Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI BAIBULO LILI NDI UTHENGA WOTANI?

N’chifukwa Chiyani Mukufunika Kulidziwa Bwino Baibulo?

N’chifukwa Chiyani Mukufunika Kulidziwa Bwino Baibulo?

Baibulo ndi buku lotchuka kwambiri kuposa buku lina lililonse. Chinthu chimodzi chimene chimachititsa kuti Baibulo likhale lotchuka ndi chakuti limanena zinthu zimene ifenso zimatichitikira. Limafotokoza nkhani zokhudza anthu enieni ndiponso zimene ankachita ndi anthu anzawo komanso ndi Mulungu. Nkhani zimenezi zimatiphunzitsa mfundo zothandiza pogwiritsa ntchito mawu osavuta kumva, omwe angathe kumasuliridwa m’zinenero zambirimbiri ndipo mtundu uliwonse wa anthu ukhoza kuzimvetsa. Komanso malamulo a m’Baibulo ndi othandiza nthawi zonse.

Mfundo yofunika kwambiri ndi yakuti, Baibulo silimangonena zokhudza Mulungu koma limanenanso kuti linachokera kwa Mulungu. Limatithandiza kudziwa dzina la Mulungu, makhalidwe ake komanso cholinga chake cholengera anthu ndiponso dziko lapansi. Cholinga chimenechi sichinasinthe ndipo sichidzasintha. Baibulo limanenanso za nkhani yakale kwambiri yomvetsa chisoni yomwe inachitika m’munda wa Edeni. Nkhani imeneyi imakhudza dziko lonse lapansi ndipo mapeto ake adzakhala osangalatsa. Choncho kuwerenga Baibulo ndi maganizo oti tidziwe zoona zenizeni kungatithandize kukhala ndi chikhulupiriro komanso chiyembekezo.

Baibulo limatiuza mfundo zothandiza zomwe sitingazipeze kwina kulikonse. Mwachitsanzo, limatiuza zoona pa nkhani zotsatirazi:

  • Zimene zinachitika kuti tizikumana ndi mavuto

  • Zimene Mulungu anachita kuti apulumutse anthu

  • Zimene Yesu watichitira

  • Tsogolo la anthu komanso dziko lapansi

Mungachite bwino kuwerenga nkhani zotsatirazi kuti mudziwe uthenga umene uli m’Baibulo.