Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mzimu Woyera Ndi Mphamvu Yofunika Pamoyo Wanu

Mzimu Woyera Ndi Mphamvu Yofunika Pamoyo Wanu

Mzimu Woyera Ndi Mphamvu Yofunika Pamoyo Wanu

MFUMU DAVIDE atachita tchimo lalikulu, anapemphera mochokera pansi pa mtima kuti: “Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere mzimu wanu woyera.”​—Salmo 51:11.

Davide anathandizidwa ndi mzimu woyera maulendo ambiri. Ali mnyamata, mzimu woyera unamuthandiza kugonjetsa Goliyati, yemwe anali msilikali woopsa kwambiri. (1 Samueli 17:45-50) Mzimu woyera unam’thandizanso kulemba ena mwa masalmo abwino kwambiri. Davide anati: “Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine, ndi mawu ake anali pa lilime langa.”​—2 Samueli 23:2.

Ndipo Yesu Khristu anatsimikizira kuti mzimu woyera unathandizadi Davide pamoyo wake. Panthawi ina, Yesu anauza omvera ake kuti: “Mwa mzimu woyera, Davide mwiniyo anati, ‘Yehova anati kwa Mbuye wanga: “Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako kunsi kwa mapazi ako.”’” (Maliko 12:36; Salmo 110:1) Yesu ankadziwa kuti Davide anathandizidwa ndi mzimu woyera polemba masalmo. Kodi mzimu woyera umenewu ungatithandize masiku ano?

“Pemphanibe, Ndipo Adzakupatsani”

N’zodziwikiratu kuti inuyo simungalembe masalmo koma mwina mungakumane ndi mavuto oopsa ngati Goliyati. Mwachitsanzo, ganizirani za Isabel. * Mwamuna wake anamusiya n’kukakwatira mtsikana. Iye anamusiya ali ndi ngongole yaikulu ndipo sankam’patsa ndalama zothandizira ana awo aakazi awiri. Isabel anati: “Ndinkaona kuti anandipusitsa ndiponso ananditaya. Komabe, ndikuona kuti mzimu woyera wa Mulungu wandithandiza kwambiri chichokereni mwamuna wanga.”

Kodi Isabel analandira mzimu woyera atangokhala, osachita chilichonse? Ayi, iye ankapempha Mulungu tsiku lililonse kuti am’patse mzimu wake. Iye ankadziwa kuti ankafunika mphamvu ya Mulungu kuti apirire mavuto ake, asamalire bwino ana ake ndiponso athetse vuto lake lodziona kuti ndi wosafunika. Iye anatsatira mawu a Yesu akuti: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani; funafunanibe, ndipo mudzapeza, gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani.”​—Mateyo 7:7.

Nayenso Roberto anaona kuti ankafunika mzimu wa Mulungu kuti umuthandize pavuto lake losuta kwambiri fodya ndiponso chamba. Iye anayesetsa kwa zaka ziwiri kuti athetse vuto limeneli koma ankalephera kusiya. Roberto anati: “Munthu amavutika kwambiri akasiya kusuta chifukwa tsiku lililonse, amakhalabe ndi chibaba cha fodyayo.”

Roberto anapitiriza kuti: “Koma ndinatsimikiza mtima kuti nditumikire Mulungu moyenera. Choncho, ndinayesetsa kuti m’maganizo mwanga muzikhala zinthu zabwino zimene ndinkawerenga m’Baibulo. Tsiku lililonse, ndinkapemphera ndi mtima wonse kuti Mulungu andipatse mphamvu chifukwa ndinkadziwa kuti pandekha sindingathe kusintha moyo wanga. Ndinaona mmene Yehova ankayankhira mapemphero anga, makamaka ndikakhumudwa chifukwa choti ndayambiranso khalidweli. Ndimakhulupirira kuti mzimu woyera wa Mulungu unandipatsa mphamvu. Popanda mzimu umenewu sindikanakwanitsa kusiya kusuta.”​—Afilipi 4:6-8.

Kuuluka Pamwamba “Ndi Mapiko Monga Ziombankhanga”

Mofanana ndi Isabel ndi Roberto, Mboni za Yehova zambirimbiri zathandizidwa ndi mzimu woyera pamoyo wawo. Ngati mutafuna, Yehova angakupatseni mphamvu yake yogwira ntchito, imene anaigwiritsa ntchito polenga chilengedwe chonsechi. Mulungu ndi wofunitsitsa kukupatsani mzimu wake ngati mungam’pemphe mwakhama. Koma kuti akupatseni, muyenera kuphunzira choonadi chake ndiponso muziyesetsa ndi mtima wonse kuchita zimene iye amafuna.​—Yesaya 55:6; Aheberi 11:6.

Mwamphamvu ya mzimu woyera, mungakwanitse kutumikira Mulungu bwinobwino ndiponso mungathane ndi mavuto aliwonse amene mungakumane nawo. Baibulo limatitsimikizira mfundo imeneyi motere: “[Yehova] alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu. . . . Iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.”​—Yesaya 40:28-31.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Tasintha mayina ena.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

‘Tsiku lililonse, ndinkapemphera ndi mtima wonse kuti Mulungu andipatse mphamvu chifukwa ndinkadziwa kuti pandekha sindingathe kusintha moyo wanga. Ndipo ndinaona mmene Yehova anayankhira mapemphero anga’

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 7]

ZIMENE MZIMU WOYERA UNACHITA

Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu woyera polenga dziko lapansi ndiponso chilengedwe chonse. Wamasalmo anati: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu. Potumizira mzimu wanu, zilengedwa.”​—Salmo 104:24, 30; Genesis 1:2; Yobu 33:4.

Mzimu woyera unathandiza anthu okhulupirika kulemba Baibulo. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.” (2 Timoteyo 3:16) Mzimu wa Yehova unatsogolera anthu osiyanasiyana kuti alembe “mawu a Mulungu.”​—1 Atesalonika 2:13.

Mzimu woyera unathandiza atumiki a Mulungu kuti alosere molondola zinthu za m’tsogolo. Mtumwi Petulo ananena kuti: “Ulosi wa m’Malemba suchokera m’maganizo a munthu. Chifukwa ulosi sunayambe wadzapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.”​—2 Petulo 1:20, 21; Yoweli 2:28.

Mzimu woyera unathandiza Yesu ndiponso anthu ena okhulupirika kuti alalikire uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndiponso kuti achite zozizwitsa. Yesu anati: “Mzimu wa Yehova uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi za kuchiritsidwa kwa akhungu.”​—Luka 4:18; Mateyo 12:28.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 9]

MMENE MZIMU WOYERA UNGATITHANDIZIRE

Mzimu woyera ungakuthandizeni kugonjetsa ziyeso ndiponso kusiya makhalidwe oipa. Mtumwi Paulo anati: “Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire, koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.”​—1 Akorinto 10:13.

Mzimu woyera ungakuthandizeni kukhala ndi makhalidwe amene amasangalatsa Mulungu. “Zipatso za mzimu ndizo chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa, kudziletsa.”​—Agalatiya 5:22, 23.

Mzimu woyera ungakuthandizeni kupirira mayesero. “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.”​—Afilipi 4:13.