Chipembedzo Chabwino Chimalimbikitsa Anthu Kukondana
BAIBULO limati: “Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Choncho, chipembedzo chabwino chiyenera kulimbikitsa anthu ake kuti azikondana.
Zipembedzo zambiri zimagwira ntchito yabwino monga kuthandiza odwala, okalamba ndiponso osauka. Zimalimbikitsa anthu awo kuti azitsatira malangizo a mtumwi Yohane akuti: “Ngati wina aliyense akukhala ndi chuma ndipo aona m’bale wake ali wosowa ndipo osamvera chisoni, kodi chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye? Ana okondedwa, chikondi chathu chisakhale 1 Yohane 3:17, 18, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.
cha pakamwa pokha koma cha pazochita zathu ndi m’choonadi.”—Komano kodi chimachitika n’chiyani mayiko akamamenyana? Kodi lamulo la Mulungu lakuti “uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini,” liyenera kutsatiridwa panthawi yamtendere yokha? Kapena linganyalanyazidwe chifukwa choti mtsogoleri wandale kapena mfumu yalamula kuti dziko lake limenyane ndi dziko lina?—Mateyo 22:39, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Yesu anati: “Anthu onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana.” (Yohane 13:35, Malembo Oyera) Mukamayankha mafunso otsatirawa, dzifunseni kuti, ‘Kodi anthu achipembedzochi amakonda anthu onse nthawi zonse, osati ndi pakamwa chabe koma ndi zochita zawo?’
NKHANI: Nkhondo.
ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: Yesu analamula ophunzira ake kuti: “Ine ndikuuzani: Kondani adani anu ndi kuwapempherera akukuzunzani.”—Mateyo 5:44, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.
Asilikali atabwera kudzagwira Yesu, mtumwi Petulo anatulutsa lupanga n’cholinga choti ateteze Yesu. Komabe, iye anamuuza kuti: “Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.”—Mateyo 26:52, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Mtumwi Yohane analemba kuti: “M’menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdyerekezi: Yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda m’bale wake. Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake: osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha m’bale wake.”—1 Yohane 3:10-12, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
FUNSO: Kodi chipembedzochi chimalimbikitsa anthu ake kuti azimenya nawo nkhondo?
NKHANI: Ndale.
ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: Anthu ena ataona kuti Yesu anali ndi mphamvu zochita zozizwitsa, anafuna kuti iye alowe m’ndale. Koma kodi iye anatani? Baibulo limati: “Yesu atadziwa kuti iwo amafuna kubwera kudzamuumiriza Iye kuti akhale mfumu, anachoka napita ku phiri kwayekha.”—Yohane 6:15, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.
Yesu atamangidwa n’kunamiziridwa kuti ankalimbikitsa anthu kuukira boma, iye anayankha kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.”—Yohane 18:36, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Popempherera ophunzira ake, Yesu anati: “Ine ndawapatsa iwo mawu anu ndipo dziko lapansi liwada iwo, pakuti siali a dziko lapansi monga Yohane 17:14, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.
Ine sindili wadziko lapansi.”—FUNSO: Kodi chipembedzochi chimatsanzira Yesu popewa kulowerera m’ndale, ngakhale kuti zimenezi zingachititse kuti anthu ake azidedwa ndi anthu ena andale?
NKHANI: Tsankho.
ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: Anthu oyambirira omwe sanali Ayuda komanso anali osadulidwa, atakhala Akhristu, mtumwi Petulo ananena kuti: “Mulungu alibe tsankho; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”—Machitidwe 10:34, 35, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Polembera Akhristu a m’nthawi ya atumwi, Yakobe ananena kuti: “Abale anga, monga mwa Yesu Khristu wa ulemerero, musaonetse kukondera. Tangoganizirani kuti pakati panu patabwera munthu wovala mphete yagolide ndi zovala zapamwamba ndipo munthu wosauka wovala nsanza nabweranso pomwepo. Ngati mutaonetsa chidwi pa munthu uja wovala bwinoyu munena kuti, ‘Khalani pampando wabwinowu’ koma wosauka uja n’kumuuza kuti, ‘Imirirani apo.’ kapena ‘Khalani pansi pafupi ndi mapazi angawa,’ kodi simunachite tsankho pakati panu ndikukhala oweruza ndi maganizo oyipa?”—Yakobe 2:1-4, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.
FUNSO: Kodi chipembedzochi chimaphunzitsa kuti Mulungu amaona kuti anthu onse ndi ofanana? Nanga kodi chimalimbikitsa anthu kuti asamasale anzawo chifukwa cha mtundu wawo kapena chifukwa choti ndi osauka?
Kodi ndi chipembedzo chiti chimene chimalimbikitsa anthu ake kuti asamasale anzawo chifukwa cha ndale, mtundu ndiponso chifukwa choti ndi osauka?