Kodi Akufa Adzakhalanso ndi Moyo?
Zimene Tikuphunzira kwa Yesu
Kodi Akufa Adzakhalanso ndi Moyo?
Yesu anaukitsa anthu atatu, ndipo izi zinasonyeza kuti akufa adzauka. (Luka 7:11-17; 8:49-56; Yohane 11:1-45) Kuti timvetse zimene zidzachitikire akufa, tifunika kudziwa kaye chimene chimachititsa imfa komanso mmene imfayo inayambira.
N’chifukwa Chiyani Timadwala ndi Kufa?
Nthawi zonse pamene Yesu anakhululukira anthu machimo awo, anthuwo ankachira. Mwachitsanzo, atapemphedwa kuti achiritse munthu wakufa ziwalo, Yesu anati: “‘Chapafupi n’chiti, kunena kuti, Machimo ako akhululukidwa, kapena kunena kuti, Nyamuka uyende? Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali ndi mphamvu padziko lapansi zokhululukira machimo—’ pamenepo anauza wakufa ziwalo uja kuti: ‘Nyamuka, tenga kama wakoyu, uzipita kwanu.’” (Mateyo 9:2-6) Choncho uchimo ndi umene umatichititsa kuti tizidwala ndiponso kufa. Panopa tonse ndife ochimwa chifukwa tinatengera uchimo kwa munthu woyamba Adamu.—Luka 3:38; Aroma 5:12.
N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa?
Yesu sanachimwe moyo wake wonse. Choncho iye sanayenere kufa. Koma iye potifera ife, analipira ngongole ya machimo athu. Yesu ananena kuti magazi ake “adzakhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri kuti machimo [awo] akhululukidwe.”—Mateyo 26:28.
Yesu ananenanso kuti: “Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyo 20:28) Yesu anatchula malipiro amene anapereka kuti “dipo” chifukwa anawombola anthu ambiri ku imfa. Iye ananenanso kuti: “Ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, inde kuti akhale nawo wochuluka.” (Yohane 10:10) Choncho, kuti timvetse bwinobwino zimene zidzachitikire akufa, tiyenera kudziwa kaye zimene zimachitika munthu akafa.
Kodi N’chiyani Chimachitika Munthu Akafa?
Lazaro atafa, Yesu anafotokoza chimene chimachitika munthu akafa ndipo anauza ophunzira ake kuti: “‘Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula, koma ndikupita [ku Betaniya] kukam’dzutsa ku tulo take.’ . . . Iwo anaganiza kuti anali kunena za kugona tulo teniteni. Choncho, Yesu tsopano anawauza mosapita m’mbali kuti: ‘Lazaro wamwalira.’” Motero, Yesu anasonyeza kuti akufa ali mtulo, sadziwa kanthu.—Yohane 11:1-14.
Pamene Yesu anaukitsa bwenzi lake Lazaro, n’kuti patapita masiku anayi kuchokera nthawi yomwe anafa. Baibulo silinena kuti Lazaro anafotokoza mmene zinthu zinalili masiku anayi amenewo. Iye atafa sanadziwe chilichonse chifukwa anali ngati munthu amene ali mtulo.—Mlaliki 9:5, 10; Yohane 11:17-44.
Kodi Akufa Adzakhalanso ndi Moyo?
Akufa adzaukitsidwa ndipo adzakhala ndi moyo kosatha. Yesu anati: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu ake [a Yesu] ndipo adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29.
Kuuka kwa akufa ndi umboni wakuti Mulungu amatikonda. Yesu anati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16; Chivumbulutso 21:4, 5.
Kuti mumve zambiri, onani mutu 6 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? *
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 15 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.