JUNE 10, 2019
PARAGUAY
Madzi Asefukira ku Paraguay
Mvula yamphamvu yomwe inayamba kugwa chakumapeto kwa April 2019 ku Paraguay, yachititsa kuti madzi asefukire n’kuononga zinthu m’madera omwe ali m’mbali mwa mtsinje wa Paraguay. Anthu osachepera 6 afa ndi madzi osefukirawa.
Ofesi ya nthambi ya ku Paraguay yanena kuti abale athu 137 a m’mizinda yosiyanasiyana akhudzidwa ndi madzi osefukirawa. Mumzinda wa Asunción womwe ndi likulu la dzikoli, madzi osefukira anagwetsa khoma la Nyumba ya Ufumu yomwe inkagwiritsidwa ntchito ngati kalasi ya Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. N’zosangalatsa kuti palibe aliyense amene anavulala.
Ofesi ya nthambi yatumiza kale zinthu monga chakudya, madzi, komanso zinthu zina zofunika kwa abale ndi alongo omwe akhudzidwa ndi madzi osefukirawa. Popeza kuti madzi akupitirizabe kusefukira, abale ku ofesi ya nthambi akupitiriza kukhala tcheru ndi mmene zinthu zilili. Iwo apitirizanso kupereka zinthu zofunika komanso kulimbikitsa abale omwe ali m’madera okhudzidwa.
Tikupempherera abale ndi alongo omwe akhudzidwa ndi madzi osefukirawa ku Paraguay. Tikudziwa kuti Yehova akhala “nyumba ya mpanda wolimba” kwa abalewa pa nthawi yovutayi.—Salimo 31:2.