JUNE 25, 2019
GERMANY
Zokhudza Msonkhano wa Mayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Berlin, Germany
Masiku: 14 mpaka 16 June, 2019
Malo: Olympic Stadium ku Berlin, Germany
Zinenero: Chingelezi, Chijeremani, Chirasha
Chiwerengero cha Osonkhana: 37,115
Chiwerengero cha Obatizidwa: 255
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 5,000
Nthambi Zoitanidwa: Brazil, Britain, Canada, Ecuador, Finland, Greece, Poland, Scandinavia, Slovenia, United States
Zina Zomwe Zinachitika: Msonkhano usanachitike komanso utatha, alendo anakaona malo otchuka osungirako zinthu zakale a ku Berlin otchedwa Pergamon Museum. Mlonda wina ataona abale athu akuona malo osungirako zinthu zakalewo anati: “Anthu ambiri alibe chiyembekezo chifukwa chakuti alibe chikhulupiriro chilichonse. Koma n’zoonekeratu kuti inuyo muli ndi chikhulupiriro komanso mumakondana.” Mlonda winanso anati: “Tikakhala ndi alendo ngati inu nthawi imatha mwamsanga, ndipo ndimasangalala kugwira ntchito nthawi yowonjezera.”
Abale ndi alongo a ku Berlin akulandira alendo pabwalo la ndege
Abale ndi alongo akucheza panja pa malo omwe kunachitikira msonkhano
Alendo akujambulitsa chithunzi ndipo ena avala zovala zachikhalidwe chakwawo
M’bale Samuel Herd wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Loweruka
Alendo akumvetsera msonkhano mu Chingelezi ndipo akulemba notsi. Alongo awiri akumvetsera msonkhanowu m’chinenero china pogwiritsa ntchito mahedifoni
Abale ndi alongo akuonerera ubatizo pa tsiku Loweruka
Alendo omwe ali muutumiki wa nthawi zonse wapadera ali m’bwalo la malo a msonkhano ndipo akubayibitsa anthu pamapeto pa msonkhano Lamlungu
Sitediyamu ya Olympic ya ku Berlin yomwe poyamba inamalizidwa kumangidwa mu 1936, ndipo chithunzichi chinajambulidwa pa tsiku loyamba la msonkhano. Mu 1990, sitediyamuyi inagwiritsidwa ntchito kupangiramo msonkhano wamayiko wosaiwalika wa ku Berlin, khoma la mzinda wa Berlin litagwa
Alendo akupanga ulaliki wa m’malo opezeka anthu ambiri kutsogolo kwa malo otchuka otchedwa Brandenburg Gate mkatikati mwa mzinda wa Berlin
Alendo asonkhana pamalo otchedwa Colonnade Courtyard, pafupi ndi Pergamon Museum
Anthu omwe amaonerera zochitika zosiyanasiyana za madzulo akuwombera m’manja pamapeto a zochitikazo