Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Anthu Amachita Zoipa?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amachita Zoipa?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amachita Zoipa?

PALI mfundo imodzi imene anthu ambiri sangakane ndipo mfundoyo ndi yonena kuti: Tonsefe ndife opanda ungwiro ndipo nthawi zina timalakwitsa kapena kuchita zinthu zimene pambuyo pake timazindikira kuti sitinachite bwino. Komabe kodi zimenezi ndi zimene zimachititsa kuti anthu azichita zoipa zambirimbiri zimene timaziona kapena kuzimva tsiku ndi tsiku, kaya ndi pa wailesi, pa TV, mu nyuzipepala kapenanso zimene ifeyo taziona tokha?

Ngakhale kuti ndife opanda ungwiro, anthu ambiri amavomereza kuti pali zinthu zina zimene munthu sayenera kuchita. Amakhulupiriranso kuti munthu wina aliyense akhoza kupewa kuchita zinthu zoipa. Ambirinso amavomereza kuti pali kusiyana pakati pa kunena mwangozi zinthu zinazake zosalondola ndi kunama mwadala, kuvulaza ena mwangozi ndi kupha munthu mwadala. Nthawi zambiri amene amachitira anzawo zinthu zoopsa ndi anthu amene amaoneka ngati abwinobwino, okhala nawo m’dera limodzi. Kodi n’chifukwa chiyani zili choncho? N’chifukwa chiyani anthu amachita zinthu zoipa?

Baibulo limafotokoza zambiri pa nkhani imeneyi. Limanena molondola zifukwa zenizeni zimene zimachititsa anthu kuchita zinthu zimenezi, ngakhale akudziwa kuti zimene akuchitazo ndi zoipa. Taonani zimene limanena.

“Nsautso iyalutsa wanzeru.”​MLALIKI 7:7.

Baibulo limasonyeza kuti nthawi zina anthu amakakamamizika kuchita zinthu zoipa chifukwa cha mmene zinthu zilili. Ena amaphwanya malamulo poganiza kuti akachita zimenezi athetsa mavuto ndiponso zinthu zopanda chilungamo zimene akukumana nazo. Buku lina linati: “Nthawi zambiri . . . anthu amachita zauchigawenga chifukwa chokhumudwa kwambiri ndi nkhani zandale, zachuma ndi zochitika m’madera amene amakhala, zomwe zimaoneka kuti sizingasinthe.”​—Urban Terrorism.

“Muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama.”​1 TIMOTEYO 6:10, BUKU LOPATULIKA NDILO MAU A MULUNGU.

Pa Chichewa pali mawu akuti: “Ndalama ndi Satana.” Mawu amenewa amatanthauza kuti ngakhale anthu abwino, nthawi zina amalolera kuchita zoipa n’cholinga choti apeze ndalama. Anthu ena amene amadziwika kuti ndi ochezeka komanso achifundo amalolera kuchita zoipa n’cholinga choti apeze ndalama kapena asaluze ndalama. Iwo amatha kusintha n’kuyamba kuchitira mwano ndiponso nkhanza anthu ena. Ndiponso tangoganizirani zoipa zimene ambiri amachita chifukwa cha dyera. Zinthu monga kuopseza kuti achitira ena zoipa akapanda kuwapatsa zinazake, kuba, katangale, kugwira ndi kusunga munthu mokakamiza ngakhale kupha kumene.

“Popeza sam’bwezera choipa chake posachedwa atam’tsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yawo kuchita zoipa.”​MLALIKI 8:11.

Lemba limeneli limanena za zimene anthu ambiri amaganiza. Iwo amaganiza kuti palibe vuto kuchita choipa chilichonse ngati palibe wina waudindo amene akuona. Mwachitsanzo, anthu amathamangitsa kwambiri galimoto, kubera mayeso, kuba ndalama za boma ndiponso kuchita zinthu zina zoipa ngati palibe wina waudindo amene akuona. Ndipo ngati palibe malamulo okhwima kapena sakuopanso kugwidwa, anthu omwe amadziwika kuti ndi omvera malamulo kwambiri amatha kuchita zinthu zimene suwayembekezera kuti angachite. Magazini ina inati: “Chifukwa chakuti anthu amene aphwanya malamulo salandira chilango, anthu ena abwinobwino amayambanso kuchita zinthu zoipa zophwanya malamulo.”​—Arguments and Facts.

“Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako cha iye mwini. Ndiye chilakolako chikatenga pathupi, chimabala tchimo.”​YAKOBE 1:14, 15.

Munthu aliyense nthawi zina angaganize zinthu zoipa. Tsiku lililonse, timakumana ndi mayesero ambirimbiri oti tichite zoipa. Kale Akhristu anauzidwa kuti: “Palibe mayesero amene mwakumana nawo osakhala amene amagwera anthu.” (1 Akorinto 10:13) Ngakhale zili choncho, zonse zimadalira zimene munthuyo wasankha kuchita, kaya kunyalanyaza maganizo oipawo kapena kuwalola kuti akule. Lemba limene lili pamwambali, la m’kalata youziridwa ya Yakobe, limachenjeza kuti ngati munthu alola maganizo oipa kuti ‘atenge pathupi,’ amayamba kuchita zinthu zoipa.

“Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: Koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.”​MIYAMBO 13:20.

Palibe amene angatsutse kuti anthu amene timacheza nawo angatichititse kukhala ndi makhalidwe abwino kapena oipa. Choncho, anthu amachita zinthu zimene safuna kuchita chifukwa chotengera anzawo. Zotsatira zake zimakhala zoipa kwambiri. M’Baibulo, mawu akuti anthu “opusa” satanthauza anthu opanda nzeru koma anthu amene amanyalanyaza malangizo opezeka m’Mawu a Mulungu. Choncho kaya ndife ana kapena achikulire, ngati timasankha anthu ocheza nawo kapena ochita nawo zinthu amene satsatira mfundo za m’Baibulo, tidziwe kuti ‘tidzapwetekedwa.’

Mavesi a m’Baibulo amenewa komanso ena amafotokoza momveka bwino zifukwa zimene anthu, ngakhale amene amadziwika kuti ndi amakhalidwe abwino, amachitira zinthu zoipa mwinanso zoopsa kwambiri. Kudziwa zimene zimachititsa anthu kuchita zinthu zoipa kwambiri n’kothandiza. Koma kodi pali chiyembekezo choti zinthu zidzasintha n’kuyamba kuyenda bwino? Inde, chifukwa Baibulo silimangonena zifukwa zimene anthu amachitira zoipa, koma limalonjezanso kuti zoipazo zidzatha. Kodi Baibulo limalonjeza chiyani pa nkhani imeneyi? Kodi zinthu zonse zoipa zimene zili padzikoli zidzathadi? Nkhani yotsatira iyankha mafunso amenewa.