Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chinsinsi cha Banja Losangalala

Zimene Mungachite Ngati Mkazi Kapena Mwamuna Wanu Ali ndi Matenda Aakulu

Zimene Mungachite Ngati Mkazi Kapena Mwamuna Wanu Ali ndi Matenda Aakulu

Atandipeza ndi matenda enaake osachiritsika amene amachititsa thupi kukhala lofooka kwambiri, ndinasiya ntchito. Kuyambira nthawi imeneyo, mwamuna wanga yekha ndi amene ali pantchito. Koma iye sakambirana nane chilichonse chokhudza ndalama, choncho ndimadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani iye akuchita zimenezi?’ Ndikuganiza kuti mwina tatsala ndi ndalama zochepa kwambiri ndipo akuganiza kuti akandiuza, ndikhumudwa kwambiri.​—Anatero Nancy. *

M’BANJA mungakhale mavuto, koma mavutowo angachuluke kwambiri ngati mkazi kapena mwamuna ali ndi matenda aakulu. * Kodi inuyo mukusamalira mkazi kapena mwamuna wanu yemwe akudwala? Ngati zili choncho, mwina nthawi zina mumadzifunsa mafunso ngati awa: ‘Kodi ndingatani kuti ndipirire ngati matendawa atapitirira kukula? Kodi ndimusamalira mpaka liti komanso kupitiriza kugwira ntchito zonse monga kuphika, kuchapa ndiponso ntchito yoti ndizipeza ndalama? N’chifukwa chiyani ndimadandaula ndikaganizira kuti ineyo ndili bwinobwino pamene mnzangayu akuvutika ndi matenda?’

Ngati inuyo ndi amene mukudwala matenda aakulu, mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndingatani kuti ndisamadzione ngati wopanda pake ndikamalephera kuchita zinthu zina? Kodi mwina mnzangayu watopa ndi matenda angawa? Kodi mmene zililimu, ndiye kuti sitingakhalenso osangalala?’

N’zomvetsa chisoni kuti mabanja ena atha chifukwa choti mwamuna kapena mkazi ali ndi matenda aakulu. Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti banja lanu silingayende bwino.

Mabanja ambiri akuyenda bwino ngakhale kuti mwamuna kapena mkazi ali ndi matenda osachiritsika. Mwachitsanzo, taganizirani za Yoshiaki ndi mkazi wake, Kazuko. Yoshiaki amalephera kuchita chilichonse payekha chifukwa anavulala msana. Kazuko ananena kuti: “Mwamuna wanga amafunika kumuchitira chilichonse. Chifukwa choti nthawi zonse ndimam’samalira, ndimamva kupweteka khosi, mapewa ndiponso manja moti ndimachita kukalandira mankhwala kuchipatala. Ndikuona kuti kusamalira wodwala ndi ntchito yaikulu zedi.” Ngakhale pali mavuto amenewa, Kazuko ananenanso kuti: “Ine ndi mwamuna wanga tikukondana kwambiri kuposa kale.”

Ndiyeno, kodi n’chiyani chimene chingathandize mabanja otere kuti azisangalala? Choyamba, mabanja amene amayesetsa kukhala osangalala wina akamadwala amaona matendawo kuti ndi vuto la onse osati la amene akudwalayo basi. Ndipotu mmodzi akadwala, onsewo zimawakhudza, ngakhale kuti zimawakhudza m’njira zosiyana. Kugwirizana kwa mwamuna ndi mkazi wake kumeneku ndi kumene kunafotokozedwa pa Genesis 2:24 kuti: ‘Mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake ndipo adzakhala thupi limodzi.’ Choncho, ngati mwamuna kapena mkazi ali ndi matenda aakulu, onse awiri ayenera kuthandizana kuti apirire vutolo.

Komanso, kafukufuku wasonyeza kuti mabanja amene amakondanabe ngakhale kuti mmodzi mwa iwo ali ndi matenda aakulu, amangovomereza mmene zinthu zilili ndipo amayesetsa kusintha zina ndi zina pamoyo wawo kuti athe kupirira vutolo. Ndipo zambiri mwa njira zimene zawathandiza kupirira n’zogwirizana ndi malangizo a m’Baibulo, omwe ndi othandiza nthawi zonse. Taonani mfundo zitatu zotsatirazi.

Muziganizirana

Lemba la Mlaliki 4:9 limati: “Awiri aposa mmodzi.” N’chifukwa chiyani limatero? Vesi 10 limayankha kuti: “Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzake.” Choncho inuyo ‘mungadzutse mnzanu’ pomuyamikira.

Yesetsani kuona zimene mungachite kuti muthandize mnzanuyo. Mwachitsanzo, bambo wina dzina lake Yong, yemwe mkazi wake anafa ziwalo zina, anati: “Ndikamachita chilichonse, ndimaganiziranso mkazi wanga. Ndikamva ludzu, ndimaonanso kuti mkazi wanga ayenera kuti ali ndi ludzu. Ndikafuna kupita kowongola miyendo, ndimam’funsa ngati tingapitire limodzi. Ndimaona kuti mavuto amene tili nawo ndi a tonse ndipo timathandizana kuti tipirire.”

Komabe, ngati inuyo ndi amene mukudwala ndipo mukuthandizidwa ndi mkazi kapena mwamuna wanu, kodi pali zinthu zina zimene mungachite panokha popanda kuwonjezera vuto lanu? Ngati zili choncho, kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muzidziona kuti ndinu wofunika komanso zingathandize kuti mwamuna kapena mkazi wanu asamavutike pokusamalirani.

M’malo mongoganiza kuti mukudziwa zonse zimene mungachite pothandiza mnzanuyo, mungachite bwino kumufunsa zimene iye angakonde mutam’chitira. Mwachitsanzo, Nancy, amene tam’tchula koyamba uja, anauza mwamuna wake kuti akudandaula chifukwa choti sakudziwa mmene ndalama za banjalo zikuyendera. Tsopano mwamuna wake amayesetsa kukambirana naye chilichonse chokhudza ndalama zawo.

TAYESANI IZI: Aliyense alembe zimene akuganiza kuti mwamuna kapena mkazi wake azichita n’cholinga choti zinthu ziziyenda bwino. Kenako sinthanani mapepalawo. Aliyense asankhepo chinthu chimodzi kapena ziwiri zimene akuona kuti angakwanitse kuchita mosavuta.

Muzipeza Nthawi Yochita Zinthu Zina

Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Kanthu kali konse kali ndi nthawi yake.” (Mlaliki 3:1) Choncho, mungachite bwino kupeza nthawi yochitako zinthu zina. Komabe, zingaoneke zovuta kuti muzichita zinthu zina chifukwa matenda aakulu angasokoneze zochita za banja lanu. Ndiyeno, kodi mungatani kuti muzikhala ndi nthawi yochita zinthu zina?

Mwina mungachite bwino kuchita zinthu zina zokuthandizani kuiwalako pang’ono za matendawo. Kodi mungathe kuchita zinthu zina zimene munkakonda kuchita ndi mkazi kapena mwamuna wanu asanayambe kudwala matendawo? Ngati simungathe, bwanji osapeza zina zimene mungachite? Mwina mungachite zinthu zing’onozing’ono monga kumuwerengera mabuku mnzanuyo kapena kuchita zinthu zina zovutirapo monga kuphunzira chinenero china. Kuchita zinthu pamodzi zimene nonse mungathe, kungathandize kuti muzikondana kwambiri monga “thupi limodzi” ndiponso kuti muzisangalala kwambiri.

Chinthu china chimene chingakuthandizeni ndi kucheza ndi anthu ena. Lemba la Miyambo 18:1 limati: “Wodzipatula amafunafuna zolakalaka zake zosonyeza kudzikonda. Iye amachita zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.” (NW) Vesili likusonyeza kuti kudzipatula kungayambitse mavuto ena. Mosiyana ndi zimenezi, kucheza ndi anthu ena nthawi zina kungakuthandizeni kuti muzisangalala ndiponso kuti muchepetse maganizo. Choncho, inuyo mungachite bwino kuyamba kuitana anthu ena kuti adzakuchezereni.

Koma, nthawi zina zimavuta kuti mwamuna kapena mkazi amene akusamalira mnzake yemwe akudwala matenda aakulu apeze nthawi yochita zinthu zina. Ena amagwira ntchito modzipanikiza kwambiri ndipo zimenezi zimachititsa kuti pang’onopang’ono, thanzi lawo liyambe kufooka. M’kupita kwanthawi, zimenezi zingawachititse kuti azilephera kusamalira mnzawo wodwalayo. Motero, ngati mukusamalira mkazi kapena mwamuna wanu yemwe ali ndi matenda aakulu, musamadzipanikize kwambiri koma sankhani nthawi yoti muzipuma. * Ena amaona kuti zimawathandiza akauza mavuto awo anzawo apamtima, omwe ndi akazi kapena amuna anzawo.

TAYESANI IZI: Lembani mavuto amene mumakumana nawo posamalira mkazi kapena mwamuna wanu amene akudwala. Mukatero, lembani njira zimene mukuona kuti zingakuthandizeni kuthetsa kapena kupirira mavutowo. M’malo molemba chilichonse chimene mungachite pothana ndi vutolo, mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi njira yabwino kwambiri ndiponso yosavuta yothetsera mavutowa ndi iti?’

Yesetsani Kuona Zinthu Moyenera

Baibulo limachenjeza kuti: “Usanene, Kodi bwanji masiku akale anapambana ano?” (Mlaliki 7:10) Choncho, pewani kumangoganizira mmene moyo ukanakhalira popanda matendawo. Musaiwale kuti m’dzikoli, palibe amene akukhala moyo wopandiratu mavuto. Chofunika kwambiri ndi kungovomereza mmene zinthu zilili.

Kodi chimene chingakuthandizeni kuchita zimenezi n’chiyani? Kambiranani zinthu zimene zikukuyenderani bwino. Muzisangalala mukapezako bwino ngakhale pang’ono. Kambiranani zinthu zimene mukufuna kuti muchite ndipo pezani njira imene mungachitire zimenezo.

Bambo wina, dzina lake Shoji pamodzi ndi mkazi wake Akiko, anatsatira malangizo amenewa ndipo zinawathandiza kwambiri. Akiko atapezeka ndi matenda enaake aakulu, iye ndi mwamuna wake anafunika kusiya utumiki wawo wachikhristu womwe ankachita nthawi zonse. N’zosakayikitsa kuti zimenezi zinawakhumudwitsa. Komabe Shoji analangiza anthu omwe ali ndi vuto ngati limeneli kuti: “Musamangoganira zinthu zimene simungathenso kuchita chifukwa zimenezi zimangokhumudwitsa basi. Muziganizira zinthu zabwino. Ngakhale kuti nonse mungamayembekezere kuti mwina m’tsogolo muno zinthu zidzakhala bwino, yesetsani kuganizira za mmene zinthu zilili panopo. Ndipo ineyo ndimaganizira za mkazi wanga ndiponso mmene ndingamuthandizire.” Malangizo abwinowa angathandize inunso ngati mkazi kapena mwamuna wanu ali ndi matenda aakulu.

^ ndime 3 Tasintha mayina ena.

^ ndime 4 M’nkhani ino, tikambirana zimene mungachite ngati mkazi kapena mwamuna wanu ali ndi matenda osachiritsika. Komabe, mfundo zake zingathandizenso mabanja amene mkazi kapena mwamuna anavulala kwambiri pangozi, amavutika kwambiri maganizo kapenanso ndi wolumala.

^ ndime 20 Mogwirizana ndi mmene zinthu zilili, mungapeze anthu ena odziwa bwino ntchito yosamalira odwala kuti nthawi zina azikuthandizani kusamalira mnzanuyo.

DZIFUNSENI KUTI . . .

Kodi ine ndi mnzangayu tiyenera kuchita chiyani panopa?

  • Kukambirana kwambiri za matendawo

  • Kupewa kukambirana kwambiri za matendawo

  • Kupewa kuda nkhawa kwambiri

  • Kuchita zinthu moganizirana

  • Kuchita zinthu zimene tonse tingathe

  • Kucheza kwambiri ndi anthu ena

  • Kukhala ndi zolinga zimene tonse tingakwanitse