Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 YANDIKIRANI MULUNGU

Kodi Yehova Amakuganizirani?

Kodi Yehova Amakuganizirani?

Mayi wina yemwe poyamba sankakhulupirira kuti Mulungu amamuganizira, ananena kuti: “Nthawi zambiri ndimadziona kuti ndine munthu wosafunika ndipo maganizo amenewa amandipangitsa kuona kuti Mulungu sandiganizira.” Kodi inunso mumaganiza choncho? Mwina munadzifunsapo kuti: “Kodi Yehova amaganiziradi mtumiki wake aliyense payekha?” Yankho la funso limeneli ndi lakuti inde amaganizira mtumiki wake aliyense payekha. Umboni wake timaupeza poona zimene Yesu ananena.—Werengani Yohane 6:44.

Kodi Yesu, amene amadziwa bwino makhalidwe komanso zolinga za Yehova, anati chiyani pa nkhani imeneyi? (Luka 10:22) Iye ananena kuti: “Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine.” Izi zikusonyeza kuti n’zosatheka munthu kukhala wotsatira wa Khristu komanso mtumiki wa Yehova, ngati Yehova sanamukoke. (2 Atesalonika 2:13) Ngati titamvetsa zimene Yesu ankatanthauza ponena mawu amenewa, tingaone umboni wamphamvu wakuti Mulungu amaganizira aliyense payekha.

Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anati Yehova ndi amene amakoka munthu? Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “kukoka” amagwiritsidwanso ntchito pokoka ukonde wa nsomba. (Yohane 21:6, 11) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yehova amatikakamiza kuti tizimutumikira tisakufuna? Ayi. Yehova anatipatsa ufulu wosankha kumutumikira ndipo satikakamiza kuti tizimumvera. (Deuteronomo 30:19, 20) Yehova amafufuza mitima ya anthu onse padziko lapansi kuti apeze amene ali ndi mtima wofunadi kumutumikira. (1 Mbiri 28:9) Akapeza munthu wotero amamuthandiza. Kodi amamuthandiza bwanji?

Yehova akapeza munthu amene ali “ndi maganizo abwino” amamukoka mwachikondi. (Machitidwe 13:48) Iye amachita zimenezi m’njira ziwiri. Yoyamba, amagwiritsa ntchito uthenga wabwino wa m’Baibulo womwe umafikira aliyense ndipo yachiwiri, amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera. Yehova akapeza munthu wofunitsitsa kumva zimene Baibulo limanena, amagwiritsa ntchito mzimu wake kuti umuthandize munthuyo kumvetsa komanso kugwiritsa ntchito zimene akuphunzirazo pamoyo wake. (1 Akorinto 2:11, 12) N’zosatheka munthu kukhala wotsatira wa Yesu komanso mtumiki wa Yehova wodzipereka popanda kuthandizidwa ndi Yehova.

Yehova amafufuza mitima ya anthu onse padziko lapansi kuti apeze amene ali ndi mtima wofunadi kum’tumikira

Ndiyeno kodi mawu a Yesu amene amapezeka pa Yohane 6:44 amatiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova Mulungu? Tikuphunzirapo kuti Yehova amakoka munthu chifukwa amaona zinthu zabwino zimene amachita komanso chifukwa chakuti amaganizira aliyense payekha. Mayi yemwe tamutchula kumayambiriro kwa nkhani ino, analimbikitsidwa atamvetsa mfundo imeneyi. Iye ananena kuti: “Ndimaona kuti kukhala mtumiki wa Yehova ndi mwayi wamtengo wapatali kuposa chilichonse. Ndipo ngati Yehova anandisankha kuti ndikhale mtumiki wake, ndiye kuti amandiona kuti ndine wofunika kwambiri.” Kodi kudziwa kuti Yehova amaganizira mtumiki wake aliyense payekha sikukukulimbikitsani kufuna kuyamba kum’tumikira?

Mavesi amene mungawerenge mu May

Luka 22-24 mpaka Yohane 1-16