Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndikuthokoza Yehova Ngakhale Kuti Ndakumana ndi Mavuto Mmene Baibulo Linandithandizira Kupirira

Ndikuthokoza Yehova Ngakhale Kuti Ndakumana ndi Mavuto Mmene Baibulo Linandithandizira Kupirira

Ndikuthokoza Yehova Ngakhale Kuti Ndakumana ndi Mavuto Mmene Baibulo Linandithandizira Kupirira

Yosimbidwa Ndi Enrique Caravaca Acosta

Panali pa April 15, 1971 ndipo ndinali pa ulendo wopita kumudzi kwathu kukaona azibale anga, amene ankakhala pafamu yathu. Popeza kuti panadutsa nthawi ndithu ndisanapite kumudzi, ndinkafunitsitsa kuwaona. Koma ndili m’njira, ndinkakayikira ngati ndingakapeze anthu onse ali pakhomo komanso sindinkadziwa kuti munthu woyamba kuwonana naye akakhala ndani. Koma nditangofika, ndinachita nthumanzi kwambiri nditapeza kuti anthu anayi, kuphatikizapo mayi anga, aphedwa.

SINDINAKHULUPIRIRE zimene ndinaonazo. Kodi chinachitika n’chiyani? Nanga ndikanatani pamenepa? Panyumbapo panalibe munthu wina aliyense ndipo ndinasowa chochita moti ndinangoti kakasi. Koma ndisanapitirize, tadikirani kaye ndikufotokozereni pang’ono mbiri yanga. Zimenezi zikuthandizani kuti mumvetse mmene ndinakhudzidwira ndi mavuto amenewa komanso mavuto ena amene ndinakumana nawo m’moyo wanga.

Tinapeza Choonadi

Ndinabadwira m’dera la Quirimán, pafupi ndi tawuni ya Nicoya, m’dziko la Costa Rica. Mu 1953, ndili ndi zaka 37, ndinkakhala ndi makolo anga pafamu yathu. Ngakhale kuti tinakulira m’banja la Chikatolika, sitinkasangalala ndi zinthu zina zimene tchalitchichi chimaphunzitsa ndipo tinali ndi mafunso ambiri omwe sitinkapeza mayankho ake.

Tsiku lina m’mawa, pakhomo pathu panafika munthu wina dzina lake Anatolio Alfaro, amene anatipempha kuti azitiphunzitsa Baibulo. Iye anatifotokozera mavesi ndiponso mfundo zambiri za m’Baibulo. Ndipo ineyo, bambo, mayi, mchimwene wanga, mlongo wanga ndiponso mnzake amene tinkakhala naye limodzi, tinakhala pansi n’kumamvetsera. Tinakambirana tsiku lonse mpaka pakati pa usiku chifukwa tinali ndi mafunso ambiri.

Anatolio anagona kwathu ndipo tinakhala naye mpaka tsiku lotsatira. Tinasangalala kwambiri ndi zimene iye anatiuza ndiponso chifukwa choti anagwiritsa ntchito Baibulo poyankha mafunso athu. Zimene tinakambiranazo zinatikhudza kwambiri. Tinaganizira kwambiri zimene tinaphunzirazo ndipo tinazindikira kuti tapeza choonadi. Pochoka, Anatolio anatisiira magazini ndiponso mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Madzulo aliwonse, tinkawerenga ndi kuphunzira mabukuwa, tonse pamodzi monga banja. Koma kuchita zimenezi kunali kovuta chifukwa tinalibe magetsi. Tisanayambe kuphunzira, aliyense ankatenga saka n’kuphimba nalo miyendo ndi mapazi ake podziteteza ku udzudzu.

Patapita miyezi 6, anthu asanu a m’banja mwathu, kuphatikizapo makolo anga ndi ineyo, tinabatizidwa. Kenako tinayamba kupita ku nyumba ndi nyumba n’kumauza ena zinthu zimene tinaphunzira. Tinkayenda ulendo wapansi pafupifupi maola awiri ndipo nthawi zina tinkakwera hatchi kupita ku tawuni ina yotchedwa Carrillo, kukasonkhana ndi Mboni za Yehova za kumeneko. Anatolio ankabwerabe kunyumba kwathu kudzaphunzira nafe Baibulo. Kenako, abale anakonza zoti tizisonkhana kunyumba kwathu ndipo pamisonkhanoyo tinkasonkhana anthu okwana 8. M’kupita kwa nthawi, anthu onse anabatizidwa ndipo gulu limeneli linakula n’kukhala mpingo wa anthu pafupifupi 20.

Ndinayamba Utumiki Wanthawi Zonse

Patapita nthawi, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Costa Rica inalengeza kuti ikufuna anthu omwe angadzipereke kuyamba utumiki wanthawi zonse. Mu 1957, ndinadzipereka kuyamba utumikiwu. Kunena zoona, ntchitoyi inali yosangalatsa kwambiri. Nthawi zambiri, ndinkayenda ndekha kwa maola ochuluka kupita kokalalikira kwa anthu a m’madera a kumidzi. Koma nthawi zina anthu sankandilandira bwino. Ndikukumbukira kuti ndinaopsezedwapo katatu konse ndi anthu omwe anali ndi zikwanje ndipo ankandifunsa kuti ndine ndani ndiponso ndikuchita chiyani.

M’zaka za m’1950, zinali zovuta kuyendera anthu chifukwa choti misewu yambiri inali ing’onoing’ono yodutsa m’tchire. Kuti tifike m’madera ena, tinkafunika kukwera hatchi ndiponso kuwoloka mitsinje yambiri. Nthawi zina tinkagona m’tchire ndipo udzudzu unkatisowetsa mtendere. Tinkafunikanso kusamala kwambiri chifukwa m’tchiremo munali njoka ndiponso ng’ona. Ngakhale zinali choncho, ndinkasangalala kwambiri kuthandiza ena kuti aphunzire ndiponso kudziwa za Yehova Mulungu. Ndipo ndikafika kunyumba, ndinkasangalala kwambiri chifukwa ndinkaona kuti ndakwanitsa kuphunzitsa anthu choonadi cha m’Baibulo. Ndikamalalikira ndiponso kuphunzira Baibulo tsiku lililonse, chikondi changa kwa Yehova Mulungu chinkakula kwambiri ndipo ndinkaona kuti ubwenzi wanga ndi iye ukulimba.

Patapita nthawi, ndinapatsidwa maudindo ena. Kwa zaka zoposa 10, ndinatumikira monga woyang’anira woyendayenda ndipo ndinkayendera ndi kulimbikitsa mipingo yosiyanasiyana mlungu uliwonse. Ngakhale kuti ndinayenera kusiya utumikiwu chifukwa chodwaladwala, koma ndinapitirizabe ndipo ndinkasangalala kutumikira Mulungu nthawi zonse.

Zinali Zoopsa Kwambiri

Mu 1971, ndili m’tawuni ya Nicoya, ndinaganiza zopita kumudzi kwathu kuti ndikaone anthu. Nditangolowa m’nyumba, ndinapeza mayi anga omwe panthawiyo anali ndi zaka 80, ali kwala pansi. Iwo anali atawomberedwa ndiponso kubayidwa. Nditawagwira, ndinaona kuti anali adakali ndi moyo koma patapita kanthawi kochepa, anamwalira ali m’manja mwanga. Nditaponyaponya maso, ndinaona mayi wina yemwe anali woyembekezera kwa miyezi 8 ndipo ankagwira ntchito yophika m’nyumba mwathu, nayenso ali kwala pansi kukhitchini, ataphedwa. Ndipotu sizinali zokhazi, nditamwazamwaza maso, ndinaonso mlongo wina ataphedwa, ndipo nditalowa kubafa, ndinapeza mwana wamwamuna wa mayi yemwe ankagwira ntchito yophika uja ataphedwanso. Onse anali atawomberedwa ndiponso kubayidwa mwankhanza kwambiri. Ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi ndani amene anachita zimenezi ndipo n’chifukwa chiyani?’

Nditatuluka panja, ndinapezanso bambo anga atawomberedwa m’mutu koma anali adakali ndi moyo. Kenako ndinathamanga kupita kwa mng’ono wanga yemwe ankakhala pafupi ndi nyumba yathu kuti ndikamuuze zimene zinachitikazo. Koma kumeneko ndinakamva kuti mayi wina ndi mwana wake wamwamuna aphedwanso. Ndinamva chisoni kwambiri kumva kuti amene anachita zimenezi anali mwana wamwamuna wa zaka 17 wa mchemwali wanga. Mnyamatayo sanali wa Mboni za Yehova ndipo ankadwala misala. Panthawiyi, iye anali atathawa m’deralo ndipo apolisi anayamba kumusakasaka. Aka kanali koyamba m’mbiri yonse ya dziko la Costa Rica kuti apolisi agwire ntchito yosaka munthu yaikulu chonchi.

Posapita nthawi, nkhaniyi inali ponseponse m’dziko lonse la Costa Rica. Patatha mlungu umodzi, apolisi anapeza mnyamatayo ali ndi chimpeni chachikulu ndiponso mfuti yaing’ono. Munthu wina ndi amene anam’gulitsa mfutiyo ngakhale kuti ankadziwa kuti iye amadwala misala. Apolisiwo anawombera ndi kupheratu mnyamatayo pomwe ankafuna kumugwira.

Panthawi imene apolisi ankasakasaka mnyamatayo, anthu ambiri anandichenjeza kuti ndithawe m’deralo poopa kuti iye angabwerere n’kudzandipha. Ndinapemphera kwa Yehova za nkhaniyi chifukwa ndinkaona kuti ndikufunika kukhalabe m’derali pamodzi ndi anthu a m’banja mwathu amene anapulumuka ndiponso anthu a mumpingo mwathu. Motero, ndinapitiriza kukhalabe m’derali.

Ndinakumana ndi Mavuto Enanso Motsatizana

Koma zinali zomvetsa chisoni kuti bambo anangokhala chaka chimodzi chokha kenako n’kumwalira. M’chaka chotsatira, mlongo wanga yemwe anali mtumiki wokhulupirika wa Yehova Mulungu anaphedwanso ndi anthu ena. Apanso banja lathu lonse linamva chisoni kwambiri. Ndipo sindingathe kufotokoza chisoni chimene ife ndiponso anzathu tinali nacho. Komabe m’nthawi yovutayi, ndinadalira Yehova kwambiri ndipo ndinkamupempha mobwerezabwereza kuti andipatse mphamvu.

Mu 1985, ndinakachita nawo sukulu ya akulu achikhristu ya masiku atatu imene inachitikira mumzinda wa San José, womwe ndi likulu la dzikoli. Ndinalimbikitsidwa kwambiri ndi sukulu imeneyi. Ndipo titamaliza sukuluyi, ndinanyamuka Lolemba m’mamawa kupita kwathu. Koma ndisanafike kumalo okwerera mabasi, ndinakumana ndi achifwamba omwe anandigwira pakhosi n’kundibera. Zimenezi zinachitika mofulumira kwambiri moti sindinathe kuona nkhope zawo. Kuyambira nthawi imeneyo sinditha kulankhula mokuwa monga mwachikhalidwe cha anthu a Costa Rica. M’dera lathu la Guanacaste, azibambo amakuwa popatsana moni ndi anzawo kapenanso pofuna kuti anthu ena adziwe kuti iwo alipo. Ndisanakumane ndi achifwambawo, ndinkakuwa kwambiri, koma masiku ano ndimalephera kuchita zimenezi.

M’chaka cha 1979, ndinakwatira mlongo wina dzina lake Celia, yemwe anali wa mumpingo woyandikana ndi wathu. Mlongoyu ankakonda kwambiri Baibulo ndipo tsiku lililonse tinkawerenga ndiponso kuphunzira Baibulo pamodzi. Koma n’zomvetsa chisoni kuti iye anamwalira ndi matenda a khansa mu July 2001. Ndimamusowa kwambiri mkazi wangayo, komabe ndimalimba mtima chifukwa ndimadziwa kuti akufa adzauka.​—Yohane 5:28, 29.

Ndine Wosangalala Ngakhale Kuti Ndinakumana ndi Mayesero

Ngakhale kuti ndakumana ndi mavuto ochuluka ndiponso oopsa kwambiri m’moyo wanga kusiyana ndi anthu ena, ndimaona kuti mayesero amenewa anandithandiza kuti ndisonyeze kuti ndine wokhulupirika kwa Yehova. (Yakobe 1:13) Nthawi zonse ndimakumbukira kuti tonse timakumana ndi ‘zotigwera mwadzidzidzi,’ ndipo zimenezi zandithandiza kuti ndisamadandaule kwambiri ndi zinthu zimene ndakumana nazo. (Mlaliki 9:11) Ndimakumbukiranso kuti tikukhala “nthawi yovuta yoikika,” yomwe anthu ndi oopsa, achiwawa ndiponso osadziletsa. (2 Timoteyo 3:1-5) Sindimaiwalanso chitsanzo cha Yobu. Ngakhale kuti iye anakumana ndi mavuto ambiri, monga kumwalira kwa ana ake, kudwala ndiponso kutha kwa chuma chake, iye ananena molimba mtima kuti: “Lidalitsike dzina la Yehova.” Ndipotu Yehova anam’dalitsa kwambiri chifukwa chopitirizabe kukhala wokhulupirika. (Yobu 1:13-22; 42:12-15) Mfundo za m’Baibulo zonsezi zimandithandiza kukhalabe wosangalala ngakhale kuti ndinakumana ndi mavuto ambirimbiri.

Yehova wakhala akundithandiza nthawi zonse kuti ndipitirize kumukonda. Kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kwandithandizanso kukhala wopirira ndiponso wolimba mtima. Kupemphera kwa Yehova nthawi zonse kwandithandiza kuti ndikhale ndi “mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira.” (Afilipi 4:6, 7) Choncho panopa ndili ndi mtendere wa mumtima. Kupezeka pamisonkhano yachikhristu ndiponso kuyankhapo kwandithandizanso kuti ndikhale ndi chikhulupiriro cholimba.​—Aheberi 10:24, 25.

Ngakhale kuti tsopano ndakalamba, ndikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa ndidakali ndi mphamvu ndipo ndimagwira nawobe ntchito yolalikira ndi Akhristu anzanga ndiponso ndimaphunzira Baibulo ndi anthu ena. Kuchita zimenezi kumandithandiza kuti ndikhalebe ndi mphamvu zopiririra mavuto. Ndipo ndikuthokoza kwambiri Yehova kuchokera pansi pa mtima ngakhale kuti ndakumana ndi mavuto ambiri. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 26 M’bale Enrique Caravaca Acosta anamwalira ali ndi zaka 90, patangopita zaka ziwiri kuchokera pamene anatitumizira nkhaniyi.

[Mawu Otsindika patsamba 20]

Kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kwandithandiza kukhala wopirira ndiponso wolimba mtima

[Chithunzi patsamba 19]

Kale, ndikukamba nkhani ya m’Baibulo

[Chithunzi patsamba 20]

Ndili mu utumiki wa kumunda panthawi imene ndinali wachinyamata