Kuona Malo ku Beteli
Tikukuitanani kuti mudzaone maofesi athu a nthambi omwenso amadziwika kuti Beteli. Ku maofesi athu ena kulinso malo achionetsero omwe mukhoza kuona nokha popanda wokutsogolerani.
Kuyambiranso Kuona Malo: M'mayiko ambiri, anthu adzayambiranso kuona malo m'maofesi athu a nthambi kuyambira pa 1 June, 2023. Kuti mudziwe zambiri, lankhulani ndi abale a ku nthambi yomwe mukufuna kukaonayo. Komabe, musapite kukaona malo ngati mwapezeka ndi COVID-19 kapena ngati muli ndi zizindikiro za chimfine kapenanso ngati posachedwapa munakumana ndi munthu amene wapezeka ndi COVID-19.
Brazil
Rodovia SP-141 - km 43
CESÁRIO LANGE-SP
18285-901
BRAZIL
+55 15-3322-9000
Kuona Malo
Lolemba mpaka Lachisanu
8:00 a.m. mpaka 11:00 a.m. ndi 1:00 p.m. mpaka 3:00 p.m.
Nthawi yonse: Maola 1.4
Zimene Timachita
Timasindikiza ma Baibulo 36 miliyoni ndiponso mabuku ndi timabuku. Timatumiza mabuku olemera matani pafupifupi 7,000 chaka chilichonse m’zinenero zoposa 90.