Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KUCHEZA NDI MUNTHU WINA

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukumbukira Imfa ya Yesu?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukumbukira Imfa ya Yesu?

Nkhani ili m’munsiyi ikusonyeza zimene a Mboni za Yehova amachita akamakambirana ndi anthu nkhani za m’Baibulo. Tiyerekeze kuti Mayi Mogan a Mboni za Yehova, afika pakhomo pa Mayi Black.

“MUZICHITA ZIMENEZI PONDIKUMBUKIRA”

Mayi Mogan: Ndasangalala kuti ndakupezani muli pakhomo Mayi Black. Zikomo kwambiri chifukwa chobwera kumwambo wokumbukira imfa ya Yesu mlungu watha. * Ndikukhulupirira kuti munasangalala ndi nkhani yomwe inakambidwa ija.

Mayi Black: Ndinasangalala nayodi kwambiri. Koma kunena zoona, zina sindinazimvetse bwinobwino. Anthu ambiri amakumbukira kubadwa kwa Yesu pa Khirisimasi komanso amachita Isitala pokumbukira kuuka kwake. Koma anthu sakumbukira imfa ya Yesu ngati mmene zimakhalira ndi kubadwa kwake.

Mayi Mogan: N’zoonadi. Khirisimasi ndi Isitala ndi zikondwerero zotchuka padziko lonse. Koma a Mboni za Yehova amaona kuti n’zofunika kwambiri kukumbukira imfa ya Yesu. Ngati muli ndi nthawi pang’ono, ndingakufotokozereni chifukwa chake.

Mayi Black: Palibe vuto. Mpata ndili nawo ndithu.

Mayi Mogan: Chifukwa chachikulu n’choti, Yesu analamula otsatira ake kuti azikumbukira imfa yake. Taganizirani zomwe zinachitika usiku woti aphedwa mawa lake. Kodi mukukumbukira kuti wokamba nkhani uja ananena kuti Yesu ndi ophunzira ake anadya chakudya chamadzulo?

Mayi Black: Eya, ndikukumbukiradi mfundo imeneyo.

Mayi Mogan: Chakudyachi chimadziwikanso kuti Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Pa nthawi ya chakudya chimenechi, Yesu anauza otsatira ake malangizo enaake. Kodi mungawerenge lemba la Luka 22:19, kuti timve zimene Yesu ananena?

Mayi Black: Chabwino, likuti. “Kenako anatenga mkate. Atayamika anaunyemanyema n’kuwapatsa, ndipo anati: ‘Mkate uwu ukuimira thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi pondikumbukira.’”

Mayi Mogan: Zikomo kwambiri. Taonani zimene Yesu ananena kumapeto kwa vesili. Anati: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.” Apa Yesu ankatanthauza kuti otsatira ake azikumbukira imfa yake, chifukwa anali atawauza kale kuti adzapereka moyo wake pofuna kuwawombola. Yesu anatchulanso mfundo yomweyi pa Mateyu 20:28. Lembali limati: “Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” Mwachidule ndingati a Mboni za Yehova chaka chilichonse amasonkhana pa tsiku limene Yesu anafa kuti akumbukire zimene Yesu anachita popereka moyo wake kuti atiwombole. Imfa yake idzathandiza anthu omvera kupeza moyo wosatha.

N’CHIFUKWA CHIYANI TINAFUNIKA KUWOMBOLEDWA?

Mayi Black: Ndamvapo anthu akunena kuti Yesu anatifera kuti tidzapeze moyo wosatha. Koma kunena zoona nkhani imeneyi sindiimvetsa bwino.

Mayi Mogan: Si inu nokha. Nkhani yokhudza dipo la Yesu ndi yovuta kumvetsa. Koma ndi imodzi mwa nkhani zofunika kwambiri zomwe Baibulo limaphunzitsa. Nkhani yake ndi yaitali ndipo pangafunike nthawi kuti muimvetse bwinobwino.

Mayi Black: Nthawi ilipo. Mukhoza kundifotokozera.

Mayi Mogan: Chabwino. Nkhani imeneyi ndinaiwerenganso posachedwapa, ndipo ndiyesetsa kufotokoza moti muimvetse bwino.

Mayi Black: Okhe.

Mayi Mogan: Kuti timvetse chifukwa chake anthufe tinkafunika kuwomboledwa, tifunika kudziwa mavuto amene Adamu ndi Hava anabweretsa atachimwa m’munda wa Edeni. Tiyeni tiwerenge lemba la Aroma 6:23. Kodi mungawerenge?

Mayi Black: Ndiwerenga. Likuti: “Malipiro a uchimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”

Mayi Mogan: Zikomo, mwawerenga bwino. Tiyeni tikambirane zimene vesili likunena. Layamba ndi mawu akuti: “Malipiro a uchimo ndi imfa.” Mfundo imeneyi yakhala ikugwira ntchito kuyambira pamene Adamu ndi Hava analengedwa. Munthu akachimwa, zotsatira zake ndi imfa. N’zoona kuti anthu atangolengedwa kumene, panalibe munthu wochimwa. Adamu ndi Hava analengedwa angwiro ndipo ana awonso akanakhala angwiro. Choncho sipakanakhalanso chifukwa choti anthu azifa. Adamu ndi Hava komanso ana awo akanakhala ndi moyo wosangalala mpaka kalekale. Koma zimenezi sizinachitike. Kodi mukudziwa chifukwa chake?

Mayi Black: Ndikuganiza kuti n’chifukwa choti Adamu ndi Hava anadya chipatso cha mtengo umene Mulungu anawaletsa.

Mayi Mogan: Zoona. Adamu ndi Hava anachimwa chifukwa anasankha dala kusamvera Mulungu. M’mawu ena tingati anasankha kuti akhale ochimwa kapena kuti asakhalenso angwiro. Komatu zimene anasankhazi zinabweretsera mavuto kwa iwowo komanso ana awo.

Mayi Black: Mukutanthauza chiyani?

Mayi Mogan: Mwina ndikupatseni chitsanzo. Kodi munayamba mwaphikapo chigumu?

Mayi Black: Ee. Ndimakonda kuphika zigumu kwabasi.

Mayi Mogan: Tiyerekeze kuti mwapeza poto wabwino woti muziphikiramo zigumu. Koma musanayambe kumugwiritsa ntchito, potoyo akugwa n’kupindika mbali imodzi. Ndiye mutati mwaphika chigumu m’mpoto ameneyu, chingakhale chotani?

Mayi Black: Chingakhale chopindika, popeza potoyo ndi wopindikanso.

Mayi Mogan: Mofanana ndi zimenezi, Adamu ndi Hava atasankha kusamvera Mulungu, sanalinso angwiro. Choncho tingati anakhala ngati apindika. Ndiye chifukwa choti anachimwa asanabereke ana, ana onse amene anabereka anabadwa opindika, kapena kuti ochimwa. M’Baibulo, mawu akuti munthu “wochimwa” ali ndi matanthauzo awiri. Choyamba amatanthauza munthu amene wachita tchimo linalake. Chachiwiri mawuwa amanenanso za anthu tonsefe. Popeza tonse tinachokera kwa Adamu ndi Hava, omwe anali ochimwa, ndiye kuti tonsefe ndife ochimwa. Tikutero chifukwa Adamu ndi Hava atachimwa anakhala ngati agulitsa ana awo onse ku uchimo, womwe umachititsa kuti anawo azifa. Ndiye chifukwa chake lemba la Aroma 6:23 limanena kuti, malipiro a uchimo ndi imfa.

Mayi Black: Komatu chimenechi si chilungamo. N’chifukwa chiyani anthu onse amavutika komanso kufa, pomwe anthu awiri okha ndi omwe anachimwa?

Mayi Mogan: Zingaonekedi ngati kupanda chilungamo. Koma zosangalatsa n’zoti, Mulungu yemwe amaweruza mwachilungamo anagamula kuti Adamu ndi Hava afe chifukwa cha tchimo lomwe anachita. Komabe anakonza njira yopulumutsira ana awo. Mulungu anakonza zoti Mwana wake afe n’cholinga choti awombole ana a Adamu ndi Hava. Taonaninso zimene zili palemba la Aroma 6:23 lija. Mwaona kuti pambuyo pa mawu akuti, “malipiro a uchimo ndi imfa” pali mawu akuti, “koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu”? Choncho, imfa ya Yesu idzathandiza kuti anthu amasuke ku uchimo ndi imfa. *

DIPO LA YESU NDI MPHATSO YAMTENGO WAPATALI YOCHOKERA KWA MULUNGU

Mayi Mogan: Koma pali mfundo ina m’vesili yomwe ndingakonde mutaidziwa.

Mayi Black: Mfundo yake ndi yotani?

Mayi Mogan: Kodi mwaona kuti vesili likunenanso kuti: “Koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu”? Popeza Yesu anavutika komanso kufa chifukwa cha ifeyo, n’chifukwa chiyani vesili likunena kuti Mulungu ndi amene amapereka mphatso ya moyo wosatha? Bwanji silikunena kuti Yesu? *

Mayi Black: Iii kayatu. Sindikudziwa.

Mayi Mogan: Kumbukirani kuti Adamu ndi Hava anachimwira Mulungu osati Yesu. Ziyenera kuti zinamupweteka kwambiri Mulungu kuona kuti anthu oyambirirawa amuchimwira. Koma pasanapite nthawi, Mulungu ananena zimene adzachite kuti athetse nkhaniyo. * Anakonza zoti mwana wake mmodzi wauzimu adzabwere padziko lapansi n’kukhala munthu wangwiro. Ankafuna kuti mwana ameneyu adzapereke dipo moyo wake kuti awombole anthu ku uchimo. Choncho, Mulungu ndi amene anakonza zoti Yesu abwere padziko lapansi. Ndiye tinganene kuti dipo la Yesu ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu. Koma palinso chifukwa china chomwe tinganenere kuti dipo la Yesu ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Kodi mukuganiza kuti Mulungu anamva bwanji pamene Mwana wake ankaphedwa? Mwina tipange chonchi, kodi muli ndi ana? Ndikuona zoseweretsa pakhomo pano.

Mayi Black: Ee ndili nawo awiri. Mnyamata ndi mtsikana.

Mayi Mogan: Ndiye poti ndinu kholo mukhoza kumvetsa mmene Yehova Mulungu anamvera pamene Yesu ankaphedwa. Kodi mukuganiza kuti ankamva bwanji pamene ankaona Mwana wake wokondedwa akumangidwa, kunyozedwa komanso kumenyedwa? Komanso taganiziraninso mmene anamvera pamene Mwana wake ankafa imfa yowawa atakhomeredwa pamtengo.

Mayi Black: Sindinaganizirepo zimenezi. Ziyenera kuti zinam’pwetekadi kwambiri.

Mayi Mogan: N’zoona kuti sitingathe kumvetsa bwinobwino mmene Mulungu anamvera pa nthawiyo. Koma chimene timadziwa n’choti, zinthu zoipa zikamachitika iye sasangalala. Timadziwanso chifukwa chake analola kuti Mwana wake afe. Zimenezi zafotokozedwa bwino palemba ili, lomwe ndi lodziwika kwa anthu ambiri, la Yohane 3:16. Kodi mungaliwerenge?

Mayi Black: Chabwino. Likuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”

Dipo la Yesu ndi njira yaikulu imene Mulungu anasonyezera kuti amatikonda

Mayi Mogan: Zikomo kwambiri. Taonani kumayambiriro kwa vesili. Akuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko.” Kusonyeza kuti chikondi n’chimene chinapangitsa kuti Mulungu alole Mwana wake kudzatifera. Choncho, dipo la Yesu ndi njira yaikulu imene Mulungu anasonyezera kuti amatikonda. N’chifukwa chake a Mboni za Yehova amakumbukira imfa ya Yesu chaka chilichonse posonyeza kuyamikira. Ndikukhulupirira kuti zimene takambiranazi zakuthandizani.

Mayi Black: Zandithandizadi. Zikomo kwambiri chifukwa chondifotokozeranso nkhaniyi bwinobwino.

Kodi pali nkhani inayake ya m’Baibulo imene simuimvetsa? Kapena mumafuna mutadziwa zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira? Ngati ndi choncho, funsani a Mboni za Yehova ndipo adzakambirana nanu.

^ ndime 5 Chaka chilichonse a Mboni za Yehova amachita mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Chaka chino mwambowu uchitika Lachisanu pa 3 April.

^ ndime 32 Nkhani ina m’tsogolomu idzafotokoza mmene imfa ya Yesu idzathandizire kuti anthu amasuke ku uchimo ndi imfa komanso zimene tiyenera kuchita kuti tidzapeze madalitso omwe imfa ya Yesuyi idzabweretse.

^ ndime 36 Baibulo limanena kuti Mulungu ndi wamkulu kuposa Yesu komanso kuti Yesu si Mulungu. Kuti mudziwe zambiri werengani mutu 4 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Bukuli