Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tingakhale Bwanji Mkhristu Weniweni Komanso Nzika Yodalirika?

Kodi Tingakhale Bwanji Mkhristu Weniweni Komanso Nzika Yodalirika?

Kodi Tingakhale Bwanji Mkhristu Weniweni Komanso Nzika Yodalirika?

KODI Yesu ankachita zinthu ziwiri ziti pa utumiki wake? Choyamba, iye ankayesetsa kuthandiza anthu kuti asinthe mitima yawo, osati kusintha ndale. Mwachitsanzo, taonani mfundo imene Yesu anatsindika pa ulaliki wake wa paphiri. Iye asanafotokoze kufunika kokhala ngati mchere komanso kuwala, anauza omvera ake kuti anthu omwe “amazindikira zosowa zawo zauzimu” ndi amene amakhala osangalala. Iye ananenanso kuti: “Odala ndi anthu amene ali ofatsa, . . . oyera mtima . . . ndi anthu amene amabweretsa mtendere.” (Mateyu 5:1-11) Yesu anathandiza otsatira ake kusintha maganizo komanso zochita zawo kuti zigwirizane ndi mfundo za Mulungu. Anawathandizanso kudziwa ubwino wotumikira Mulungu ndi mtima onse.

Chachiwiri, Yesu akaona anthu akuvutika, ankagwidwa chifundo ndipo ankawathandiza kuti mavuto awowo achepe. Komabe, cholinga chake sichinali kuthetsa mavuto onse amene analipo. (Mateyu 20:30-34) Iye anachiritsa anthu odwala, koma sikuti matenda anatha. (Luka 6:17-19) Anathandiza anthu oponderezedwa, koma anthu anapitirizabe kuvutika chifukwa cha kupanda chilungamo. Iye anadyetsa anthu anjala, koma mavuto a njala anapitirirabe.​—Maliko 6:41-44.

Anathandiza Anthu Kusintha Mitima Yawo Komanso Anawachepetsera Mavuto

Kodi n’chifukwa chiyani cholinga cha Yesu chinali kusintha mitima ya anthu ndiponso kuchepetsa mavuto awo, osati kusintha boma kapena kuthetseratu mavuto onse? Ndi chifukwa chakuti Yesu ankadziwa kuti Mulungu ali ndi cholinga choti m’tsogolo adzagwiritse ntchito Ufumu Wake kuthetsa maboma onse a anthu ndiponso kuthetsa mavuto onse. (Luka 4:43; 8:1) Choncho, pa nthawi ina ophunzira ake atamupempha kuti apitirize kuchiritsa odwala, Yesu anawauza kuti: “Tiyeni tipite kwina kumidzi yapafupi, kuti ndikalalikire kumenekonso, pakuti ndicho cholinga chimene ndinabwerera.” (Maliko 1:32-38) Yesu anathandiza anthu ambiri amene anali ndi mavuto koma ntchito yofunika kwambiri kwa iye inali yolalikira ndi kuphunzitsa mawu a Mulungu.

Masiku anonso, a Mboni za Yehova akamalalikira amayesetsa kutsanzira Yesu. Akaona munthu amene akuvutika, amamumvera chifundo ndipo amayesetsa kumuthandiza kuti mavuto ake achepe. Komabe, a Mboni salimbana n’kuti athetse kupanda chilungamo konse m’dzikoli chifukwa amakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetse mavuto onse. (Mateyu 6:10) Mofanana ndi Yesu, iwo amayesetsa kusintha mitima ya anthu osati maboma andale. Ntchito imene amagwirayi ndi yofunika chifukwa chimene chingathandize kwambiri anthu si kusintha ndale, koma kuwathandiza kuti asinthe makhalidwe awo.

Iwo Ndi Nzika Zodalirika

Koma a Mboni za Yehova amakhulupirira kuti monga Akhristu ayenera kukhala nzika zodalirika. Choncho iwo amalemekeza ulamuliro wa boma. Kudzera m’mabuku awo komanso mu ntchito yolalikira, amalimbikitsa anthu kuti azimvera malamulo a boma. Komabe ngati boma lalamula kuti achite zinthu zosemphana ndi malamulo a Mulungu, iwo amasankha “kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”​—Machitidwe 5:29; Aroma 13:1-7.

A Mboni za Yehova amapita kunyumba za anthu a m’dera lawo ndipo amawapempha kuti aziphunzira nawo Baibulo kwaulere. Maphunziro amenewa athandiza anthu mamiliyoni ambiri kusintha mitima yawo. Chaka chilichonse, anthu ambiri amathandizidwa kusiya makhalidwe oipa monga chiwerewere, juga, kusuta fodya, kumwa mowa mwauchidakwa komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Anthu amenewa asintha makhalidwe awo oipa ndipo tsopano ndi nzika zodalirika chifukwa chophunzira kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo.​—Onani nkhani yakuti “Baibulo Limasintha Anthu,” patsamba 18.

Komanso maphunziro a m’Baibulo amenewa amathandiza kuti mwamuna azilemekezana ndi mkazi wake, ana azilemekeza makolo awo komanso kuti ana azilemekezana. Maphunziro amenewa amathandizanso kuti anthu onse m’banja azilankhulana bwino ndipo zimenezi zimachititsa kuti mabanja aziyenda bwino. Mabanja akakhala ogwirizana amachititsanso kuti anthu a m’dera lonse akhale ogwirizana.

Pambuyo pokambirana nkhani zimenezi, kodi mukuganiza bwanji? Kodi Baibulo limavomereza zimene anthu ena amachita zosakaniza ndale ndi chipembedzo? Yankho la funsoli ndi lachidziwikire kuti ayi, Baibulo silivomereza. Koma kodi Akhristu oona ayenera kuthandiza anthu a m’dera lawo? Inde, ayenera kutero. Koma kodi angachite bwanji zimenezi? Angachite zimenezi potsatira lamulo la Yesu lakuti ayenera kukhala ngati mchere komanso kuwala kwa dziko lapansi.

Anthu amene amayesetsa kutsatira malangizo a Khristu amenewa, iwo ndi mabanja awo amapindula komanso amapindulitsa anthu a m’dera limene amakhala. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu zambiri zokhudza maphunziro a Baibulo amenewa, omwenso akuchitika m’dera lanu. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Ngati mungafune kudziwa zambiri, pitani pa adiresi iyi ya Intaneti ya Mboni za Yehova: www.mr1310.com/ny.

[Mawu Otsindika patsamba 10]

Yesu ankayesetsa kuthandiza anthu kuti asinthe mitima yawo, osati kusintha ndale

[Mawu Otsindika patsamba 11]

A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti ayenera kukhala nzika zodalirika