Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kutonthoza Komanso Kuthandiza Anthu Omwe Akudwala

Kutonthoza Komanso Kuthandiza Anthu Omwe Akudwala

Anthu amene akudwala kwambiri akhoza kuyamba kuda nkhawa mosavuta, ndipo ngati angafunikire thandizo la kuchipatala, kawirikawiri amayamba kuvutika maganizo kwambiri. Malinga ndi zimene magazini ina yothandiza azachipatala inanena, “kafukufuku akusonyeza kuti kuthandiza odwala mwamaganizo komanso mwauzimu n’kothandiza kwambiri kuti odwalawo akhale ndi thanzi labwino.” *

Chifukwa cha zimenezi, a Mboni za Yehova amatonthoza a Mboni anzawo omwe agonekedwa m’chipatala pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo komanso amawathandiza m’njira zosiyanasiyana. Akulu a m’mipingo ya Mboni za Yehova amayendera anthu a mumpingo mwawo omwe akudwala. Koma kodi chimachitika n’chiyani ngati wa Mboni yemwe akudwala akulandira thandizo ku chipatala cha kutali kwambiri ndi kwawo? A Mboni za Yehova anakhazikitsa Magulu Oyendera Odwala m’mizinda ikuluikulu padziko lonse. Akulu a m’mipingo ya Mboni za Yehova omwe ali m’maguluwa, nthawi ndi nthawi amapita m’zipatala kuti akathandize a Mboni omwe akudwala limodzi ndi mabanja awo omwe achokera kumadera ena a m’dzikolo kapenanso ku mayiko ena kuti adzalandire chithandizo cha mankhwala. Padziko lonse pali Magulu Oyendera Odwala okwana 1,900 ndipo muli anthu ongodzipereka opitirira 28,000. *

Kodi Magulu Oyendera Odwala amatonthoza bwanji odwala ndi mfundo za m’Baibulo?

A William omwe ali m’gulu lina la oyendera odwala anati: “Ndakhala ndikutonthoza a Mboni komanso anthu a m’banja mwawo omwe si a Mboni pongoyankhula nawo ndiponso kuwamvetsera. Ndimawatsimikizira kuti Yehova Mulungu akudziwa zimene akukumana nazo komanso zimamukhudza. Odwala ndi anthu a m’banja mwawo amayamikira tikawapempherera.”

Anthu ambiri anafotokoza zinthu zosonyeza kuyamikira chifukwa cholimbikitsidwa ndi Magulu Oyendera Odwala. M’munsimu muli zitsanzo zochepa za ku United States, kumene kuli anthu pafupifupi 7,000 omwe amayendera odwala.

  • Priscilla anati: “Zikomo chifukwa chodzaona bambo anga m’chipatala atadwala sitiroko. Iwo anasangalala kwambiri chifukwa munkadzawaona. Iwo anachita chidwi atazindikira kuti pali dongosolo loyendera odwala m’zipatala. Ndikuganiza kuti kubwera kwanu kunawathandiza kuti achire mwamsanga.”

  • Ophilia yemwe mayi ake anamwalira, anauza mmodzi mwa anthu oyendera odwala kuti: “Kubwera kwanu kunawathandiza kwambiri mayi anga. Iwo ankadziwa kuti Yehova ndi amene anakutumizani. Zikomo chifukwa cha chikondi chanu.”

  • Wodwala wina anasokonezeka kwambiri maganizo komanso kuda nkhawa atauzidwa kuti wangotsala ndi masiku ochepa oti akhale ndi moyo. A James omwe ndi mmodzi mwa anthu oyendera odwala, anapita kukamuona ndipo anamutonthoza pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo zopezeka pa Afilipi 4:6, 7. Iwo anati: “Nditapita kukamuona tsiku lotsatira, anali atasintha kwambiri maganizo ake. Ngakhale kuti anauzidwa zoti watsala ndi masiku ochepa oti akhale ndi moyo, anayamba kukhulupirira kuti Yehova amuthandiza komanso anandilimbikitsa ineyo.”

Kodi Magulu Oyendera Odwala amathandiza bwanji anthu?

Pauline yemwe mwamuna wake anamwalira kuchipatala chakutali ndi kwawo, analemba kuti: “Zikomo kwambiri chifukwa munatithandiza pa nthawi yomwe banja lathu linakumana ndi mavuto aakulu kwambiri pa moyo wathu. Zinatilimbikitsa kwambiri titangodziwa kuti mubwera kudzationa pakati pausiku ngakhale kuti munkafunikanso kupita kuntchito tsiku lotsatira. Zikomo potithandiza kupeza malo ogona a anthu tonse 11 komanso kumatiimbira pa nthawi yonse yomwe tinali m’chipatala. Ndikuthokoza Yehova ndi gulu lake potithandiza mwa njira imeneyi.”

Nicki, Robin komanso Gayle anachita ngozi yagalimoto. Ngoziyi inachitikira pamtunda wa makilomita 300 kuchokera kwawo. A Carlos omwe ndi mmodzi mwa anthu oyendera odwala atadziwitsidwa za ngoziyi, anapita ku chipatala komwe anthuwa anapititsidwa. A Carlos anati: “Ndinadzipereka kuti ndiwathandiza pa chilichonse chomwe ankafunikira ndipo pamene Nicki ankakalandira chithandizo ndinatenga galu wake n’kumamuyang’anira.” Kenako a Curtis omwenso ndi mmodzi mwa anthu oyendera odwala anafika kuchipatalako limodzi ndi mkazi wawo. Iwo anakhalabe kuchipatalako kwa maola ambiri mpaka pamene achibale a anthu omwe anachita ngoziwo anafika. Bambo wina yemwe ndi mnzawo wa omwe anachita ngoziwo anati: “Onse atatu anatonthozedwa chifukwa cha mmene anathandizidwira. Robin yemwe ndi mng’ono wake wa Nicki ndipo si wa Mboni za Yehova, anachita chidwi kwambiri ndi thandizo limene anthu omwe ali m’Magulu Oyendera Odwala anapereka.”

^ ndime 2 Kafukufukuyu anasindikizidwa m’magazini ya The Joint Commission Journal on Quality and Patient Safety, mu December 2003, Voliyumu 29, Na. 12, tsamba 661, pamutu wakuti “Kuthandiza Odwala Mwamaganizo Komanso Mwauzimu.”

^ ndime 3 Monga mmene akulu onse a m’mipingo ya Mboni za Yehova amachitira, akulu omwe ali m’Magulu Oyendera Odwala amatumikiranso m’mipingo yawo monga abusa auzimu, aphunzitsi, komanso alaliki. Iwo salandira malipiro alionse akamagwira ntchito zimenezi, koma amatumikira modzipereka ndiponso mofunitsitsa.​—1 Petulo 5:2.