Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | MULUNGU AKHOZA KUKHALA MNZANU WAPAMTIMA

Kodi N’zotheka Mulungu Kukhala Mnzanu Wapamtima?

Kodi N’zotheka Mulungu Kukhala Mnzanu Wapamtima?

“Ukamadziwa kuti Mulungu ndi mnzako wapamtima, umaona kuti ndiwe wotetezeka ndipo umasangalala. Umaonanso kuti iye ndi wokonzeka kukuthandiza nthawi zonse kuti zinthu zizikuyendera bwino.”—CHRISTOPHER, MNYAMATA WA KU GHANA.

“Ukakhala pa mavuto, Mulungu amaona zonse ndipo amakuthandiza mwachikondi kuposa mmene umaganizira.”—HANNAH, MTSIKANA WAZAKA 13 WA KU ALASKA, U.S.A.

“Mulungu akakhala kuti ndi mnzako wapamtima, umamva bwino kwambiri komanso umasangalala.”—GINA, MAYI WAZAKA ZA M’MA 40 WA KU JAMAICA.

Si anthu atatu okhawa amene ali ndi maganizo amenewa. Pali anthu enanso ambiri amene amaona kuti Mulungu ndi mnzawo wapamtima. Kodi inunso mumaona choncho? Kapena mukufuna Mulungu atakhala mnzanu? Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi n’zothekadi munthu kukhala mnzake wapamtima wa Mulungu, yemwe ndi Wamphamvuyonse? Nanga munthu angatani kuti zimenezi zitheke?’

MULUNGU ANGATHE KUKHALA MNZANU WAPAMTIMA

Baibulo limanena kuti n’zotheka Mulungu kukhala mnzathu wapamtima. Mwachitsanzo, limati Mulungu anatchula Abulahamu kuti, “bwenzi langa.” (Yesaya 41:8) Komansotu lemba la Yakobo 4:8 limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” Zimenezi zikusonyeza kuti n’zotheka ndithu Mulungu kukhala mnzathu wapamtima. Koma popeza Mulungu ndi wosaoneka, kodi ‘tingamuyandikire’ bwanji n’kukhala mnzathu wapamtima?

Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambirane zomwe zimachitika kuti anthu akhale mabwenzi apamtima. Choyamba anthuwo amauzana mayina. Ndiyeno akamalankhulana komanso kuuzana zakukhosi, amayamba kugwirizana kwambiri. Zikatere amayamba kupatsana mphatso kapena kuchitirana zinthu zosiyanasiyana. Izi zimapangitsa kuti azikondana kwambiri. Umu ndi mmenenso ubwenzi ndi Mulungu umayambira. Tiyeni tione mmene zimenezi zimachitikira.