Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandiza Mwana Wanu Panthawi Yachisoni

Kuthandiza Mwana Wanu Panthawi Yachisoni

Kuthandiza Mwana Wanu Panthawi Yachisoni

M’SITOLO ina yogulitsa mabuku, mayi wina atakhumudwa anadandaulira wogulitsa m’sitoloyo kuti: “Muli ndi mabuku ambirimbiri, koma mulibiretu buku loti lingathandize mwana wanga.” Mayiyu anali kufunafuna malangizo omwe angapatse mwana wake pomuthandiza chifukwa cha chisoni chimene anali nacho, wachibale wawo atamwalira mwadzidzidzi.

M’pomveka kuti mayiyu anali ndi nkhawa chonchi. Mwana wamng’ono amasokonezeka maganizo kwambiri ndi imfa ya munthu amene anali kum’konda. Ana amasangalala ndiponso amakula bwino akamasamalidwa ndi anthu a m’banja mwawo, komabe munthu aliyense wa m’banjamo akhoza kumwalira. Monga kholo, kodi mungam’thandize motani mwana wanu ngati wina m’banjamo watsala pang’ono kumwalira kapena ngati wamwalira kale?

N’zoona kuti wachibale akamwalira nanunso mungamavutike ndi chisoni ndipo mwinanso mungasokonezeke maganizo kwambiri. Komabe, musaiwale kuti mwana wanu amafunikira kuti mumulimbikitse. Buku lina lofalitsidwa ndi achipatala china ku Minnesota, m’dziko la United States linati: “Ana akapanda kuuzidwa bwinobwino za imfa, koma n’kumangomva mwa apo ndi apo anthu ena akukambirana, nthawi zambiri iwo amatha kutanthauzira molakwika zimene amvazo.” Bukuli linanenanso kuti: “Ana amafunika kuuzidwa zoona.” Motero ndi bwino kuwafotokozera zoona zenizeni zokhudza imfa malinga ndi msinkhu wawo ngakhale kuti kuchita zimenezi n’kovuta chifukwa chakuti luso la ana lomvetsa zinthu limasiyanasiyana.​—1 Akorinto 13:11.

Mmene Mungafotokozere za Imfa kwa Ana Anu

Akatswiri ena ochita kafukufuku amanena kuti pofotokozera mwana za imfa, makolo ayenera kupewa kugwiritsa ntchito mawu ngati akuti “wagona,” “wasowa” kapena “wachokapo.” Kugwiritsa ntchito mawu ngati amenewa popanda kuwafotokoza bwinobwino kungathe kusokoneza mwana. N’zoona kuti Yesu anafanizira imfa ndi kugona ndipo panali pomveka kutero. Komabe, tisaiwale kuti panthawiyi iye sankalankhula ndi ana komanso anafotokozera fanizo lakelo. Yesu anauza otsatira ake kuti: “Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula.” Ngakhale kuti ophunzirawo anali anthu akuluakulu, “iwo anaganiza kuti [Yesu] anali kunena za kugona tulo teniteni.” Choncho, Yesu anawafotokozera momveka bwino kuti: “Lazaro wamwalira.” (Yohane 11:11-14) Ngati anthu akuluakulu anafunika kuwafotokozera chonchi, ndiye kuli bwanji ana?

M’buku lawo lofotokoza mmene makolo angathandizire ana kupirira chisoni, Mary Ann Emswiler ndi James P. Emswiler anati: “Pofotokozera mwana za imfa, makolo angayesetse kugwiritsa ntchito mawu osachititsa mantha kwa mwanayo. Koma kuchita zimenezi kungachititse mwanayo kuyamba kuganizira zinthu zimene anali asanaziganizirepo n’komwe, zimene zingakhale zoopsa.” Mwachitsanzo, kungomuuza mwana wamng’ono kuti munthu amene wamwalirayo wagona, kungam’chititse kuti aziopa kugona usiku poganiza kuti sangadzukenso. Kapena angaganize kuti wathawidwa ngati atangouzidwa kuti munthu womwalirayo “wachokapo.”

Pofotokozera mwana za imfa, makolo ambiri aona kuti ana amamvetsa bwino akauzidwa mawu osakuluwika. (1 Akorinto 14:9) Akatswiri ena ochita kafukufuku amanena kuti ndi bwino kumulimbikitsa mwana wanuyo kuti azifunsa mafunso ndiponso kuti azifotokoza zimene zikum’detsa nkhawa. Kulankhula naye za nkhaniyi mobwerezabwereza kungam’thandize kuti aimvetse bwino ndiponso kungathandize inuyo kupeza njira zina zothandizira mwana wanuyo.

Kumene Tingapeze Malangizo Odalirika

Panthawi yachisoniyo, mwana wanu angakudalireni kuti mum’tsogolere, kumulimbikitsa ndiponso kuyankha mafunso ake. Ndiyeno kodi n’kuti kumene mungapeze mfundo zodalirika zofotokoza za imfa? Anthu ambiri aona kuti Baibulo limawatonthoza ndi kuwapatsa chiyembekezo. Baibulo limafotokoza momveka bwino za mmene imfa inayambira, mmene akufa aliri ndiponso za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa. Mfundo ya choonadi yosavuta kumva yakuti “akufa sadziwa kanthu bi,” ingam’thandize mwanayo kuzindikira kuti wachibale kapena mnzake amene wamwalira sakuvutika. (Mlaliki 9:5) Komanso kudzera m’Baibulo, Mulungu amatipatsa chiyembekezo chakuti m’dziko lapansi laparadaiso, tidzaonananso ndi abale komanso anansi athu amene anamwalira.​—Yohane 5:28, 29.

Mwa kugwiritsa ntchito Malemba Opatulika, mungathandize mwana wanu kudziwa kuti Baibulo lili ndi malangizo odalirika ndiponso limalimbikitsa munthu pavuto lililonse limene angakumane nalo. Komanso, mwanayo angaone kuti inuyo mumadalira malangizo a m’Mawu a Mulungu pankhani zofunika kwambiri.​—Miyambo 22:6; 2 Timoteyo 3:15.

Kuyankha Mafunso Anu

N’kutheka kuti nthawi zina mungathedwe nzeru kwambiri pamene mukuthandiza mwana wanu chifukwa cha chisoni chimene ali nacho. Ndiye zikatere mungachite chiyani? * Tiyeni tione ena mwa mafunso amene mungakhale nawo.

Kodi n’kulakwa kumusonyeza mwana wanga kuti ndili ndi chisoni? Mwachibadwa makolo amafuna kuteteza ana awo. Komano kodi kulira pamaso pa mwana wanu n’kulakwa? Makolo ambiri aona kuti ndi bwino kusabisa chisoni chawo ndipo pochita zimenezi amasonyeza ana awo kuti kumva chisoni sikulakwa. Ndipo makolo ena akambiranapo ndi ana awo zitsanzo za m’Baibulo za anthu omwe analira pamaso pa anthu ena. Mwachitsanzo, Yesu analira mnzake wapamtima Lazaro atamwalira. Iye sanabise chisoni chimene anali nacho.​—Yohane 11:35.

Kodi ndi bwino kuti mwana wanga wamng’ono apite ku maliro? Ngati mukufuna kuti mwana apite ku maliro, mwina ndi bwino kumuuziratu zimene zikachitike kumeneko. N’zoona kuti nthawi zina makolo angaone kuti pali zifukwa zomveka zoti ana awo asapitire ku maliro. Ana omwe apita ku mwambo wa maliro wa Mboni za Yehova angakapindule ndi nkhani ya m’Baibulo imene imakambidwa kumeneko. Komanso, mwana angatonthozedwe ndi kulimbikitsidwa ndi chikondi chimene anthu obwera pa malirowo amasonyeza.​—Aroma 12:10, 15; Yohane 13:34, 35.

Kodi ndiyenera kupewa kuuza mwana wanga chilichonse chokhudza womwalirayo? Akatswiri ena ochita kafukufuku amanena kuti ngati mupewa kunena chilichonse, mwana wanu angaganize kuti mukum’bisira chinachake chokhudza munthuyo kapena mukungofuna kuti womwalirayo aiwalike. Katswiri wina wolemba mabuku dzina lake Julia Rathkey anati: “M’pofunika kuthandiza anawo kuti asamachite mantha akakumbukira za womwalirayo.” Kulankhula momasuka za munthu womwalirayo, mwinanso kutchula zinthu zabwino zokhudza khalidwe ndi moyo wake kungathandizenso kwambiri panyengo yachisoniyo. Makolo amene ndi a Mboni za Yehova amalimbikitsa ana awo ndi zimene Baibulo limanena zoti akufa adzauka ndi kukhala m’paradaiso padziko lapansi. M’dziko limeneli simudzakhala matenda ndiponso imfa.​—Chivumbulutso 21:4.

Kodi ndingam’thandize motani mwana wanga panthawi yachisoni? Panthawi imeneyi, mwana wanu angathe kudwala, kuoneka wokhumudwa ndipo mwinanso kusokonezeka maganizo. Musadabwe ngati mwanayo akukukakamirani kwambiri, akuda nkhawa kwambiri chifukwa choti mwachedwa kufika ku nyumba kapena chifukwa choti mwadwala, kapenanso ngati akudziimba mlandu kuti ndi iye amene wachititsa kuti munthuyo amwalire. Kodi mungamuthandize bwanji? Yesetsani kuchita zinthu zoti mwana wanuyo asaganize kuti simukudziwa kuti iye akuvutika maganizo. Mwachitsanzo, khalani womvetsa ndiponso watcheru ndi mmene mwanayo wakhudzidwira ndi chisonicho. Musathamangire kum’dzudzula kuti akulakwa kukhala ndi chisoni kapena kuganiza kuti iye akungokokomeza zinthu. Muzimulimbikitsa nthawi zonse ndipo muzimulola kukufunsani mafunso pazinthu zimene zikum’detsa nkhawa ndiponso azilankhula nanu momasuka. Mungalimbikitse chikhulupiriro cha mwanayo, ndiponso chanu “mwa chitonthozo cha m’Malemba.”​—Aroma 15:4.

Kodi payenera kutenga nthawi yaitali motani kuti banja lathu liyambirenso kuchita zinthu monga kale? Akatswiri ena amalimbikitsa mabanja kuti aziyesetsa kupitiriza kuchita zinthu zonse monga mmene ankachitira kale. Kupitiriza kuchita zinthu zofunika kungathandize kuchepetsa chisoni. Makolo ambiri omwe ndi a Mboni za Yehova aona kuti kupitiriza kuchita zinthu zauzimu, monga kuchita phunziro la Baibulo labanja ndiponso kupita ku misonkhano yachikhristu nthawi zonse, kumalimbikitsa kwambiri banja lonse.​—Deuteronomo 6:4-9; Aheberi 10:24, 25.

Panopa, popeza kuti Yehova Mulungu sanathetse matenda ndi imfa, ana apitirizabe kuvutika ndi chisoni chifukwa cha imfa ya wachibale kapena mnansi wawo. (Yesaya 25:8) Komabe, ana angathandizidwe kupirira panthawi yachisoni akamatsogoleredwa bwino ndiponso kulimbikitsidwa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Cholinga cha mfundo zimene zili m’nkhani ino sikukhazikitsa malamulo ayi. Ndi bwino kudziwa kuti zochitika ndiponso miyambo ya pamaliro imasiyana m’mayiko komanso m’zikhalidwe zosiyanasiyana.

[Mawu Otsindika patsamba 19]

Limbikitsani mwana wanuyo kuti azifunsa mafunso ndiponso kuti azifotokoza zimene zikum’detsa nkhawa

[Chithunzi patsamba 20]

Pitirizani kuchita zinthu zimene mumachita nthawi zonse, kuphatikizapo phunziro la Baibulo labanja