Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Muzisangalatsa Yehova”

“Muzisangalatsa Yehova”

Mwambo wa Omaliza Sukulu ya Giliyadi​—Gulu la Nambala 131

“Muzisangalatsa Yehova”

PA SEPTEMBER 10, 2011, ophunzira a m’kalasi ya nambala 131 ya Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo limodzi ndi achibale awo, anzawo komanso anthu ena, anasonkhana pa mwambo wa omaliza maphunziro. Pamene mwambowo unkayamba, mitima ya ophunzira komanso ya okamba nkhani inali m’mwamba. Koma pofika kumapeto, anthu onse okwana 9,063 amene anapezeka pa mwambowu, anali osangalala chifukwa cha nkhani, zitsanzo komanso zimene ophunzirawo anafotokoza.

M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova yemwe anali tcheyamani pa mwambowu anakamba nkhani yoyamba. Iye anakambirana ndi ophunzirawo mavesi a m’Baibulo amene amasonyeza kuti Yehova Mulungu ali ndi thupi lophiphiritsira. Anafotokoza kwambiri malemba amene amalongosola mmene Yehova amagwiritsa ntchito maso, makutu komanso manja ake ophiphiritsira.

Poyamba m’baleyu anafotokoza lemba la 2 Mbiri 16:9 limene limanena kuti “maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” Ophunzirawo analimbikitsidwa kuti apitirize kukhala ndi mtima wodzipereka kwambiri kwa Yehova. Anawauzanso kuti, potengera chitsanzo cha Mulungu, aziona zinthu zabwino zimene ena amachita. Kenako M’bale Lett anafotokoza lemba la 1 Petulo 3:12 limene limanena kuti makutu a Yehova amamva pembedzero la anthu ake olungama. Analimbikitsanso ophunzirawo kuti azipemphera nthawi zonse podziwa kuti Yehova amafuna kumva mapemphero awo.

M’bale Lett anafotokozanso lemba la Yesaya 41:13. Palemba limeneli pali lonjezo ili la Yehova: “Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja. Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’” M’bale Lett anauza ophunzirawo kuti: “Mawu a Yehova amenewa ndi olimbikitsa. Iye amatambasula dzanja lake kuti agwire dzanja lathu.” Kenako m’baleyu analimbikitsa ophunzirawo kuti nthawi zonse azilola Yehova kuwathandiza ndipo asamakane. Ananenanso kuti ophunzirawo angatsanzire Yehova potambasula dzanja lawo ndi kuthandiza ena.

Pomaliza M’bale Lett anawerenga lemba la Yesaya 40:11 ndipo analimbikitsa omvera kuti aganizire za chikondi cha Yehova chimene chafotokozedwa palembali. Iye anati: “Yehova amatinyamula ndi manja ake n’kutiika pachifuwa pake.” Kodi ifeyo tizitani Yehova akafuna kutinyamula? Ophunzirawo analangizidwa kuti ayenera kukhala omvera komanso ofatsa ngati mwana wa nkhosa chifukwa zimenezi n’zimene zingachititse kuti Yehova azifuna kuwanyamula pachifuwa pake.

“Tili Ndi Chuma Chimenechi M’zonyamulira Zoumbidwa Ndi Dothi”

M’bale David Splane wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani ya mutu umenewu, womwe ndi wochokera m’Malemba. (2 Akorinto 4:7) Kodi chuma chimene chatchulidwa palembali ndi chiyani? Kodi chuma chimenechi ndi zimene tikudziwa kapena nzeru zomwe tili nazo? M’bale Splane ananena kuti: “Chuma chimenechi sichikutanthauza zimenezi. Chuma chimene mtumwi Paulo ankanena palembali ndi ‘utumiki woonetsera poyera choonadi.’” (2 Akorinto 4:1, 2, 5; Chipangano Chatsopano mu Chichewa Cha Lero.) M’bale Splane anakumbutsa ophunzirawo kuti pa miyezi isanu ya maphunziro awo, anali kukonzekera utumiki wapadera. Ophunzirawo ayenera kuona kuti utumiki umenewu ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri.

M’bale Splane anafotokozanso kuti “zonyamulira zoumbidwa ndi dothi” zimene zatchulidwa palembali zikutanthauza matupi athu. Iye anafotokoza kusiyana kwa chonyamulira chadothi ndi chagolide. Zonyamulira zagolide sizigwiritsidwa ntchito kawirikawiri. Koma zonyamulira zadothi n’zimene zimagwiritsidwa ntchito nthawi zambiri. Munthu akaika zinthu mu chonyamulira chagolide, amaganizira kwambiri za chonyamuliracho kuposa zinthu zimene wanyamulazo. Ndiyeno M’bale Splane anati: “Nanunso musamakaganizire kwambiri za inuyo. Monga amishonale cholinga chanu n’kuthandiza anthu kudziwa Yehova. Choncho, mukakhale ngati zonyamulira zoumbidwa ndi dothi.”

Popitiriza chitsanzochi, m’baleyu anafotokoza kuti kale zonyamulira zina zadothi zinkakhala zoti sizingawonongeke ndi moto ndipo zina ankazipaka zinthu zinazake n’cholinga choti zisamayoyoke. Kodi pamenepa mfundo yake inali yotani? Amishonalewo ayenera kukonzekera kuti m’miyezi yawo yoyambirira akakumana ndi mavuto. Mavutowo akawaphunzitsa kupirira ndipo pamapeto pake akakhala olimba ngati zonyamulira zopakidwa zinthu kunja kwake. Akadzakhala olimba, adzasiya kukwiya msanga anthu akamawanyoza kapena kuwachitira zinthu zokhumudwitsa. M’bale Splane anati: “Mukadzayamba utumiki wanu, mudzadabwa kuona mmene mulili olimba pokumana ndi mavuto.” Yehova wapereka utumiki wapadera umenewu kwa anthu, omwe ndi zonyamulira zoumbidwa ndi dothi, osati kwa angelo. M’baleyu anamaliza ndi mawu akuti: “Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amakudalirani kwambiri.”

“Unali Kuthamanga Ndi Anthu Oyenda Pansi . . . Ungapikisane . . . Ndi Mahatchi?”

M’bale Samuel Herd wa m’Bungwe Lolamulira anayamba nkhani yake ndi funso lakuti: “Kodi mungathe kuthamanga mofulumira komanso mtunda wautali?” Kodi n’chifukwa chiyani m’baleyu anafunsa ophunzirawo funso limeneli? Iye anayerekezera zimene ophunzirawo akakumane nazo ndi zimene mneneri Yeremiya anakumana nazo. Mneneriyu anali atakumana ndi mavuto ena komabe ankayembekezera kukumananso ndi mavuto ena aakulu kuposa oyambawo. Choncho Yehova anamufunsa kuti: “Pakuti unali kuthamanga ndi anthu oyenda pansi ndipo anali kukutopetsa, ndiye ungapikisane bwanji ndi mahatchi?”​—Yeremiya 12:5.

Pofotokoza mfundo ya lembali, M’bale Herd ananena kuti: “Mwina mungaganize kuti mwathamanga kale ndi mahatchi poganizira za mayeso amene mwalemba. Koma dziwani kuti pamenepa mwangothamanga ndi anthu oyenda pansi. Pa ntchito yanu yaumishonale mukathamanga ndi mahatchi kapena kuti mukakumana ndi mavuto aakulu kuposa amene mungaganizire panopa. Dziwani kuti sukuluyi yakuthandizani kukonzekera kuthamanga ndi mahatchi koma osatopa.” M’bale Herd analimbikitsa ophunzirawo kuti akapitirize kuphunzira Baibulo, kupemphera komanso kuchita zinthu zina zimene zingawathandize kukhala olimba mwauzimu.

M’bale Herd ananena kuti n’kutheka kuti ena mwa amishonale amenewa akakumana ndi zinthu zokhumudwitsa komanso anthu opanda chidwi. Ena akhoza kukadwala kapena kuyamba kudziona kuti sangakwanitse utumiki umene apatsidwa. Koma m’baleyu anatsimikizira ophunzirawo kuti Yehova akawathandiza kupeza mphamvu kuti akathe kupirira komanso kuti asakatope. Iye anati: “Kaya mukupikisana ndi anthu oyenda pansi kapena ndi mahatchi, muzikhulupirira kuti dzanja lamphamvu la Mulungu likhoza kukukokani kuti mudutse mzere womalizira wa mpikisanowo. Zimenezi zidzachititsa kuti mukwanitse utumiki wanu waumishonale ndipo zidzapangitsa kuti Yehova atamandidwe.”

Nkhani Zina Zapamwambowu

“Usakabwereke Zochepa Ayi.” M’bale John Ekrann, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ya ku United States anafotokoza nkhani yokhudza mneneri Elisa ndi mayi wina wamasiye amene ana ake aamuna anatsala pang’ono kugulitsidwa kuti akhale akapolo. (2 Mafumu 4:1-7) Mayi ameneyu anangotsala ndi kamtsuko kamodzi kokha ka mafuta. Ndiyeno Elisa anamuuza kuti apite kwa anthu okhala nawo pafupi kukabwereka zotengera zina zoti aikemo mafutawo. Iye anamuuza kuti: “Usakabwereke zochepa ayi.” Kudzera mwa Elisa, Yehova anachititsa kuti mafutawo adzaze m’zotengera zonse zimene mayiyo anabwereka. Kenako mayiyo anagulitsa mafutawo n’kupeza ndalama zokwanira kubweza ngongole imene anali nayo komanso anatsala ndi ndalama zina zomwe anagwiritsa ntchito pa banja lake.

Kodi nkhani imeneyi inaphunzitsa chiyani amishonale atsopanowo? Pamene mkazi wamasiyeyo ankakabwereka zotengera, ayenera kuti ankatenga chilichonse chimene chapezeka. M’bale Ekrann anati: “Mayiyo ayenera kuti ankatenga chinthu chilichonse chimene angathe kusungiramo mafuta ndipo akapeza chachikulu ankasangalala kwambiri.” Kenako m’baleyu analimbikitsa ophunzirawo kuti akalandire utumiki uliwonse umene angakapatsidwe, ngakhale utaoneka ngati wotsika. Iye anati: “Musamakasankhe utumiki.” M’baleyu anakumbutsa ophunzirawo kuti mayi wamasiye uja analandira madalitso ambiri chifukwa choti anatsatira malangizo onse amene Elisa anamupatsa. Kodi nkhani imeneyi ndi yothandiza bwanji? Tikamachita zinthu modzipereka komanso ndi chikhulupiriro, timalandiranso madalitso ambiri. M’bale Ekrann anauza ophunzirawo kuti: “Simuyenera kuchita zinthu moumira kapena mwamphwayi.”

“Ali Ngati Chakudya Kwa Ife.” M’bale William Samuelson, yemwe ndi woyang’anira wa Dipatimenti Yoyang’anira Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu, anakamba nkhani ya mutu umenewu wochokera palemba la Numeri 14:9. Iye anatchula chitsanzo chabwino chimene Yoswa ndi Kalebe anasonyeza. Mawu akuti “chakudya” amene anawagwiritsa ntchito palembali, anasonyeza kuti Aisiraeli adzagonjetsa anthu a ku Kanani ndipo zimenezi zidzachititsa Aisiraeliwo kukhala okhutira komanso zidzawalimbikitsa kwambiri. Kodi ophunzirawo anaphunzira chiyani pamenepa? M’bale Samuelson anati: “Pa ntchito yanu yaumishonale, muzikaona kuti mavuto omwe mungakumane nawo angakulimbikitseni komanso kukuthandizani kukhala okhutira.”

“Kodi Ngalawa Zawo Zachikhulupiriro Zidzatha Kulimbana Ndi Mphepo Yamkuntho?” M’bale Sam Roberson, mmodzi mwa alangizi a sukuluyi, anakamba nkhani yokhudza chenjezo la mtumwi Paulo lonena za anthu ena amene ‘chikhulupiriro chawo chinasweka ngati ngalawa.’ (1 Timoteyo 1:19) Iye analimbikitsa ophunzirawo kuti akathandize anthu ena kukhala ndi chikhulupiriro cholimba mwa Yehova Mulungu. M’baleyu anati: “Ntchito yanu ili ngati ya anthu osula zitsulo.” Munthu wosula zitsulo akhoza kulumikiza tizitsulo ting’onoting’ono n’kupanga tcheni chomwe chikhoza kugwira chombo mwamphamvu ndi kuchiteteza kuti chisapite ndi madzi. Mofanana ndi zimenezi, amishonale amathandiza ophunzira Baibulo kuti akhale ndi makhalidwe amene angawathandize kuti adzapulumuke.

Iye anayerekezera tizitsulo timene amalumikiza popanga tcheni ndi makhalidwe 8 amene anafotokozedwa pa 2 Petulo 1:5-8. M’bale Roberson ananena kuti ngati amishonalewo angathandize ophunzira Baibulo kuona mmene Yehova amasonyezera makhalidwe amenewa, ophunzira Baibulowo angayambe kukonda kwambiri Yehova. Iwo angathe kupirira mayesero alionse, amene ali ngati mphepo ya mkuntho, omwe angayese chikhulupiriro chawo.

Zokumana Nazo Komanso Kucheza Ndi Ophunzira

M’bale Michael Burnett, yemwe ndi mmodzi mwa alangizi a sukuluyi, anapempha ophunzirawo kuti afotokoze komanso kusonyeza zina mwa zimene anakumana nazo mu utumiki. Anthu amene anasonkhana pamwambowu anasangalala kumva zimene ophunzirawa anachita kuti athe kulalikira kwa anthu pamalo amalonda, kubwalo la ndege, kunyumba ndi nyumba komanso kwa munthu amene anaimba foni pa nambala yolakwika.

Kenako M’bale Michael Hansen, yemwe amatumikira pa Beteli ya ku United States, anacheza ndi abale atatu amene akhala amishonale kwa nthawi yaitali. Abale amenewa ndi Stephen McDowell yemwe watumikira ku Panama, Mark Noumair ku Kenya, ndi William Yasovsky ku Paraguay. Zimene abale amenewa ananena zinali zogwirizana ndi mutu wakuti: “Kukondwera Ndi Kuchita Chifuniro Cha Yehova.” (Salimo 40:8) Mwachitsanzo, M’bale Mark Noumair ananena zinthu zimene iye ndi mkazi wake anasangalala nazo pa ntchito yawo yaumishonale. Chimodzi mwa zosangalatsa zimenezi ndi choti iye ndi mkazi wake anapeza mabwenzi m’mipingo ya Mboni za Yehova imene ankatumikira. Komanso iwo anasangalala kuona abale akuyamba kutsatira malangizo, akusintha zinthu zina pa moyo wawo komanso kuona mmene Yehova wadalitsira khama la abalewo. M’bale Noumair anatsimikizira ophunzirawo kuti adzapeza madalitso ambiri m’tsogolo.

Kenako mmodzi mwa ophunzira a m’kalasiyi anawerenga kalata yoyamikira imene ophunzirawa analemba. Ndiyeno M’bale Lett anamaliza pulogalamu ya mwambowu ndi kulimbikitsa omaliza maphunzirowa kuti akachite zinthu mwanzeru. Iye anawauza kuti “adzasangalatsa Yehova” akakachita zimenezi. N’zodziwikiratu kuti amishonale amenewa akasangalatsadi Yehova pamene akumutumikira mokhulupirika pa ntchito yawo yaumishonale.​—Yesaya 65:19.

[Tchati/​Mapu patsamba 31]

ZA OPHUNZIRAWO

Mayiko amene ophunzira anachokera: 10

Avereji ya zaka zobadwa: 34.7

Avereji ya zaka zimene akhala Mboni kuchokera pamene anabatizidwa: 19.0

Avereji ya zaka zimene achita utumiki wa nthawi zonse: 13.5

[Mapu]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Ophunzirawa anatumizidwa kumayiko amene ali pansipa

KUMENE OPHUNZIRA ANATUMIZIDWA

BENIN

BRAZIL

BULGARIA

BURUNDI

CAMEROON

CANADA

CENTRAL AFRICAN REPUBLIC

GERMANY

GHANA

HONG KONG

INDONESIA

KENYA

LIBERIA

LITHUANIA

MALAYSIA

MOZAMBIQUE

NEPAL

PANAMA

PARAGUAY

SIERRA LEONE

SLOVAKIA

SOUTH AFRICA

UNITED STATES OF AMERICA

VENEZUELA

[Chithunzi patsamba 30]

Ophunzira akusonyeza zina mwa zimene anakumana nazo mu utumiki

[Chithunzi patsamba 31]

Gulu la Nambala 131 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo

Pamndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mumzera uliwonse mayina tawandandalika kuyambira dzina la munthu amene ali kumanzere kupita kumanja.

(1) Lesch, C.; Lesch, N.; Shakarjian, P.; Shakarjian, T.; Budden, R.; Budden, K.; Nash, T.; Nash, L.

(2) Tremblay, E.; Tremblay, C.; Garvey, D.; Garvey, G.; Gaunt, R.; Gaunt, P.; Lau, J.; Lau, J.

(3) Davis, S.; Davis, S.; Sargeant, J.; Sargeant, J.; Fonseca, C.; Fonseca, S.; Thenard, E.; Thenard, A.

(4) Petratyotin, A.; Petratyotin, R.; Reyes, N.; Reyes, N.; Eisiminger, B.; Eisiminger, S.; Hacker, J.; Hacker, C.

(5) Hartman, E.; Hartman, T.; Goolia, W.; Goolia, K.; Thomas, J.; Thomas, E.; Okazaki, N.; Okazaki, M.

(6) Mills, C.; Mills, A.; Benning, L.; Benning, T.; Sobiecki, S.; Sobiecki, T.; Gagnon, L.; Gagnon, E.

(7) Hansen, B.; Hansen, M.; Fahie, A.; Fahie, M.; Dalgaard, J.; Dalgaard, J.; Andersson, M.; Andersson, R.