Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyamba ndi Kutha kwa “Zombo zaku Tarisi”

Kuyamba ndi Kutha kwa “Zombo zaku Tarisi”

Kuyamba ndi Kutha kwa “Zombo zaku Tarisi”

“Zombo za ku Tarisi zinadutsa nyanja ndi malonda ako.”​—EZEKIELI 27:25, THE JERUSALEM BIBLE

ZOMBO za ku Tarisi zinathandiza Mfumu Solomo kukhala ndi chuma chambiri. Anthu amene ankapanga zombozi anathandiza kupanga alifabeti ya Chigiriki ndi Chiroma. Komanso iwo anakhazikitsa mzinda wa Byblos, mawu amene kunachokera dzina la buku lotchuka kwambiri kuposa lililonse.

Kodi ndani amene ankapanga ndi kuyendetsa zombo za ku Tarisi? Kodi dzina lakuti zombo za ku Tarisi linabwera bwanji? Kodi nkhani zokhudza anthu amenewa ndi zombo zawo zimasonyeza bwanji kuti Baibulo ndi lolondola?

Eni Nyanja ya Mediterranean

Afoinike ndiwo ankapanga zombo zomwe zinayamba kudziwika kuti zombo za ku Tarisi. Zaka pafupifupi 1,000 Khristu asanabwere, Afoinike anali kale akatswiri apanyanja. Iwo ankakhala m’kachigawo kam’mphepete mwa nyanja kumene panopa ndi ku Lebanon. Mitundu ina inkakhala kumpoto, kum’mawa ndi kum’mwera kwa derali ndipo kumadzulo kunali nyanja yaikulu ya Mediterranean. Afoinike ankadalira nyanjayo kuti apeze chuma.

M’kupita kwa nthawi, Afoinike apanyanja anapanga zombo zamalonda zolimba. Atayamba kupindula kwambiri ndi malonda awo ndiponso luso la zopangapanga litapita patsogolo, iwo anapanganso zombo zikuluzikulu zoyenda mtunda wautali. Atafika ku Kupuro, Sardinia ndi ku zilumba za Balearic, Afoinikewo anatsatira gombe la kumpoto kwa Africa kulowera kumadzulo mpaka kukafika ku Spain. (Onani mapu.)

Afoinike amene ankapanga zombo anayambanso kupanga zombo zazitali mamita 30. Zombo zapanyanja zimenezi zikuoneka kuti zinkatchedwa “zombo za ku Tarisi” chifukwa zinkatha kuyenda mtunda wa makilomita 4,000 kuchokera ku Foinike kupita kum’mwera kwa Spain, komwe mwina kunali ku Tarisi. *

N’kutheka kuti cholinga cha Afoinike sichinali kulamulira dziko, koma kupanga ndalama basi. Kuti akwaniritse cholinga chimenechi, iwo anakhazikitsa misika yambirimbiri. Choncho pankhani ya malonda, Afoinike anali eni nyanja ya Mediterranean.

Anapitirira Nyanja ya Mediterranean

Pofuna kupeza ndalama zambiri, Afoinike oona malo anapitirira ulendo wawo mpaka kukafika ku nyanja ya Atlantic. Zombo zawo zinayendabe, kulambalala gombe la kum’mwera kwa Spain mpaka zinakafika m’dera lotchedwa Tartessus. Pofika m’chaka cha 1100 B.C.E., iwo anakhazikitsa mzinda umene anautchula kuti Gadir. Panopa mzindawo womwenso ndi doko umadziwika kuti Cádiz, ndipo uli ku Spain. Mzinda wa Cádiz unadzakhala umodzi mwa mizinda yaikulu yoyambirira kumadzulo kwa Ulaya.

Afoinike ankagulitsa malonda a mchere, vinyo, nsomba zouma, mitengo yamkungudza ndi paini, zitsulo, magalasi, zolukaluka ndi zosemasema, nsalu za bafuta ndiponso nsalu zathonje lofiirira za ku Turo. Kodi dziko la Spain linkawapatsa chiyani Afoinikewo?

Dera la kum’mwera kwa Spain kunkapezeka siliva wambiri ndi miyala ina ya mtengo wapatali kuposa madera ena a ku Mediterranean. Ponena za Turo, lomwe linali doko lalikulu la Afoinike, mneneri Ezekieli anati: “Unkachita malonda ku Spain ndipo unkatengako siliva, chitsulo, tini ndi mtovu, mosinthana ndi katundu wako.”​—Ezekiel 27:12, Today’s English Version.

Afoinike anapeza migodi yambiri ya miyala imeneyi kufupi ndi mtsinje wa Guadalquivir, m’dera la Cádiz. Miyala imeneyi imakumbidwabe mpaka pano m’derali, lomwe tsopano limatchedwa kuti Río Tinto. Migodi imeneyi yakhala ikutulutsa miyala yabwino kwambiri kwa zaka pafupifupi 3,000.

Anthu a ku Spain ndi Afoinike anakhazikitsa malo opangirako zombo zonyamula katundu, ndipo zimenezi zinapangitsa kuti Afoinikewo akhale ndi ulamuliro waukulu pa siliva wa ku Spain. Chifukwa cha zimenezi, siliva wambiri ankapita ku Foinike, komanso dziko loyandikana nalo la Isiraeli. Ndipo kenako Mfumu Solomo ya Isiraeli inapanga mgwirizano wa zamalonda ndi mfumu Hiramu ya ku Foinike. Zotsatira zake zinali zakuti m’masiku a Solomo, siliva anayesedwa “opanda pake.”​—1 Mafumu 10:21. *

Ngakhale kuti Afoinike anatsogola pa zamalonda, iwo ankachitanso zankhanza. Akuti nthawi zina ankakopa anthu kuti akwere zombo ponamizira kuwasonyeza malonda awo koma ali ndi cholinga chowagwira ukapolo. M’kupita kwa nthawi, anatembenukira Aisiraeli ngakhale kuti anali anzawo ochita nawo malonda n’kuyamba kuwagulitsa kuukapolo. Chifukwa cha zimenezi aneneri achiheberi analosera za kuwonongedwa kwa mzinda wa Afoinike wa Turo. Maulosi amenewa anakwaniritsidwa ndi Alesandro Wamkulu mu 332 B.C.E. (Yoweli 3:6; Amosi 1:9, 10) Kuwonongedwa kwa mzindawu ndiye kunali kutha kwa Afoinike.

Zimene Afoinike Anasiya

Mofanana ndi anthu onse odziwa bwino malonda, Afoinike ankalemba mapangano azamalonda. Komanso iwo ankagwiritsa ntchito alifabeti yofanana ndi alifabeti ya Chiheberi chakale. Mitundu ina itaona ubwino wa alifabeti ya Afoinike, anaisintha mwina ndi mwina n’kupanga alifabeti ya Chigiriki. Ndipo alifabeti ya Chigirikiyo anaigwiritsa ntchito popanga alifabeti ya Chiroma, imene ndi imodzi mwa maalifabeti amene amagwiritsidwa ntchito m’madera ambiri masiku ano.

Mzinda wa Afoinike wa Byblos unali wofunika kwambiri. M’mzindawu munkapezeka gumbwa wochuluka ndiponso n’kumene kunayambira luso lopanga mapepala amene timagwiritsira ntchito masiku ano. Kulemba pa gumbwa kunathandiza kuti mabuku ambiri alembedwe. Komanso dzina la buku limene anthu ambiri ali nalo loti Baibulo, linachokera ku dzina la mzindawu lakuti Byblos. Choncho, zolemba zokhudza mbiri ya Afoinike ndi zombo zawo zimatitsimikizira kuti Baibulo ndi lolondola ndiponso lodalirika.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 M’kupita kwa nthawi, mawu akuti “zombo za ku Tarisi” ankatanthauza mtundu wa zombo zotha kuyenda ulendo wautali panyanja.

^ ndime 15 “Zombo za ku Tarisi” za Solomo zinkagwira ntchito pamodzi ndi za Hiramu, ndipo mwina zinkachita malonda kunja kwa dera lotchedwa Ezioni Geberi ndiponso zinkafika ku Nyanja Yofiira ndi madera ena akutali.​—1 Mafumu 10:22.

[Mapu patsamba 27]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

NJIRA ZIMENE AFOINIKE ANKADUTSA

SPAIN

TARTESSUS

Mtsinje wa Guadalquivir

Gadir

Corsica

Zilumba za Balearic

Sardinia

Sisile

Kerete

Kupuro

Byblos

Turo

NYANJA YA MEDITERRANEAN

Ezioni Geberi

Nyanja Yofiira

AFRICA

[Chithunzi patsamba 27]

Ndalama yosonyeza chombo cha Afoinike, m’zaka za m’ma 200 ndi 300 B.C.E.

[Chithunzi patsamba 27]

Mabwinja a mzinda wa Afoinike ku Cádiz, Spain

Mawu a Chithunzi patsamba 26

Museo Naval, Madrid

[Mawu a Chithunzi patsamba 27]

Coin: Museo Arqueológico Municipal. Puerto de Sta. María, Cádiz; remains: Yacimiento Arqueológico de Doña Blanca, Pto. de Sta. María, Cádiz, España