinamiza. Dustin anati: “M’malo mochita zinthu ndi mpingo tinkangokhalira kukonza  boti lathu. Tinazindikira kuti ngati tikufunadi kuika Yehova pa malo oyamba, tinafunika kusintha zinthu zina.”

Dustin ndi Jassa

Jassa anati: “Ndisanakwatiwe ndinkakhala ku Mexico ndipo ndinali mu mpingo wa Chingelezi. Ndinkasangalala kwambiri kutumikira kumeneko ndipo ndinkafunitsitsa kubwerera.” Kuti akhale ndi mtima wofunitsitsa kukatumikira kudziko lina, Dustin ndi Jassa ankawerenga nkhani za Akhristu amene anasamukira kumadera ena kumene anthu ambiri ankafuna kudziwa choonadi. Ankachita zimenezi pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja. (Yoh. 4:35) Dustin anati: “Nafenso tinkafuna kukatumikira kumadera oterewa.” Anzawo a ku Mexico atawauza kuti pali kagulu kena kamene kalibe ofalitsa ambiri, Dustin ndi Jassa anaganiza zopita kumeneko. Iwo anasiya ntchito, anagulitsa boti lawo lija ndipo anasamukira ku Mexico.

“TINACHITA BWINO KWAMBIRI”

Dustin ndi Jassa anakakhala m’tauni ya Tecomán. Tauniyi ilinso pafupi ndi nyanja ya Pacific koma ili pa mtunda wa makilomita 4,345 kum’mwera kwa Astoria. Dustin anati: “Kumene tinkakhala poyamba kuja kunali kozizirira bwino ndiponso kunali mapiri okongola kwambiri. Koma kuno n’kotentha kwambiri ndipo kuli mitengo ya mandimu yokhayokha.” Atangofika kumene, sanapeze ntchito. Chifukwa chosowa ndalama, ankangodya mpunga ndi nyemba masana ndi madzulo. Jassa anati: “Koma zisanafike poipa kwambiri, anthu amene tinkaphunzira nawo Baibulo anayamba kutipatsa mango, nthochi, mapapaya ndi matumba a mandimu.” Kenako banjali linapeza ntchito pa Intaneti. Analembedwa ntchito ndi sukulu ya ku Taiwan yophunzitsa chilankhulo. Ndalama zimene amalandira zimakwanira kugula zinthu zofunika pa moyo wawo.

Kodi Dustin ndi Jassa amamva bwanji ndi zimene anachitazi? Iwo anati: “Timaona kuti tinachita bwino kwambiri kusamuka. Panopa ubwenzi wathu ndi Yehova ndi wolimba kwambiri ndipo ifenso tikugwirizana kwabasi. Tsiku lililonse timachitira limodzi zinthu monga kulalikira, kukambirana mmene tingathandizire maphunziro athu komanso kukonzekera misonkhano. Moyo wathunso si wopanikiza ngati kale. Pano tikumvetsa tsopano mfundo ya pa Salimo 34:8 yakuti: ‘Talawani ndipo muone kuti Yehova ndi wabwino.’”

N’CHIFUKWA CHIYANI AMBIRI AMADZIPEREKA?

Pali abale ndi alongo oposa 2,900 amene asamukira kumadera amene kulibe ofalitsa ambiri m’dziko la Mexico. Ena ndi apabanja ena ayi, ndipo ambiri ndi azaka za m’ma 20 kapena 30. N’chifukwa chiyani anthuwa amadzipereka chonchi? Ambiri atafunsidwa  funso limeneli, anatchula zifukwa zitatu zikuluzikulu. Kodi zifukwa zake ndi ziti?

Leticia ndi Hermilo

Kukonda Yehova ndi anthu. Mlongo wina dzina lake Leticia anabatizidwa ali ndi zaka 18. Iye anati: “Pamene ndinadzipereka kwa Yehova, ndinazindikira kuti ndifunika kum’tumikira ndi mtima wanga wonse komanso moyo wanga wonse. Pofuna kusonyeza kuti ndimakondadi Yehova, ndinafuna kugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zanga pomutumikira.” (Maliko 12:30) Hermilo, yemwe anakwatira Leticia, anapita kukatumikira kudera losowa ali ndi zaka za m’ma 20. Iye anati: “Ndinaona kuti njira yaikulu imene ndingasonyezere kuti ndimakonda anthu ndi kuwathandiza kudziwa Yehova.” (Maliko 12:31) Iye anasamuka mumzinda wa Monterrey n’kusiya ntchito ya kubanki imene ankagwira. Analolera kusiya moyo wosasowa kanthu n’kusamukira kukatauni kakang’ono.

Essly

Kuti apeze chimwemwe chenicheni. Leticia atangobatizidwa anatsagana ndi mlongo wina amene ankachita upainiya kutauni ina kumene anakalalikira kwa mwezi umodzi. Leticia anati: “Ndinagoma kwambiri. Ndinasangalala kuona anthu akuchita chidwi ndi uthenga umene tinkalalikira. Pamene mweziwo unkatha ndinati: ‘Zoyenera kuchita n’zimenezi basi, palibenso china!’” Izi n’zimene zinachitikiranso mtsikana wina wazaka za m’ma 20, dzina lake Essly. Iye anaganiza zoyamba upainiya chifukwa choona kuti ndi ntchito yosangalatsa. Iye ali kusekondale, anakacheza ndi Akhristu ambiri amene ankatumikira kumadera amene kunalibe ofalitsa ambiri. Iye anati: “Abale ndi alongo ankaoneka osangalala kwambiri moti nanenso ndinayamba kulakalaka utumikiwu.” Pali alongo ankhaninkhani amene amaonanso choncho moti anayamba utumikiwu. Ku Mexico, kuli alongo osakwatiwa oposa 680 amene akutumikira kumadera amene kulibe ofalitsa ambiri. Kunena zoona, alongowa akupereka chitsanzo chabwino kwambiri.

Kuti moyo wathu ukhale waphindu. Essly atangomaliza maphunziro a kusekondale anapatsidwa mwayi woti alipiriridwe ku yunivesite. Anzake anamulimbikitsa kuti avomere n’cholinga choti apeze digiri, ntchito yabwino, galimoto komanso kuti azisangalala. Koma iye sanamvere zimenezo. Essly anati: “Akhristu anzanga amene anachita zimenezi anasiya kuika Ufumu patsogolo. Ndinaonanso kuti zinthu sizinkawayendera bwino chifukwa chotengeka kwambiri ndi zinthu za m’dzikoli. Ine ndinkafuna kugwiritsa ntchito mphamvu zanga potumikira Yehova.”

Racquel ndi Phillip

Essly anangochita makosi ena omwe anamuthandiza kupeza ntchito yoti izimuthandiza kupeza  kangachepe uku akuchita upainiya. Kenako anasamukira kudera limene kunalibe ofalitsa ambiri. Iye anaphunziranso zilankhulo za anthu akuderalo. Essly watumikira kuderali kwa zaka zitatu ndipo anati: “Ndikusangalala kwambiri kutumikira kudera lino ndipo panopa moyo wanga ndi waphindu. Chofunika kwambiri n’chakuti kwandithandiza kulimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova.” Phillip ndi mkazi wake Racquel, a ku United States, akuvomerezanso mfundo imeneyi. Iwo ali ndi zaka za m’ma 30 ndipo anati: “Zinthu m’dzikoli zikusintha kwabasi moti anthu ambiri amadera nkhawa zam’tsogolo. Koma kutumikira m’dera limene anthu ambiri amafuna kumva uthenga wa m’Baibulo kwatithandiza kuti tisamadere nkhawa kwambiri tsogolo lathu. Zimasangalatsa kwambiri.”

ZIMENE AMACHITA AKAKUMANA NDI MAVUTO

Verónica

N’zoona kuti kutumikira kumadera amene kulibe ofalitsa ambiri kuli ndi mavuto ake. Vuto lina ndi kapezedwe ka ndalama. Koma kuti zinthu ziyende, munthu amafunika kusintha mogwirizana ndi mmene zinthu zilili kuderalo. Verónica, yemwe wachita upainiya kwa nthawi yaitali, anati: “Kudera lina kumene ndinkachita upainiya, ndinkaphika zakudya zotchipa n’kumagulitsa. Kwina ndinkagulitsa zovala komanso kumeta anthu. Pano ndimagwira ntchito yoyeretsa m’nyumba komanso kuphunzitsa makolo luso lolankhulana ndi ana awo.”

Kukhala ndi anthu achikhalidwe china n’kovutanso makamaka kukakhala kumadera akumidzi. Izi n’zimene zinachitikira Phillip ndi Racquel pamene ankalalikira kudera la anthu olankhula Chinawato. Phillip anati: “Chikhalidwe cha anthuwa n’chosiyana kwambiri ndi chathu.” N’chiyani chinathandiza Phillip ndi mkazi wake? Iye anati: “Tinkaganizira kwambiri zinthu zabwino zimene tinkaona kwa anthuwa. Mabanja awo amakhala ogwirizana, amachita zinthu moona mtima ndipo ndi anthu owolowa manja.” Racquel anati: “Tinaphunzira zambiri kuderali komanso potumikira ndi abale ndi alongo a kumeneko.”

ZIMENE MUNGACHITE POKONZEKERA

Ngati mukufuna kukatumikira kudera limene kulibe ofalitsa ambiri, kodi mungakonzekere bwanji? Abale ndi alongo amene achita zimenezi amati: Usananyamuke umafunika kuyamba kukhala moyo wosalira zambiri ndiponso kumakhutira ndi zimene uli nazo. (Afil. 4:11, 12) Koma pali zinanso zimene mungachite. Leticia anati: “Ndinkapewa ntchito zolembedwa zimene zingandichititse kumera mizu pamalo enaake. Izi zinandithandiza kuti ndizisamuka pa nthawi iliyonse kupita kulikonse kumene ndikufuna.” Hermilo anati: “Ndinaphunzira kuphika, kuchapa ndi kusita.” Verónica anati: “Pa nthawi imene ndinali kunyumba, ndinkathandiza makolo ndi abale anga kuyeretsa pakhomo komanso ndinkaphika chakudya chotchipa koma chopatsa thanzi. Ndinaphunziranso kusunga ndalama.”

Amelia ndi Levi

Levi ndi Amelia a ku United States akhala m’banja zaka 8 ndipo ananena kuti kutchula zinthu mosapita m’mbali popemphera kunawathandiza pokonzekera kukatumikira ku Mexico. Levi anati: “Tinawerengetsa ndalama zimene zingafunike kuti tikatumikire kudziko lina kwa chaka chathunthu ndipo tinapempha Yehova kuti atithandize kusunga ndalama zimenezo.” Patangopita miyezi yochepa, ndalama zimene ankafunazo zinakwana ndipo ananyamuka nthawi yomweyo. Levi anati: “Yehova anayankha pemphero lathu ndipo ndinaona kuti ndi nthawi yoti tinyamuke basi.” Amelia anati: “Poyamba tinkaganiza kuti tingotumikira kuno kwa chaka chimodzi, koma pano tatha zaka 7 ndipo sitifuna kubwerera. Kunoko tikuona kuti Yehova akutithandiza kwambiri. Tsiku lililonse timaona umboni wakuti iye ndi wabwino.”

Adam ndi Jennifer

Adam ndi Jennifer a ku United States ali mu mpingo wa Chingelezi ku Mexico. Iwo anaonanso kuti pemphero ndi lothandiza kwambiri ndipo anati: “Musamadikire kuti chilichonse chikhale bwino. Muuzeni Yehova m’pemphero kuti mukufuna kukatumikira kwinakwake ndipo chitani zinthu mogwirizana ndi pempherolo. Yambani kukhala moyo wosalira zambiri, kenako lemberani kalata ofesi ya nthambi ya dziko limene mukufunalo. Pambuyo poona kuti mungakwanitse kukakhala kumeneko, samukani.” * Mukatero mudzasangalala kwambiri ndipo mudzapeza madalitso osaneneka.

^ ndime 21 Kuti mudziwe zambiri onani nkhani ya mutu wakuti, “Kodi ‘Mungawolokere ku Makedoniya’?” mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 2011.