Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kusala Kudya Kumathandiza Munthu Kuyandikira kwa Mulungu?

Kodi Kusala Kudya Kumathandiza Munthu Kuyandikira kwa Mulungu?

Kodi Kusala Kudya Kumathandiza Munthu Kuyandikira kwa Mulungu?

‘Kusala kudya kumathandiza munthu kuganizira kwambiri za ubwenzi wake ndi Mulungu ndipo kumam’kumbutsa mfundo yakuti zinthu zakuthupi sizofunikira kwambiri pamoyo.’​—ANATERO MAYI WINA WACHIKATOLIKA.

‘Kusala kudya kumathandiza munthu kuti akhale paubwenzi ndi MULUNGU.’​—ANATERO RABI WINA WACHIYUDA.

‘M’chipembedzo chathu timakhulupirira kuti kusala kudya ndi lamulo, ndiponso ndi chizindikiro chosonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu komanso chosonyeza kuti tikumuthokoza. Ndimasala kudya chifukwa ndimakonda Mulungu.’​—ANATERO MAYI WINA WACHIPEMBEDZO CHA CHIBAHAYI.

ANTHU a m’zipembedzo zambiri monga Chibuda, Chihindu, Chisilamu, Chijaini ndiponso Chiyuda amasala kudya. Anthu ambiri amakhulupilira kuti kusala kudya kumathandiza munthu kuyandikira kwa Mulungu.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi muyenera kusala kudya? Kodi Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, limati chiyani pankhaniyi?

N’chifukwa Chiyani Anthu Ena Ankasala Kudya?

M’nthawi za m’Baibulo, anthu ankasala kudya pazifukwa zosiyanasiyana zovomerezeka ndi Mulungu. Ena ankasala pofuna kusonyeza kuti akumva chisoni kwambiri kapena posonyeza kulapa machimo awo. (1 Samueli 7:4-6) Ankasalanso pochonderera Mulungu kuti awathandize ndiponso kuti awatsogolere. Ndiponso ankasala kudya kuti asamadodometsedwe ndi zinthu zina akamasinkhasinkha.​—Oweruza 20:26-28; Luka 2:36, 37; Mateyo 4:1, 2.

Komabe Baibulo limanenanso za kusala kudya kwina kosavomerezeka ndi Mulungu. Mwachitsanzo, panthawi ina Mfumu Sauli anasala kudya asanapite kwa sing’anga. (Levitiko 20:6; 1 Samueli 28:20) Anthu enanso oipa monga Yezebeli ndiponso anthu amene ankafuna kupha mtumwi Paulo, ankasala kudya. (1 Mafumu 21:7-12; Machitidwe 23:12-14) Afarisi nawonso anali odziwika bwino pa nkhani ya kusala kudya. (Maliko 2:18) Komabe, sikuti Mulungu ankasangalala nawo ndipo n’chifukwa Yesu anawadzudzula. (Mateyo 6:16; Luka 18:12) Ndiponso Yehova sanasangalale ndi Aisiraeli omwe ankasala kudya chifukwa iwo anali ndi khalidwe ndiponso maganizo olakwika.​—Yeremiya 14:12.

Zitsanzo zimenezi zikusonyeza kuti kusala kudya pakokha sikusangalatsa Mulungu. Komabe, Mulungu anasangalala ndi atumiki ake ambiri okhulupirika omwe ankasala kudya. Ndiyeno, kodi Akhristu ayenera kusala kudya?

Kodi Pali Lamulo Loti Akhristu Azisala Kudya?

M’chilamulo cha Mose, Ayuda analamulidwa kuti ‘azizunza moyo wawo,’ kutanthauza kuti azisala kudya kamodzi pachaka, pa Tsiku la Chitetezo. (Levitiko 16:29-31; Salmo 35:13) Iyi inali nthawi yokhayo imene Yehova analamula anthu kuti azisala kudya. * Ayuda amene ankatsatira Chilamulo cha Mose, ankafunika kumvera lamulo limeneli. Koma Akhristu safunika kutsatira Chilamulo cha Mose.​—Aroma 10:4; Akolose 2:14.

Ngakhale kuti Yesu nthawi zina ankasala kudya mogwirizana ndi Chilamulo, iye sankadziwika monga munthu wokonda kusala kudya. Iye anauza otsatira ake zimene angachite akamasala kudya, koma sanawalamulire kuti azisala kudya. (Mateyo 6:16-18; 9:14) Nanga n’chifukwa chiyani Yesu anauza otsatira ake kuti adzasala kudya pambuyo pa imfa yake? (Mateyo 9:15) Apa, sikuti ankapereka lamulo. Koma Yesu ankasonyeza kuti iye akadzaphedwa, ophunzira ake adzakhala ndi chisoni kwambiri moti sadzakhala ndi chikhumbo chofuna kudya.

Nkhani ziwiri za m’Baibulo zonena za Akhristu oyambirira zimasonyeza kuti Mulungu amasangalala munthu akamasala kudya ali ndi zolinga zabwino. (Machitidwe 13:2, 3; 14:23) * Choncho, palibe lamulo lakuti Akhristu azisala kudya. Komabe munthu amene wasankha kusala kudya ayenera kusamala ndi mavuto ena amene angabwere chifukwa cha kusala kudyako.

Samalani ndi Kusala Kudya

Chinthu choyamba chimene tiyenera kupewa pankhani ya kusala kudya ndicho mtima wodzionetsa kuti ndife olungama. Baibulo limatichenjeza kuti sitiyenera ‘kudzichepetsa mwachinyengo.’ (Akolose 2:20-23) Fanizo la Yesu lonena za Mfarisi wonyada ndiponso wodziona kuti ndi woposa ena chifukwa chakuti iye ankasala kudya kawirikawiri, limasonyeza kuti Mulungu sasangalala ndi khalidwe limeneli.​—Luka 18:9-14.

Chinthu chinanso chimene tiyenera kupewa ndicho kuchita kulengeza kuti tikusala, kapenanso kusala chifukwa choti munthu wina watiuza. Pa Mateyo 6:16-18, Yesu analangiza kuti munthu akamasala kudya sayenera kulengeza kwa anthu ena, koma izikhala nkhani ya pakati pa iyeyo ndi Mulungu.

Tisamaganize kuti munthu angakhululukidwe machimo ake chifukwa cha kusala kudya. Mulungu angasangalale ndi munthu amene akusala kudya, ngati munthuyo amatsatira malamulo ake. (Yesaya 58:3-7) Iye amakhululukira anthu amene alapa ndi mtima wonse, osati chifukwa chakuti akusala kudya. (Yoweli 2:12, 13) Baibulo limasonyeza kuti Yehova amatikhululukira machimo chifukwa cha kukoma mtima kwake kwa m’chisomo kumene anakusonyeza kudzera mu nsembe ya Khristu. N’zosatheka kuti Mulungu atikhululukire machimo chifukwa cha zimene timachita zokha, kuphatikizapo kusala kudya.​—Aroma 3:24, 27, 28; Agalatiya 2:16; Aefeso 2:8, 9.

Lemba la Yesaya 58:3 likusonyeza chinthu chinanso cholakwika. Aisiraeli ankaganiza kuti Mulungu awachitira zinazake chifukwa choti akusala kudya. Ndiponso iwo ankaganiza kuti akamasala kudya ndiye kuti akuthandiza Mulungu. N’chifukwa chake iwo anafunsa Mulungu kuti: “Bwanji ife tasala kudya, ndipo Inu simuona? ndi bwanji ife tavutitsa moyo wathu, ndipo Inu simusamalira?” Masiku anonso, anthu ambiri amaganiza kuti Mulungu angawadalitse akamasala kudya. Choncho, tisatsatire khalidwe lopanda ulemu ndiponso losagwirizana ndi Malemba limeneli.

Anthu ena amakhulupirira kuti Mulungu akhoza kuwayanja chifukwa chozunza thupi lawo monga kusala kudya ndiponso kudzikwapula. Koma Mawu a Mulungu amatsutsa maganizo amenewa, ndipo amasonyeza kuti ‘kuzunza thupi n’kosathandiza polimbana’ ndi zilakolako za thupilo.​—Akolose 2:20-23.

Khalani ndi Maganizo Oyenera

Kusala kudya si lamulo komanso sikolakwika. Nthawi zina kusala kudya kungakhale koyenera ngati munthu atapewa zinthu zolakwika zimene tafotokoza kalezi. Komabe, kusala kudya sikofunika kuti Mulungu avomereza kulambira kwathu. Yehova ndi “Mulungu wa chisangalalo” ndipo amafuna kuti atumiki ake azisangalala. (1 Timoteyo 1:11) Mawu ake amati: “Iwo alibe ubwino koma . . . kuti munthu yense adye namwe nawone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.”​—Mlaliki 3:12, 13.

Tiyenera kukhala osangalala polambira Mulungu ndipo Baibulo silisonyeza kuti anthu amakhala achimwemwe chifukwa cha kusala kudya. Komanso, ngati thanzi lathu likufooka chifukwa cha kusala kudya kapena ngati mphamvu zimene tikanazigwiritsira ntchito polengeza Ufumu wa Mulungu zikutha chifukwa cha kusala kudya, ndiye kuti kusala kudyako n’kosayenera.

Ngati ife tasankha kusala kudya kapena ayi, tisaweruze ena. Akhristu oona sayenera kusemphana maganizo pankhani imeneyi, “pakuti ufumu wa Mulungu si kudya ndi kumwa ayi, koma chilungamo ndi mtendere ndi chimwemwe mwa mzimu woyera.”​—Aroma 14:17.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Estere anasala kudya Phwando la Purimu lisanachitike. Ngakhale kuti Mulungu sanamulamule kuti achite zimenezi, zikuoneka kuti iye anasangalala naye.

^ ndime 14 M’mabaibulo ena muli nkhani zina zokhuza kusala kudya zomwe si zoona, ndipo nkhani zimenezi sizipezeka m’mipukutu yakale ya Chigiriki.​—Mateyo 17:21; Maliko 9:29; Machitidwe 10:30; 1 Akorinto 7:5, King James Version.

[Mawu Otsindika patsamba 28]

Afarisi ankadzichepetsa mwachinyengo akamasala kudya

[Mawu Otsindika patsamba 29]

“Ufumu wa Mulungu si kudya ndi kumwa ayi, koma chilungamo ndi mtendere ndi chimwemwe mwa mzimu woyera”

[Bokosi patsamba 29]

Kodi Akhristu Ayenera Kusala Kudya Pokonzekera Isitala?

Anthu ena amasala kudya kwa masiku 40 potsanzira Khristu amenenso anasala kudya kwa masiku 40. Koma Yesu sanalamule ophunzira ake kuti azichita zimenezi, ndipo palibe umboni wosonyeza kuti iwo ankasala kudya. Nkhani yoyamba yosonyeza kuti anthu ankasala kudya kwa masiku 40 pokonzekera Isitala, iyenera kuti inapezeka m’makalata a Athanasius a mu 330 C.E.

Zingaoneke ngati zodabwitsa kuona kuti anthu azipembedzo zina amasala kudya pokonzekera Isitala, pamene Yesu sanasale kudya atatsala pang’ono kuphedwa, koma atangobatizidwa kumene. Komabe, anthu akale a ku Babulo, Iguputo ndiponso Girisi ndi omwe ankasala kudya kwa masiku 40, cha kumayambiriro kwa chaka. Choncho, zipembedzo za Chikhristu zinatengera mwambowu kwa anthu amenewa.