Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Amadziwa Zimene Sitingakwanitse

Amadziwa Zimene Sitingakwanitse

Yandikirani Mulungu

Amadziwa Zimene Sitingakwanitse

Levitiko 5:2-11

MAYI wina yemwe ankayesetsa kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu anati: “Ndinkayesetsa ndithu komabe ndinkaona kuti sindikukwanitsa.” Kodi Yehova Mulungu amafuna kuti atumiki ake asamalakwitse zinthu ngakhale pang’ono? Kodi iye amazindikira kuti pali zinthu zina zimene atumiki ake sangakwanitse? Kuti tiyankhe mafunso amenewa, choyamba tiyeni tione zimene Chilamulo cha Mose chinanena zokhudza kupereka nsembe, monga mmene lemba la Levitiko 5:2-11 limasonyezera.

M’Chilamulo cha Mose, anthu ankafunika kupereka nsembe zosiyanasiyana kwa Mulungu, kuti iye awakhululukire machimo awo. Malinga ndi zimene mavesiwa akusonyeza, nthawi zina munthu sankachimwa mwadala. (Vesi 2-4) Choncho munthuyo akazindikira kuti wachimwa, ankayenera kuulula tchimo lake n’kukapereka nsembe yopalamula yomwe inkakhala “msoti wa nkhosa, kapena msoti wa mbuzi.” (Vesi 5, 6) Komano kodi chinkachitika n’chiyani ngati munthuyo anali wosauka moti sakanakwanitsa kupereka nkhosa kapena mbuzi? Kodi Chilamulo chinkafuna kuti munthuyo akatenge ngongole n’cholinga choti apeze nyamayo? Kapena kodi anafunika kukayamba wagwira ntchito kuti apeze nyamayo, zomwe zikanachititsa kuti achedwe kupereka nsembeyo?

Posonyeza kuti Yehova ndi wachifundo kwambiri, Chilamulocho chinafotokoza kuti: “Chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, wochimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yake yopalamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri.” (Vesi 7) Mawu akuti “chikapanda kufikira,” angalembedwenso kuti “dzanja lake likapanda kufikira.” Choncho ngati munthu amene wachimwayo ndi wosauka kwambiri moti sangakwanitse kupereka nkhosa, Mulungu ankalandira nsembe imene munthuyo akanakwanitsa, yomwe ndi njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri.

Komano chinkachitika n’chiyani ngati munthuyo sakanakwanitsabe kupereka mbalame ziwirizo? Chilamulo chinafotokoza kuti: “Koma chuma chake chikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wochimwayo azidza nacho chopereka chake limodzi la magawo khumi la efa [makapu 8 kapena 9] la ufa wosalala, likhale la nsembe yauchimo.” (Vesi 11) Yehova ankalola kuti anthu osauka kwambiri azipereka nsembe ya uchimo yopanda magazi. * Motero ku Isiraeli, umphawi sichinali chinthu cholepheretsa munthu kupeza mwayi wokhululukidwa machimo ake kapena kukhala paubwenzi wabwino ndi Mulungu.

Ndiyeno kodi lamulo la nsembe za uchimo likutiphunzitsa chiyani za Yehova? Likutiphunzitsa kuti iye ndi Mulungu wachifundo kwambiri amene amazindikira zimene atumiki ake sangakwanitse. (Salmo 103:14) Iye amafuna kuti timuyandikire ndiponso tikhale naye paubwenzi ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto monga ukalamba, matenda, komanso mavuto amene amabwera posamalira banja ndi zina zotero. Tingasangalale kudziwa kuti Yehova Mulungu amasangalala tikamachita zinthu zimene tingakwanitse pomutumikira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Magazi, omwe Mulungu amawaona kuti ndi opatulika, ndi omwe ankathandiza kuti iye akhululukire munthu machimo ake. (Levitiko 17:11) Ndiyeno kodi zimenezi zikusonyeza kuti nsembe za ufa zimene anthu osauka ankapereka zinali zopanda ntchito? Ayi, chifukwa Yehova ankaona kuti anthu omwe ankapereka nsembe zotere ankasonyeza kudzichepetsa komanso kumvera. Ndiponso machimo a Aisiraeli onse, kuphatikizapo omwe anali osauka, ankakhululukidwa chifukwa cha magazi a nyama zomwe zinkaperekedwa nsembe kwa Mulungu chaka chilichonse pa Tsiku la Chitetezo.​—Levitiko 16:29, 30.