Kusunga Misozi M’nsupa
Kusunga Misozi M’nsupa
PANTHAWI ina Davide ali mnyamata, ankangokhalira kuthawathawa. Tsiku lina anathedwa nzeru kwambiri moti misozi inkangoyenderera m’masaya. Kenako anapempha Yehova Mulungu kuti amukomere mtima ndi kum’chitira chifundo. Iye anati: “Sungani misozi yanga m’nsupa yanu.” (Salmo 56:8) Patapita nthawi Davide anadzakhala mfumu ya Isiraeli. Koma kodi nsupa imene anatchulayo inali yotani? Ndipo zikanatheka bwanji kuti Mulungu asunge misozi ya Davide m’nsupayo?
Nsupayi inali thumba la chikopa limene anthu ankasungamo zinthu monga madzi, mafuta ndi mowa. Davide ankadziwa bwino nsupa yotereyi. Anthu monga Atuwaregi, amene amakhala ku chipululu cha Sahara, amagwiritsabe ntchito matumba oterewa opangidwa ndi chikopa chonse cha mbuzi kapena nkhosa. Matumba amenewa amatha kusunga madzi ambirimbiri malinga ndi kukula kwa chikopa chimene apangira. Ndipo madzi akasungidwa m’matumba amenewa amakhalabe ozizira ngakhale kunja kutatentha kwambiri m’chipululu. Kale matumbawa ankanyamulidwa pa abulu kapena ngamila basi. Koma masiku ano mungathe kuona matumba otere atakolekedwa kutsogolo kwa galimoto zamphamvu zotha kuyenda m’misewu yovuta.
Mawu okhudza mtima amene Davide ananena okhudza matumba amenewa angatilimbikitsenso ifeyo kwambiri. Angatilimbikitse motani? Pajatu Baibulo limati Satana ndiye akulamulira dzikoli ndiponso kuti masiku ano ali ndi “mkwiyo waukulu.” N’chifukwa chake padzikoli pali mavuto osaneneka. (Chivumbulutso 12:12) Pachifukwa chimenechi, pali anthu ambiri, makamaka amene akuyesetsa kutumikira Mulungu, amene mofanana ndi Davide amavutika maganizo ndiponso amakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Kodi umu ndi mmene zinthu zilili ndi inunso? Anthu okhulupirika amalimba mtima pa mavuto amene amakumana nawo ndipo ngakhale atafika ‘polira,’ amayesetsabe kukhala okhulupirika. (Salmo 126:6) Iwowa sayenera kukayika kuti Yehova, Atate wawo wakumwamba, amaona mayesero awowo komanso mmene akumvera mumtima mwawo. Iye amamvetsa kwambiri ululu umene atumiki ake akumva. Mwachifundo chake, amakumbukira masautso awo ndi misozi yawo yonse, ngati kuti akuisunga m’nsupa.