Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani anthu amanena kuti “ameni” pamapeto pa pemphero?

Mawu akuti “ameni,” anawamasulira kuchokera ku mawu a Chiheberi akuti ʼa·menʹ. Anthu amanena limodzi mawuwa pamapeto pa pemphero, akamaliza kulumbira ndiponso kudalitsa. Kwenikweni mawuwa amatanthauza kuti “zikhale choncho,” kapena “ndithu,” kusonyeza kuti munthu akutsimikizira ndiponso kugwirizana ndi zomwe zanenedwazo. Buku lina limanena kuti, “mawuwa amatanthauza kutsimikizira, kunena zoona komanso kusakayikira.” Kale munthu akamaliza kulumbira kapena kuchita pangano ankanena mawu akuti “ameni,” ndipo zimenezi zinkasonyeza kuti akuvomereza mwalamulo kuti adzachita zonse zimene walonjezazo. Komanso ankasonyeza kuti akuvomereza mavuto ena alionse omwe angabwere ngati iye sadzasunga panganolo.​—Deuteronomo 27:15-26.

Polalikira ndiponso pophunzitsa, Yesu ankayamba kutchula mfundo zina ndi mawu akuti “ameni.” Iye ankachita zimenezi pofuna kutsindika kuti zimene akufuna kunenazo n’zoona. Mawu achigiriki akuti a·menʹ akagwiritsidwa ntchito m’njira imeneyi, amawamasulira kuti “ndithu.” (Mateyo 5:18; 6:2, 5) Mawuwa akawatchula motsatizana, ngati m’mene Yesu anachitira mu uthenga wabwino wa Yohane, ndiye kuti amawamasulira kuti “ndithudi.” (Yohane 1:51) Anthu amati m’Baibulo lonse, ndi Yesu yekha amene anagwiritsa ntchito mawu akuti ameni m’njira imeneyi.

M’Malemba Achigiriki Achikhristu, Yesu amatchedwanso kuti “Ameni,” posonyeza kuti iye ndi mboni “yokhulupirika ndi yoona.”​—Chivumbulutso 3:14.

Kodi Urimu ndi Tumimu zinali chiyani?

Zikuoneka kuti Urimu ndi Tumimu zinali zinthu zimene Aisiraeli ankagwiritsa ntchito kuti adziwe zimene Yehova akufuna pankhani zokhudza mtunduwo kapena atsogoleri awo. Zinthu zimenezi zinkakhala ndi wansembe wamkulu ndipo iye ankazisunga m’thumba la “chapachifuwa cha chiweruzo.” (Eksodo 28:15, 16, 30) Malemba safotokoza mwatsatanetsatane zonse zokhudza mmene zinthu zimenezi zinkaonekera ndiponso mmene ankazigwiritsira ntchito. Komabe, Malemba angapo amasonyeza kuti zinthu zimenezi zinkagwiritsidwa ntchito pochita maere omwe yankho lake linkakhala “inde” kapena “ayi,” ndipo nthawi zina sankalandira yankho lililonse kuchokera kwa Mulungu.

Chitsanzo chimodzi cha mmene anagwiritsira ntchito Urimu ndi Tumimu, m’pamene Davide anauza Abiyatara kuti amubweretsere efodi, yemwe zikuoneka kuti anali wa mkulu wa ansembe wokhala ndi zinthuzi. Davide anafunsa Yehova mafunso awiri akuti: ‘Kodi Sauli anditsatiradi kuno?’ ‘Kodi amuna a ku Keila adzandiperekadi m’dzanja lake?’ Ndipo Yehova anamuyankha kuti zonsezi zidzachitikadi. Choncho zimenezi zinathandiza Davide kuchita zinthu mwanzeru.​—1 Samueli 23:6-12.

Panthawi ina zimenezi zisanachitike, Mfumu Sauli anagwiritsa ntchito Urimu ndi Tumimu pofuna kudziwa kuti wolakwa ndani, pakati pa iyeyo ndi mwana wake Yonatani, kapena Aisiraeli onse. Kenako anafunanso kudziwa yemwe anali wolakwa pakati pa iyeyo ndi mwana wakeyo. (1 Samueli 14:40-42) Koma Mulungu atasiya kukonda Sauli, anasiyanso kumupatsa malangizo kudzera ‘m’maloto, Urimu, kapena aneneri.’​—1 Samueli 28:6.

Koma zikuoneka kuti Ayuda anasiya kugwiritsa ntchito Urimu ndi Tumimu, kachisi wa Yehova atawonongedwa mu 607 B.C.E.

[Chithunzi patsamba 27]

Mawu akuti “ameni,” pa Chivumbulutso 3:14, mu mpukutu wa Alexandrinus, wa m’zaka za m’ma 400 C.E.