Kodi Mukumanga Pamchenga Kapena Pathanthwe?
Kodi Mukumanga Pamchenga Kapena Pathanthwe?
KODI mumakonda kuwerenga Baibulo? Kodi mumapatula nthawi yophunzira Baibulo mokhazikika ndi Mboni za Yehova? Ngati ndi choncho, mwina mwaona kuti zimene mwaphunzira zakuthandizani kumvetsa chifukwa chake padzikoli pali mavuto ochuluka. (Chivumbulutso 12:9, 12) Ndiponso mwina, mavesi ambiri a m’Baibulo akulimbikitsani panthawi yamavuto komanso kukupatsani chiyembekezo.—Salmo 145:14; 147:3; 2 Petulo 3:13.
Kudziwa Baibulo molondola ndi chinthu chofunika kwambiri kwa anthu amene akufuna kukhala otsatira a Khristu. Koma chofunika si chokhacho. Kuti wophunzira Baibulo akhale Mkhristu weniweni, makamaka pamene akukumana ndi mayesero, ayenera kuchita chinthu chinanso chofunika kwambiri. Kuti tidziwe chinthucho, tiyeni tione mwachidule ulaliki wa paphiri umene Yesu anapereka ku Galileya.—Mateyo 5:1, 2.
Nyumba Ziwiri Ziyesedwa
Kodi mukudziwa zimene Yesu ananena mu ulaliki wa paphiri? Ulaliki wodziwika umenewu mungaupeze m’Mauthenga Abwino a Mateyo ndi Luka. (Mateyo 5:1–7:29; Luka 6:20-49) Ungakutengereni mphindi 20 zokha kuti muuwerenge. Komatu muulaliki umenewu, Yesu anagwira mawu Malemba Achiheberi maulendo 20 komanso uli ndi mafanizo oposa 50. Fanizo limodzi, lonena za nyumba ziwiri limene Yesu analinena kumapeto kwa ulaliki wake ndi losaiwalika. Mutamvetsa mfundo ya m’fanizoli, mungathandizidwe kudziwa mmene mungakhalirebe wolimba monga wotsatira wa Khristu, kaya mukumane ndi mayesero otani.
Yesu anati: “Aliyense wakumva mawu angawa ndi kuwachita adzafanizidwa ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe. Ndipo kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinafika ndi kuwomba nyumbayo, koma sinagwe chifukwa chakuti inakhazikika pathanthwepo. Koma aliyense wakumva mawu angawa ndi kusawachita adzafanizidwa ndi munthu wopusa, amene anamanga nyumba yake pamchenga. Ndipo kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinafika ndi kuwomba nyumbayo kotero kuti inagwa, ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.”—Mateyo 7:24-27.
Munthu “Amene Anakumba Mozama Kwambiri”
Kodi ndi mfundo yofunika iti imene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake m’fanizo la anthu awiri omanga nyumba? Kuti mudziwe mfundoyo, werengani bwinobwino zimene Yesu ananena pa lembali. Onani kuti nyumba ziwiri zonsezo zinakumana ndi tsoka lofanana. N’kutheka kuti nyumbazo zinali zofanana, zinali dera limodzi ndiponso mwina zinali zoyandikana. Komabe, ina inamangidwa pamchenga ndipo ina pathanthwe. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Malinga ndi Uthenga Wabwino wa Luka, munthu wochenjerayu “anakumba mozama kwambiri” kuti apeze thanthwe. (Luka 6:48) N’chifukwa chake nyumba yake inali yolimba.
Kodi Yesu anafuna kuti anthu aphunzire mfundo yotani? Iye anafuna kuti anthu adziwe zimene omangawo anachita, osati maonekedwe a Luka 6:46-48.
nyumbazo, dera lake kapena kukula kwa tsokalo. Munthu wina anakumba mozama pamene winayo sanatero. Kodi mungatani kuti mufanane ndi munthu wochenjerayo amene anakumba mozama? Yesu anafotokoza mwachidule mfundo ya fanizoli ponena kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani mumandiitana kuti ‘Ambuye! Ambuye!’ koma osachita zimene ndimanena? Aliyense wobwera kwa ine, ndi kumva mawu anga, ndi kuwachita, ndikuuzani amene amafanana naye: Iyeyo ali ngati munthu . . . amene anakumba mozama kwambiri ndi kuyala maziko pathanthwe.”—Kunena zoona, kungomvetsera zimene Baibulo limaphunzitsa kapena kuwerenga Baibulo mwamwambo chabe kuli ngati kumanga nyumba pamchenga, popanda kukumba. Koma kuchita kapena kutsatira zimene Khristu anaphunzitsa n’kovuta. Pamafunika kukumba mozama kwambiri kuti mupeze thanthwe.
Choncho, kuti mukhalebe wolimba monga wotsatira Khristu, zikudalira kutsatira zimene mukumva. Mukamatsatira zimene mukuphunzira m’Baibulo pamoyo wanu, mumafanana ndi munthu wochenjera amene anakumba mozama kwambiri. Choncho, wophunzira Baibulo aliyense ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndine wongomva, kapena ndine wochita? Kodi ndimangowerenga ndi kuphunzira Baibulo mwamwambo chabe, kapena ndimatsatira malamulo a m’Baibulo posankha zochita?’
Phindu Lokumba Mozama Kwambiri
Taganizirani chitsanzo cha José. Ngakhale kuti makolo ake anamuphunzitsa kulemekeza mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino, iye sankaphunzira Mawu a Mulungu payekha. Iye anati: “Nditachoka panyumba, ndinkayesetsa kukhala munthu wabwino, koma anzanga amene ndinkacheza nawo anali amakhalidwe oipa. Ndinayamba mankhwala osokoneza bongo, chiwerewere, ndiponso ndinkakonda kuchita ndewu.”
Patapita nthawi, José anaganiza zosintha khalidwe lake ndipo anayamba kuphunzira Baibulo mwakhama. Iye anati: “Chinthu chimodzi chomwe chinandilimbikitsa kuti ndisinthe, ndicho kuwerenga ndiponso kusinkhasinkha ulaliki wa Yesu wa paphiri. Koma zinanditengera nthawi kuti ndisinthe umunthu wanga ndiponso kuti ndisiye khalidwe langa loipa. Poyamba, ndinkaopa kuti anzanga azindinyoza. Koma kenako manthawo anatha. Ndinasiya kunama ndi kutukwana ndipo ndinayamba kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova. Mogwirizana ndi mawu a Yesu, ndinaona kuti kusafuna zambiri pamoyo ndiponso kutsatira mfundo za m’Baibulo kumabweretsadi chimwemwe chenicheni.”—Mateyo 5:3-12.
Kodi chingachitike n’chiyani ngati mwakumba mozama kwambiri ndi kumanga pathanthwe, kapena kuti kuyesetsa kutsatira zimene mumawerenga m’Mawu a Mulungu? Yesu anati: “Pamene mtsinje unasefukira, madzi anawomba nyumbayo, koma sanathe kuigwedeza, chifukwa Luka 6:48) Ndithudi, ngati mwamanga bwino mwa kutsatira zimene mukuphunzira, mayesero okhala ngati chimphepo adzalephera kugwetsa nyumba yanu, ngakhale kuigwedeza. Zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri.
anaimanga bwino.” (Wophunzira Yakobe, m’bale wake wa Yesu, anatchulanso phindu lina limene ophunzira Baibulo amene samangomva koma amachitadi zimene Mawu a Mulungu amanena, amapeza. Yakobe analemba kuti: “Khalani ochita zimene mawu amanena, osati ongomva chabe. . . . [Munthu] woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro laufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala polichita chifukwa chakuti sali wongomva n’kuiwala, koma wochita.”—Yakobe 1:22-25.
N’zoonadi kuti amene amatsatira mfundo za m’Baibulo amakhaladi achimwemwe. Chifukwa cha chimwemwe chimenechi, otsatira a Khristu amakhala ndi mphamvu yopirira mayesero angati chimphepo amene amayesa chikhulupiriro chawo ndiponso kudzipereka kwawo kwa Mulungu.
Kodi Inuyo Mutani?
Paulaliki wa paphiri, Yesu anatsindika fundo yakuti ngati munthu akufuna kutumikira Yehova Mulungu ayenera kusankha chinthu chimodzi, osati kuphatikiza. Mwachitsanzo, Yesu anaphunzitsa kuti munthu ayenera kusankha kukhala ndi diso lolunjika chimodzi kapena loipa, kukhala kapolo wa Mulungu kapena wa chuma, komanso kuyenda pamsewu wopanikiza kapena waukulu ndi wotakasuka. (Mateyo 6:22-24; 7:13, 14) Kenako, m’fanizo lake la anthu awiri omanga nyumba, Yesu anapatsanso otsatira ake mwayi wosankha chinthu chimodzi, kaya kuchita zinthu ngati munthu wochenjera uja kapena wopusa.
Ngati mukupitirizabe kutsatira ndi mtima wonse zimene mukuphunzira m’Baibulo, ndiye kuti mukuchita zinthu ngati munthu wochenjera. Inde, mukamakumba mozama kwambiri ndi kumanga pathanthwe, mungapeze madalitso panopa komanso m’tsogolo.—Miyambo 10:25.
[Zithunzi patsamba 30]
Tikamachita zimene tikuphunzira timakhala olimba pokumana ndi mayesero