Yandikirani Mulungu
Mitundu Idzadziwa Kuti Ine Ndine Yehova’
KODI mungamve bwanji anthu ena akukuimbani mlandu wa zinthu zoti inuyo simunachite? Nanga mungatani ngati zimene akukunamiziranizo zikuchititsa kuti anthu enanso, kuphatikizapo osalakwa, avutike? Mosakayikira mungayesetse kuti anthu onse adziwe kuti mlandu umene mukuimbidwawo ndi wabodza ndipo inuyo ndinu wosalakwa. Kodi mukudziwa kuti zoterezi n’zimenenso zikumuchitikira Yehova? Masiku ano anthu ambiri amaimba Mulungu mlandu chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo komanso mavuto amene akuchitika padzikoli. Chifukwa cha zimenezi, Mulungu ndi wofunitsitsa kusonyeza kuti zimene anthu akumunenerazi ndi zabodza. Taganizirani zimene zinalembedwa m’buku la Ezekieli.—Werengani Ezekieli 39:7.
Yehova ananena kuti: “Sindidzalolanso kuti dzina langa lidetsedwe.” Anthu akamanena kuti Yehova ndi amene amachititsa kuti zinthu zopanda chilungamo zizichitika, ndiye kuti akudetsa dzina lake. Kodi n’chifukwa chiyani tikutero? M’Baibulo, nthawi zambiri mawu akuti “dzina la munthu” amatanthauza mbiri ya munthuyo. Buku lina linanena kuti dzina la Mulungu limatanthauza “zimene anthu amadziwa zokhudza iye, zimene Mulungu ananena zokhudza iyeyo komanso ulemu umene angalandire chifukwa cha zochita zake.” Choncho dzina la Yehova likuphatikizapo mbiri yake yonse. Ndiye kodi Yehova amaziona bwanji zinthu zopanda chilungamo zimene zimachitika padzikoli? Iye amadana nazo kwambiri. Komanso amamvera chisoni anthu amene amachitiridwa zinthu mopanda chilungamo. * (Ekisodo 22:22-24) Ndiyetu anthu akamanena kuti Mulungu ndi amene amachititsa mavuto padzikoli, ndiye kuti akuwononga mbiri yake. Pamenepa iwo amakhala ‘akunyoza dzina lake.’—Salimo 74:10.
Onani kuti Yehova ananena kuti “dzina langa loyera.” (Vesi 7) M’Baibulo, nthawi zambiri dzina la Yehova limayendera limodzi ndi mawu akuti “loyera.” Tikanena kuti chinthu ndi “choyera” zimatanthauza kuti chinthucho n’chosadetsedwa. Dzina la Yehova ndi loyera chifukwa Yehovanso ndi woyera ndipo kwa iye kulibiretu uchimo kapena chodetsa.Ndiye chifukwa chake anthu amene amaimba Yehova mlandu chifukwa cha zoipa zimene zikuchitika padzikoli, amakhala akunyoza kwambiri ‘dzina lake loyera.’
Nkhani yaikulu m’Baibulo ndi yoti Yehova adzayeretsa dzina lake pogwiritsa ntchito Ufumu wake. Nkhani imeneyi yatsindikidwa kwambiri m’buku la Ezekieli. M’bukuli mawu osonyeza kuti ‘mitundu ya anthu idzadziwa kuti iye ndi Yehova’ amatchulidwa mobwerezabwereza. (Ezekieli 36:23; 37:28; 38:23; 39:7) Onani kuti apa sakunena kuti mitundu ya anthu idzachita kusankha ngati ikufuna kudziwa kuti iye ndi Yehova kapena ayi. M’malomwake, kaya iwo akufuna kapena ayi, koma ‘adzadziwa’ kuti iye ndi Yehova. Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova adzachita zinthu zimene zidzawakakamize anthuwa kudziwa kuti iye ndi Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndipo dzina lake limaimira kuti ndi woyera komanso wosadetsedwa.
Zimene Yehova walonjezazi, zoti ‘mitundu ya anthu idzadziwa kuti iye ndi Yehova,’ ndi nkhani yabwino kwa anthu amene amafunitsitsa kuona zinthu zopanda chilungamo komanso zoipa zonse zitatha padzikoli. Posachedwapa Yehova akwaniritsa lonjezo limeneli ndipo ayeretsa dzina lake kuti lisadzanyozedwenso. Iye adzachotsa mavuto onse padzikoli komanso anthu amene amayambitsa mavutowo ndipo adzapulumutsa anthu onse amene amalemekeza dzina lake. (Miyambo 18:10) Kodi simungafune kuyandikira Yehova, Mulungu woyera amenenso “amakonda chilungamo”?—Salimo 37:9-11, 28.
Mavesi amene mungawerenge mu September:
^ ndime 2 Onani nkhani yakuti “Yandikirani Mulungu—Wokonda Chilungamo,” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2008.