Boti la Lightbearer Linabweretsa Kuwala kwa Choonadi Kum’mwera Chakum’mawa kwa Asia
Chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1930, a Mboni za Yehova anali asanalalikirepo kumayiko monga, Indonesia, Malaysia, ndiponso kumene panopa kumatchedwa kuti Papua New Guinea. Kodi uthenga wabwino ukanafika bwanji m’mayiko amenewa? Pofuna kuthetsa vutoli, nthambi ya Australia (yomwe panopa imatchedwa Australasia) inagula boti lalitali mamita 16. Botili linali ndi mitengo iwiri italiitali yomangirirapo nsalu zoyendetsera botilo. Analipatsa dzina lakuti Lightbearer, limene limatanthauza kuti wobweretsa kuwala, chifukwa chakuti anthu onse amene ankayenda pabotilo anali apainiya a ndipo cholinga chawo chinali chakuti afikitse kuwala kwa choonadi kumadera akutali.—Mateyu 5:14-16.
Kulalikira ku New Guinea
Mu February 1935, anthu 7 amene ankayenda pabotilo ananyamuka ku Sydney, ku gombe lakum’mawa la Australia, n’kulowera kumpoto paulendo wapanyanja wopita ku Port Moresby, m’dziko la New Guinea. Paulendowu ankagwira nsomba ndipo anaima pa madoko angapo kuti agule mafuta, chakudya, komanso kuti akonzetse zina ndi zina pa botilo. Pa 10 April 1935, ananyamuka ku Cooktown, m’chigawo cha Queensland ku Australia. Anagwiritsa ntchito injini ya botilo pamene ankadutsa pa malo ena oopsa panyanja otchedwa Great Barrier Reef. Koma injiniyo inayamba kupanga phokoso linalake lachilendo ndipo anaizimitsa. Tsopano anayenera kusankha kuti kodi abwerere kapena azipitirirabe mpaka ku New Guinea? Eric Ewins, yemwe anali kaputeni wa botilo anati: “Tinaona kuti sizingakhale bwino kubwerera.” Choncho botilo linapitirizabe ulendo wake ndipo linafika bwinobwino ku Port Moresby pa 28 April, 1935.
Pamene makaniko ankakonza injini ya botilo, anthu onse amene ankayenda pa botilo, kupatulapo Frank Dewar, ankalalikira uthenga wabwino ku Port Moresby. Frank, amene mmodzi wa abalewo anamufotokoza kuti anali “mpainiya wakhama kwabasi,” anati, ‘Ndinatenga mpukutu wa mabuku ndipo ndinayamba kuyenda kumalowera nawo kumtunda. Ndinayenda mwina makilomita 32 ndipo ndinkalalikira kwa anthu okhala kumeneko.’ Pobwerera, anadzera njira ina yowolokera pakamtsinje kenakake kodzaza ndi ng’ona. Koma iye anayesetsa kuwoloka mosamala mpaka anafika bwinobwino. Khama la amuna amenewa polalikira linawapindulira. Anthu ena amene analandira mabuku panthawi imeneyo anadzakhala a Mboni za Yehova.
Kulalikira ku Java
Injini ija itakonzedwa, boti lija linachoka ku Port Moresby ndipo linayamba ulendo wopita kuchilumba cha Java m’dziko la Dutch East Indies (mbali yaikulu ya dziko limeneli tsopano ili ku Indonesia). Botilo linaima maulendo angapo kuti anthuwo agule zinthu zofunikira, kenako pa 15 July 1935, linafika ku Batavia (kumene tsopano ndi ku Jakarta).
Atafika kumeneko, Charles Harris, yemwe ankayenda nawo m’botilo, anatsika n’kukhazikika ku Java, kumene anapitiriza kulalikira uthenga wabwino mwakhama. b Iye anati: “M’masiku amenewo, nthawi zambiri tinkangopereka kwa anthu mabuku othandiza pophunzira Baibulo kenako n’kupita ku tawuni yotsatira. Ndinkanyamula mabuku a m’Chiarabu, Chitchainizi, Chidatchi, Chingelezi, ndi Chiindoneziya. Anthu ambiri ankalandira mabuku athu, moti ndinkagawira mabuku okwana mpaka 17,000 pachaka.”
Chifukwa cha khama la Charles, ngakhale akuluakulu a boma Achidatchi anadziwa zimene iye ankachita. Panthawi ina, mkulu wa boma anafunsa munthu wina wa Mboni amene ankalalikira ku Java kuti panali Mboni zingati zimene zinkalalikira kum’mawa kwa Java, kumene kunali Charles. “Kuli m’modzi yekha,” anayankha choncho m’baleyo. Mkulu wabomayo sanakhulupirire ndipo anati, “Aa, ukuganiza kuti ine ndingakhulupirire zimenezo? Muyenera kuti muli ndi gulu la anthu amene akulalikira kumeneko, chifukwa kukugawidwa mabuku ochuluka kwabasi.”
Kulalikira ku Singapore ndi ku Malaysia
Botilo litachoka ku Indonesia linapita ku Singapore, komwe linafikako pa 7 August. Paliponse pamene ankaima, abalewo ankawulutsa nkhani zojambulidwa kuti anthu amvere ndipo zinkamveka bwino pa zokuzira mawu zamphamvu za botilo. Njira yolalikira imeneyi nthawi zambiri inkakopa anthu ambiri. Mwachitsanzo, nyuzipepala ina yotchedwa Singapore Free Press inati: “Pamadzi panamveka mawu amphamvu kwambiri Lachitatu usiku,” ndipo inapitiriza kuti: “Inali nkhani yapadera kwambiri, . . . ndipo imachokera . . . m’boti lotchedwa ‘Lightbearer,’ lomwe lakhala likufalitsa mapulogalamu a Watch Tower ku Singapore kuno kuyambira pamene linafika kuchokera ku Australia.” Nkhaniyo inapitiriza kuti, “nyengo ikakhala bwino, mapulogalamuwa akumamveka kutali, mpaka kukafika pamtunda wa . . . makilomita atatu kapena anayi kuchokera pamadzipo.”
Panthawi imene botili linali ku Singapore, Frank Dewar anasiyana nalo kuti akayambe utumiki watsopano. Pokumbukira mmene anachokera, Frank anati: “Tinayamba kuchita upainiya ku Singapore uku tikupitiriza kukhala m’botilo. Nthawi yoti botilo lipitirize ulendo wake itakwana, Eric Ewins anandiuza mawu amene sindinkayembekezera. Anati: ‘Frank, paja unati unasankha dziko la Siam (limene panopa ndi Thailand) kuti likhale gawo lako. Basi tikusiya panopa. Tiye, zipita!’ Ndinangoti kukamwa yasa, kusowa chonena. Kenako ndinati: ‘Komatu sindikudziwa n’komwe kuti ku Siam n’kuti kuchokera panopa.’” Eric anamuuza kuti akhoza kukafikako pa sitima kuchokera ku Kuala Lumpur, m’dziko limene panopa ndi la Malaysia. Frank anamvera ndipo ananyamuka ulendo wopita ku Kuala Lumpur, n’kukafika ku Thailand patatha miyezi ingapo. c
Pamene botilo linkayenda mphepete mwa gombe chakumadzulo kwa dziko la Malaysia, linaima ku Johore Bahru, Muar, Malacca, Klang, Port Swettenham (komwe pano ndi ku Port Klang), ndi ku Penang. Padoko lililonse lomwe ankaima, abalewo ankawulutsa nkhani za m’Baibulo zojambulidwa pa zokuzira mawu za botilo. Jean Deschamp, wa Mboni amene panthawiyo ankatumikira ku Indonesia anati: “Anthu ankachita chidwi kwambiri ndi botilo, ngati kuti lachokera kumwamba.” Akamaliza kuwulutsa nkhani zojambulidwazo, abalewo ankapita kumtunda kukagawira mabuku kwa anthu achidwi.
Kulalikira ku Sumatra
Botilo litachoka ku Penang, abalewo anapitiriza ulendo wawo kudutsa pa Nyanja ya Malacca kukafika ku Medan, m’dziko la Sumatra (lomwe pano ndi mbali ya Indonesia). Eric Ewins akukumbukira kuti: “Zinthu zinatiyendera bwino kwabasi panthawi imene tinali m’chigawo cha Medan, ndipo anthu ambiri anasangalala kumva uthenga wabwino.” Abalewo anagawira mabuku pafupifupi 3000 m’dera limenelo.
Pamene botilo linkapitiriza ulendo wake chakum’mwera, abalewo ankalalikira pa madoko akuluakulu kum’mawa kwa Sumatra. Mu November 1936, botilo linabwerera ku Singapore, kumene Eric Ewins anasiyana nalo. Patapita milungu ingapo, iye anakwatira Irene Struys, wa Mboni wina amene ankakhala ku Singapore. Eric ndi Irene anapitiriza limodzi utumiki wawo waupainiya ku Sumatra. Koma zimenezi zinatanthauza kuti tsopano pankafunika kaputeni wina kuti aziyendetsa boti lija.
Kulalikira ku Borneo
Amene anakhala kaputeni watsopano anali munthu wina wodziwa bwino kuyendetsa masitima apamadzi dzina lake Norman Senior. Iye anafika mu January 1937 kuchokera ku Sydney. Kenako abalewo ananyamuka ku Singapore kupita ku Borneo ndi ku Celebes (kumene tsopano ndi ku Sulawesi) ndipo analalikira kwambiri m’dera limeneli, mpaka kukafika makilomita 480 kumtunda.
Botilo litafika padoko la Samarinda ku Borneo, mkulu woyang’anira dokolo anakana kulola abalewo kulalikira kwa anthu akuderalo. Koma Norman atamufotokozera mkuluyo za ntchito yathu, anasiya kuvuta mpaka anatengako mabuku angapo.
Panthawi ina, m’busa wa tchalitchi chinachake kuderalo anaitana Norman kuti akalalikire kutchalitchi kwake. Koma m’malo mokamba nkhani yekha, Norman anawulutsa matepi asanu a nkhani za m’Baibulo zojambulidwa pa chipangizo cha fonogilafu ndipo m’busayo anasangalala nazo kwambiri, moti anatengako mabuku ena kuti akapatseko anzake. Koma azibusa ambiri ankachita zosiyana ndi m’busa ameneyu. Nthawi zambiri atsogoleri a zipembedzo sankasangalala ndi ntchito ya Mboni za Yehova. Iwo anakwiya kwambiri poona mmene abale oyenda pa botiwo ankalalikirira mopanda mantha, ndipo anauza akuluakulu a boma kuti aletse boti la Lightbearer kuima pa madoko ena.
Kubwerera ku Australia
Mu December 1937, botilo linabwerera ku Australia chifukwa chakuti atsogoleri a zipembedzo analimbikitsa maboma kuti asalilolenso kuima pamadoko awo. Abale omwe ankayenda pabotilo anaima pa Sydney Harbor ndipo anangofika panthawi yake chifukwa anachita nawo msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova mu April 1938. Apa n’kuti patatha zaka zoposa zitatu kuchokera pamene botilo linanyamuka ku Sydney. Botilo analigulitsa kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1940, ntchito ya Mboni itangoletsedwa kumene ku Australia. M’bale Ewins anati: “Tinaona kuti botilo linali litakwaniritsa ntchito yake.” M’baleyu anati zaka zimene anakhala akuchita utumiki wake m’boti la Lightbearer ‘zinali zina mwa zaka zosangalatsa kwambiri pamoyo wake.’
Mmene Anthu Akupindulirabe ndi Ntchito Imene Boti la Lightbearer Inagwira
Abale amene ankayenda paboti la Lightbearer anabzala mbewu za Ufumu m’dera lalikulu kwambiri lokhala ndi anthu ambiri. Ndipo ngakhale kuti ankatsutsidwa, pang’ono ndi pang’ono ntchito yawo inabala zipatso. (Luka 8:11, 15) Ndipotu m’madera amene apainiya oyambirira amenewo analalikira, tsopano muli ofalitsa Ufumu oposa 40,000. Zoonadi, ntchito yotamandika imene amuna olimba mtima ochepa amenewa anagwira inathandiza anthu ambiri. Ndithu, boti lawo linagwiradi ntchito yobweretsa kuwala kwa choonadi kumadera akutali!