Phunzitsani Ana Anu
Yoasi Anasiya Kutumikira Yehova Chifukwa Chocheza ndi Anthu Ochita Zoipa
INALI nthawi yovuta kwambiri ku Yerusalemu, mzinda umene kunali kachisi wa Mulungu. Panthawiyi, Mfumu Ahaziya anali atangophedwa kumene. Ndipo zimene Ataliya, yemwe anali mayi wake wa Ahaziya anachita zinali zovuta kumvetsa. Iye anapha zidzukulu zake, ana aamuna a Ahaziya. Kodi ukudziwa chifukwa chimene anachitira zimenezi?— * Iye anatero kuti akhale wolamulira m’malo mwa zidzukulu zakezo.
Komabe Yoasi, mmodzi mwa zidzukulu za Ataliya amene panthawiyi anali wakhanda, anapulumuka ndipo agogo akewo sanadziwe chilichonse. Kodi ukufuna kudziwa kuti anapulumuka bwanji?— Mwanayo anali ndi azakhali ake a Yoseba ndipo iwo anam’tenga n’kukamubisa mu kachisi wa Mulungu. Iwo anatha kukamubisa m’kachisi chifukwa amuna awo a Yehoyada anali mkulu wa ansembe. Choncho, awiriwa anaonetsetsa kuti mwanayo akutetezedwa.
Yoasi anabisidwa m’kachisi kwa zaka 6, ndipo ali m’kachisimo, anaphunzitsidwa mfundo zonse zokhudza Yehova Mulungu ndi malamulo Ake. Kenako Yoasi atafika zaka 7, Yehoyada anachita zinthu zoti Yoasi akhale mfumu. Kodi ungakonde kudziwa mmene Yehoyada anachitira zimenezi ndiponso zimene zinachitikira mfumukazi yoipa Ataliya, yomwe inali agogo ake a Yoasi?—
Yehoyada anaitanitsa mwamseri asilikali olondera mafumu a ku Yerusalemu. Ndipo iye anawafotokozera mmene iye ndi mkazi wake anapulumutsira Yoasi, mwana wa Mfumu Ahaziya. Kenako, Yehoyada anatenga Yoasi n’kumusonyeza kwa asilikaliwo, ndipo iwo anaona kuti iye ndi amene anali woyenera kukhala mfumu. Choncho, anakonza njira yoti amulonge ufumu.
Yehoyada anatulutsira Yoasi kunja, n’kumuveka korona wachifumu. Zitatero anthu anayamba ‘kuwomba m’manja, nati, Mfumu ikhale ndi moyo.’ Asilikali olondera mfumu aja anam’zungulira Yoasi pomuteteza. Koma Ataliya atamva anthu akufuula chifukwa cha chisangalalo, anathamanga kuti akawaletse. Ndipo Yehoyada analamula kuti Ataliya aphedwe, ndipo asilikaliwo anamuphadi.—2 Mafumu 11:1-16.
Kodi ukuganiza kuti Yoasi anapitiriza kumvera Yehoyada ndiponso kuchita zinthu zabwino?— Inde, koma iye ankachita zimenezi panthawi yokha imene Yehoyada anali ndi moyo. Ndipo Yoasi anaonetsetsa kuti anthu apereka ndalama zokonzera kachisi wa Mulungu yemwe ananyalanyazidwa ndi abambo ake a Ahaziya, komanso agogo ake a Yehoramu. Koma tiye tione zimene zinachitika Mkulu wa Ansembe, Yehoyada atamwalira.—Nthawiyi n’kuti Yoasi ali ndi zaka pafupifupi 40. M’malo mopitiriza kucheza ndi atumiki a Yehova, Yoasi anayamba kucheza ndi anthu olambira milungu yonyenga. Zekariya, mwana wa Yehoyada ndi amene anali wansembe wa Yehova panthawiyi. Kodi ukuganiza kuti Zekariya anatani atamva zinthu zoipa zimene Yoasi anali kuchita?—
Zekariya anauza Yoasi kuti: “Popeza mwasiya Yehova, Iye wasiyanso inu.” Yoasi anakwiya kwambiri atamva mawu amenewa, moti analamula kuti Zekariya aphedwe moponyedwa miyala. Tangoganiza, Yoasi anatetezedwa kuti asaphedwe koma kenako, iye anadzapha munthu.—2 Mbiri 24:1-3, 15-22.
Kodi tikuphunzira zotani m’nkhaniyi?— Tikuphunzira kuti sitiyenera kukhala ngati Ataliya, amene ankadana ndi anthu komanso kuwachitira nkhanza. M’malomwake, tiyenera kukonda Akhristu anzathu ngakhalenso adani athu ngati mmene Yesu anatiphunzitsira. (Mateyo 5:44; Yohane 13:34, 35) Ndiponso, kuti tizichita zabwino ngati mmene Yoasi anachitira poyamba, tiyenera kupitiriza kukondana ndi anthu amene amakonda Yehova ndiponso amene angatilimbikitse kumulambira.
^ ndime 3 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana wanu, mukapeza pamene pali mzere pakusonyeza kuti muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.