Kodi Ndani Angamasulire Ulosi?
Kodi Ndani Angamasulire Ulosi?
Nthano inayake yakale imati mumzinda wa Gordium munamangidwa mfundo, yomwe inali chinthu chovutitsitsa kuchimasula m’masiku a Alekizanda Wamkulu. Munthu amene akanakwanitsa kumasula mfundo yovutayo anayenera kukhala wanzeru kwambiri komanso anayenera kudzagonjetsa mayiko ambiri. * Alekizanda ndi yemwe anakwanitsa kumasula mfundoyi ndipo malinga ndi nthanoyi, iye anangodula mfundoyo ndi lupanga lake kamodzi n’kamodzi.
KWA zaka zambiri, kuwonjezera pa kumasula mfundo zovuta, anthu anzeru ankamasuliranso miyambi, ankamasulira maulosi komanso ankalosera zam’tsogolo.
Komabe nthawi zambiri iwo ankalephera kumasulira zinthu zimenezi. Mwachitsanzo, anthu anzeru a ku Babulo analephera kumasulira uthenga umene dzanja linalemba mozizwitsa pakhoma la nyumba ya Mfumu Belisazara, pa nthawi imene ankachita phwando limene panali phokoso lalikulu. Koma Danieli yekha, mneneri wokalamba wa Yehova Mulungu, amenenso anali wodziwika bwino chifukwa cha nzeru zake zakuya, ndi amene anakwanitsa kumasulira uthenga waulosiwo. (Danieli 5:12) Ndipo ulosi umenewo, womwe unali wonena za kugonjetsedwa kwa Ufumu wa Babulo, unakwaniritsidwa usiku wa tsiku lomwelo.—Danieli 5:1, 4-8, 25-30.
Kodi Ulosi N’chiyani?
Mawu akuti ulosi amatanthauza kuneneratu kapena kulemberatu zinthu zodzachitika m’tsogolo, zinthuzo zisanachitike. Ulosi woona umakhala uthenga wouziridwa ndi Mulungu, kaya wachita kulembedwa kapena kunenedwa, ndipo umaneneratu zimene Mulungu akufuna kuchita. Mwachitsanzo, m’Baibulo muli maulosi osiyanasiyana, monga onena za kuonekera kwa Mesiya ndi mmene anthu adzamudziwire ndiponso onena za “mapeto a nthawi ino.” Komanso muli mauthenga achiweruzo ochokera kwa Mulungu.—Mateyu 24:3; Danieli 9:25.
Anthu amene amati ndi anzeru masiku ano, monga akatswiri asayansi, azachuma, azaumoyo, andale, azachilengedwe ndi ena ambiri, amayesa kuneneratu zimene zingachitike m’tsogolo. Mauthenga ambiri amene anthuwa amanena okhudza zimene akuganiza kuti zidzachitika m’tsogolo amafalitsidwa kwambiri m’mawailesi, pa TV ndi m’manyuzipepala. Ngakhale kuti anthu ambiri sakayikira mauthengawa, zoona zake n’zakuti akatswiriwo amangonena zimene akuganiza kuti zingachitikedi. Komanso, pa chilichonse chimene wina anganene kuti chidzachitika, nthawi zonse akatswiri ena amanena maganizo komanso mfundo zambirimbiri zotsutsa. Ndipotu anthu amene amaneneratu zimene akuganiza kuti zidzachitika m’tsogolo amasowa mtendere chifukwa sangathe kutsimikizira kuti zimene akunenazo zidzachitikadi.
Kodi Ulosi Woona Umachokera Kuti?
Nanga kodi ulosi woona umachokera kuti, ndipo ndani angaumasulire? Mtumwi Petulo analemba kuti: “Palibe mau a chinenero [ulosi wa m’Malemba NW] otanthauzidwa pa okha.” (2 Petulo 1:20, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.) Palembali, mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “otanthauzidwa” amatanthauzanso “kupeza njira” kapenanso “kuulula” makamaka ponena za “chinthu chimene chamasulidwa chomwe poyamba chinali chomangidwa.” N’chifukwa chake Baibulo lina linamasulira mawu a Petulowa kuti: “Munthu aliyense payekha . . . sangathe kumasula ulosi wa m’Malemba.”—The Amplified New Testament.
Tayerekezerani kuti munthu woyendetsa boti akumanga chingwe mwaluso n’kupanga mfundo yovuta kwambiri kumasula. Iye akamaliza kumanga mfundoyo, chimene munthu wamba angaone ndi chingwe chopotanapotana chomwe chapanga mfundo, koma sangadziwe mmene angachimasulire. Mofanana ndi zimenezi, masiku ano anthu angaone
zochitika zosiyanasiyana zimene zingayambitse mavuto aakulu, komabe sangadziwe mwatsatanetsatane mmene zinthu zidzakhalire m’tsogolomu.Aneneri akale ouziridwa, monga Danieli, sankayesa kulosera zam’tsogolo pongoona mmene zinthu zinkayendera m’nthawi yawo ndiyeno n’kunena zimene akuganiza kuti zingachitike m’tsogolo. Iwo akanayesa kulosera zam’tsogolo mwanjira imeneyi, ndiye kuti ulosiwo ukanakhala wa m’mutu mwawo, kapena kuti ukanangokhala maganizo chabe a anthu opanda ungwiro. M’malomwake, Petulo anapitiriza kufotokoza kuti: “Ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.”—2 Petulo 1:21.
‘Mulungu Ndiye Amamasulira’
Pafupifupi zaka 3,700 zapitazo, anthu awiri anatsekeredwa m’ndende ku Iguputo. Kenako anthu onsewo analota maloto osiyana oimitsa mutu kwambiri. Popeza anthuwo analibe mwayi woonana ndi anthu anzeru a m’dzikolo, iwo anauza Yosefe, yemwenso anali m’ndendemo, kuti: “Talota maloto, koma palibe wotimasulira malotowo.” Yosefe, yemwe anali mtumiki wa Mulungu anapempha anthuwo kuti amufotokozere malotowo, ndipo anawauza kuti: “Kodi Mulungu sindiye amamasulira maloto?” (Genesis 40:8) Yehova Mulungu yekha ndi yemwe amatha kumasulira maulosi, ngati mmene munthu yemwe wakhala akumanga ndi kumasula zingwe zoyendetsera boti kwa nthawi yaitali angamasulire mfundo yovuta kumasula. Popeza ndi Mulungu yemweyo amene anapereka maulosiwo, sangavutike kuwamasulira pa nthawi yake yoyenera. Ndipotu tiyenera kudalira iyeyo kuti tithe kumvetsa kumasulira kwake, kapena tanthauzo lake. Choncho, Yosefe sanalakwitse pamene anapereka ulemerero kwa Mulungu kuti ndiye amamasulira.
N’chifukwa chiyani tinganene kuti ‘Mulungu ndiye amamasulira maloto’ kapena maulosi? Pali zifukwa zambiri zotsimikizira mfundo imeneyi. Mwachitsanzo, maulosi ena a m’Baibulo analembedwa pamodzi ndi nkhani yonena za kukwaniritsidwa kwawo. Maulosi amenewa ndi osavuta kuwamasulira. Zimenezi n’zofanana ndi mfundo zina zomwe woyendetsa boti angafotokozere ena mosavuta mmene angazimasulire.—Genesis 18:14; 21:2.
Koma maulosi ena angafotokozedwe komanso kumasuliridwa poganizira mofatsa nkhani yonse yomwe mukupezeka ulosiwo. Mwachitsanzo, m’masomphenya aulosi, mneneri Danieli anaona ‘nkhosa yamphongo yomwe inali ndi nyanga ziwiri.’ Kenako anaona “mbuzi yamphongo yaubweya wambiri” yomwe ‘pakati pa maso ake panali nyanga yoonekera patali.’ Mbuziyo inagunda nkhosayo modetsa nkhawa n’kuigwetsera pansi. Nkhani yonse yomwe mukupezeka masomphenyawa ikusonyeza kuti nkhosa yamphongo ya nyanga ziwiri ikuimira “mfumu ya Mediya ndi mfumu ya Perisiya,” ndipo mbuziyo ikuimira “mfumu ya Girisi.” (Danieli 8:3-8, 20-22) Patapita zaka zoposa 200, Alekizanda Wamkulu, yemwe ankaimira “nyanga yaikulu” ija, anayamba kugonjetsa dera la Perisiya. Ndipo Josephus, yemwe anali katswiri wolemba mbiri yachiyuda, ananena kuti pa nthawi imene Alekizanda ankagonjetsa madera ozungulira mzinda wa Yerusalemu, anaonetsedwa ulosiwu ndipo anakhulupirira kuti unkanenadi za iyeyo.
Pali chifukwa chinanso chotsimikizira kuti ‘Mulungu ndiye amamasulira maloto’ kapena maulosi. Motsogoleredwa ndi mzimu woyera, Yosefe, amene anali mtumiki wokhulupirika wa Yehova Mulungu, anamvetsa tanthauzo la maloto ozunguza mutu amene akaidi anzakewo anamuuza. (Genesis 41:38) Atumiki a Mulungu masiku ano akapanda kumvetsa tanthauzo la ulosi winawake, amapemphera kuti Mulungu awapatse mzimu wake, kenako amaphunzira ndi kufufuza mozama m’Mawu a Mulungu ouziridwa ndi mzimu. Akatero Mulungu amawatsogolera kuti apeze malemba amene angawathandize kumvetsa matanthauzo a maulosi ena. Izi zikusonyeza kuti palibe munthu amene angatanthauzire maulosi mozizwitsa. Mulungu ndi amene amatanthauzira maulosi chifukwa chakuti atumiki ake amamvetsa maulosiwo mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu komanso Mawu ake. Choncho matanthauzo a ulosi tingawapeze m’Baibulo mokha, osati kwa anthu olosera zam’tsogolo.—Machitidwe 15:12-21.
Tinganenenso motsimikiza kuti ‘Mulungu ndiye amamasulira maloto’ kapena maulosi, chifukwa chakuti ndi iyeyo amene amasankha nthawi yoti atumiki ake okhulupirika padziko lapansi amvetse tanthauzo la ulosi, komanso amayendetsa zinthu kuti zimenezi zichitike pa nthawi yake. Tanthauzo la ulosi lingadziwike ulosiwo usanakwaniritsidwe, uli mkati mokwaniritsidwa, kapena utakwaniritsidwa kale. Popeza kuti Mulungu ndi amene amapereka ulosi, amaperekanso tanthauzo lake pa nthawi yake yoyenera.
Pa nkhani ya Yosefe ndi anzake awiri amene anali nawo m’ndende aja, Yosefe anamasulira malotowo kutatsala masiku atatu kuti akwaniritsidwe. (Genesis 40:13, 19) Patapita nthawi, Yosefe anatulutsidwa m’ndendemo kuti akamasulire maloto a Mfumu Farao, ndipo apa n’kuti zaka 7 zimene anthu anakolola chakudya chambiri zitatsala pang’ono kuyamba. Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, Yosefe anatanthauzira maloto a Farao. Izi zinathandiza kuti chakudya chokwanira chisungidwe m’zaka zimene malotowo anasonyeza kuti m’dzikomo mudzakhala chakudya chambiri.—Genesis 41:29, 39, 40.
Atumiki a Mulungu amamvetsa matanthauzo a maulosi ena pambuyo poti maulosiwo akwaniritsidwa. Mwachitsanzo, zinthu zambiri zimene zinachitika pa moyo wa Yesu zinalembedwa kale m’maulosi, zaka zambiri Yesuyo asanabadwe. Koma ophunzira a Yesu sankamvetsa bwino maulosi amenewa mpaka pamene Yesu anaukitsidwa. (Salimo 22:18; 34:20; Yohane 19:24, 36) Pomaliza, malinga ndi lemba la Danieli 12:4, maulosi ena anali ofunika ‘kuwatseka ndi kuwamata’ “kufikira nthawi yamapeto” pamene Danieli anati anthu “adzadziwa zinthu zambiri zoona.” Panopa tikukhala m’nthawi imene maulosi amenewo ali mkati mokwaniritsidwa. *
Kodi Maulosi a M’Baibulo Akukukhudzani Bwanji?
Yosefe ndi Danieli anaimirira pamaso pa mafumu a m’nthawi yawo n’kupereka mauthenga aulosi amene anakhudza mayiko ndi maufumu. Nawonso Akhristu a m’nthawi ya atumwi anaima pamaso pa anthu a m’nthawi yawo n’kumalankhulira Yehova, Mulungu wa maulosi, ndipo aliyense amene analabadira uthenga wawo anapeza madalitso.
Masiku anonso, a Mboni za Yehova padziko lonse akulengeza uthenga wa ulosi, kapena kuti uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Iwo akuuza anthu kuti ulosi wa Yesu wonena za “mapeto a nthawi ino” ukukwaniritsidwa panopa. (Mateyu 24:3, 14) Kodi ulosi umenewu mukuudziwa? Nanga kodi mukudziwa mmene udzakukhudzireni? A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukuthandizani kuti mumvetse ulosi umenewu ndi kupindula nawo. Ndipo n’zosakayikitsa kuti ulosiwu ndi umodzi mwa maulosi ofunika kwambiri pa maulosi onse a m’Baibulo.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Nthano ina yachigiriki imati mumzinda wa Gordium, womwe unali likulu la dera la Fulugiya, munali galeta lomwe linamangiriridwa kumtengo ndi mfundo yovuta kwambiri kumasula. Mwini wa galetalo anali munthu wina yemwe anayambitsa kumanga mzindawo dzina lake Gordius. Yemwe akanatha kumasula mfundoyo ndi munthu yekhayo amene akanagonjetsa chigawo cha Asia.
^ ndime 19 Onani nkhani zakuti “Maulosi 6 a M’Baibulo Amene Akukwaniritsidwa Masiku Ano” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2011.
[Zithunzi pamasamba 12, 13]
Yosefe komanso Danieli anapereka ulemerero kwa Mulungu pamene ankatanthauzira maulosi