KHALANI MASO
N’chifukwa Chiyani Anthu Sangathe Kubweretsa Mtendere?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Mabungwe komanso atsogoleri a mayiko alephera kubweretsa mtendere. Panopa anthu akukangana komanso kumenyana kwambiri padzikoli kuposa nthawi iliyonse kuchokera pamene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inatha. Anthu pafupifupi 2 biliyoni, omwe akuimira munthu mmodzi pa anthu 4 alionse padzikoli, amakhala m’madera amene mukuchitika mikangano imeneyi.
N’chifukwa chiyani anthu sangabweretse mtendere? Kodi Baibulo limanena zotani?
N’chifukwa chiyani anthu sangabweretse mtendere?
1. Anthu ali ndi makhalidwe amene amawalepheretsa kubweretsa mtendere. Baibulo linaneneratu kuti m’nthawi yathu ino, “anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, odzikweza, . . . osakhulupirika, . . . osafuna kugwirizana ndi ena, . . . osadziletsa, oopsa, . . . osamva za ena, odzitukumula chifukwa cha kunyada.”—2 Timoteyo 3:2-4.
2. Munthu aliyense payekha kapena anthu onse pamodzi sangathe kuthetsa mavuto awo popanda kuthandizidwa ndi Mlengi wawo, Yehova a Mulungu. Baibulo limanena kuti “munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.
3. Anthu ambiri m’dzikoli akulamuliridwa ndi wolamulira wamphamvu komanso woipa, Satana Mdyerekezi, yemwe “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 12:9) Pa nthawi yonse imene dzikoli lipitirize kukhala “m’manja mwa woipayo,” nkhondo komanso mikangano zipitiriza kuchitika.—1 Yohane 5:19.
Kodi ndi ndani angabweretse mtendere?
Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu ndi amene adzabweretse mtendere, osati anthu.
“‘Ndikudziwa bwino zimene ndikuganiza zokhudza inu. Ndikuganiza zokupatsani mtendere osati masoka ndiponso zokupatsani tsogolo labwino ndi chiyembekezo chabwino,’ akutero Yehova.”—Yeremiya 29:11.
Kodi Mulungu adzakwaniritsa bwanji lonjezo limeneli? ‘Mulungu amene amapereka mtendere adzaphwanya Satana.’ (Aroma 16:20) Kuti akhazikitse mtendere padziko lonse, Mulungu adzagwiritsa ntchito boma lakumwamba, lomwe Baibulo limalitchula kuti “Ufumu wa Mulungu.” (Luka 4:43) Yesu Khristu yemwe ndi Mfumu ya Ufumu umenewu akamadzalamulira, anthu adzaphunzira kukhala mwamtendere.—Yesaya 9:6, 7.
Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti, “Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Chiyani?”
a Yehova ndi dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.