Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupirira Chipangano Chakale?
Zimene Owerenga Amafunsa
Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupirira Chipangano Chakale?
Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu ndipo zimaona Chipangano Chakale ndiponso Chipangano Chatsopano kuti ndi mbali zofunika kwambiri za Baibulo. Komabe, iwo amagwiritsa ntchito mayina ake oyenerera akuti “Malemba Achihebri” ndiponso “Malemba Achigiriki Achikristu.” Amachita zimenezi chifukwa Chiheberi ndi Chigiriki ndi zilankhulo zazikulu zoyambirira zimene zinagwiritsidwa ntchito polemba Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano.
Komabe, anthu ena omwe amati ndi Akhristu sakhulupirira Chipangano Chakale. Iwo amanena kuti Malemba amenewa amasonyeza kuti Mulungu ndi wankhanza, amene ankavomereza nkhondo, kuphana komanso makhalidwe ena oipa, zomwe ndi zosiyana kwambiri ndi zimene zili ku Chipangano Chatsopano komwe Mulungu amasonyezedwa kuti ndi wamakhalidwe abwino komanso wachikondi. Ndipo ena amanena kuti popeza Chipangano Chakale chimafotokoza kwambiri za chipembedzo cha Ayuda, ndiye kuti si chofunika kwa Akhristu. Komabe, malinga ndi lamulo la Mulungu lopezeka pa Deuteronomo 12:32, loletsa kuwonjezera kapena kuchotsa kalikonse pa mawu ake, kodi zimenezi ndi zifukwa zomveka zokanira mbali yaikulu ya Baibulo imeneyi?
Panthawi ina mu 50 C.E. pamene mtumwi Paulo anakachezera anthu a ku Tesalonika, ku Girisi, “anakambirana nawo kuchokera m’Malemba. Iye anafotokoza ndi kusonyeza umboni wolembedwa powatsimikizira kuti kunali koyenera kuti Khristu avutike ndi kuuka kwa akufa.” (Machitidwe 17:1-3) Anthu ena omwe ankamumvetsera anakhala Akhristu, ndipo patapita nthawi Paulo anawayamikira kuti: “Pamene munalandira mawu a Mulungu amene munamva kwa ife, simunawalandire monga mawu a anthu ayi, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu.” (1 Atesalonika 2:13) Panthawi imene ankachezera anthu amenewa, zikuoneka kuti Uthenga Wabwino wa Mateyo wokha ndi umene unali utalembedwa pa mabuku onse 27 a Malemba Achigiriki Achikristu. Motero, n’zosakayikitsa kuti “Malemba” amene Paulo anagwiritsa ntchito ‘posonyeza umboni wolembedwa’ anali ochokera m’Malemba Achiheberi.
Ndipotu olemba Malemba Achigiriki Achikristu analemba ndendende mawu a m’Malemba Achiheberi nthawi zokwana 320 ndipo anagwira mawu ena m’Malemba amenewa nthawi mazana angapo. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? “Pakuti zonse zimene zinalembedweratu zinalembedwa kuti zitilangize ife, kuti mwa chipiriro chathu ndi mwa chitonthozo cha m’Malemba tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Zimenezi zikusonyeza kuti anthu amene amakhulupirira Baibulo lonse, amapindula kwambiri.
Malemba Achigiriki Achikristu amapitiriza kufotokoza momveka bwino Mawu a Mulungu ndiponso kukwaniritsidwa kwa zolinga zake pogwiritsa ntchito zimene zili m’Malemba Achiheberi. Malemba amenewa sapangitsa Malemba Achiheberi kukhala osafunika. Ndipo katswiri wina wa maphunziro a zaumulungu pa Cambridge University dzina lake Herbert H. Farmer, anati, “kuti timvetse Mauthenga Abwino tiyenera kuganiziranso moyo wa anthu amene ankatsatira pangano la Chilamulo omwe mbiri yawo inalembedwa m’Chipangano Chakale.”
Mawu a Mulungu sayenera kusinthidwa. Komabe, “mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.” (Miyambo 4:18) Mwa kuwonjezera Malemba Achigiriki Achikristu m’Baibulo, Mulungu anaunika mmene cholinga chake chidzakwaniritsidwire popanda kupangitsa Malemba Achiheberi kukhala osafunika. Malemba onsewa ndi mbali ya “mawu a Yehova [amene] amakhala kosatha.”—1 Petulo 1:24, 25.