SEPTEMBER 17, 2019
UNITED KINGDOM
Ntchito Yomanga Ofesi ya Nthambi ku Britain Yatsala Pang’ono Kutha
Ntchito yomanga ofesi ya nthambi ya Britain pafupi ndi mzinda wa Chelmsford ku Essex, ikuyembekezeka kutha mu December 2019. Akatswiri ayamba kale kunena kuti ntchito yomangayi ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yochititsa kuti malo ayambirenso kuoneka okongola.
Pamene abale athu ankagula malowa mu 2015, n’kuti akugwiritsidwa ntchito ngati mtaya wa zinyalala za magalimoto akutha komanso zinyalala zina. Abale ndi alongo ongodzipereka anafukula zinthu zambirimbiri zomwe zinatayidwa pamalowa ndipo anazipanga kuti zithe kugwiritsidwanso ntchito. Zina mwa zinthuzo zinali matayala masauzande ambiri ndipo ena mwa matayalawo anali a pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Kenako anasefa dothi lomwe linali ndi zinthu zosafunika kuti athe kuchotsa tizinyalala ting’onoting’ono. Nthawi zinanso ankatha kugwiritsanso ntchito tizinyalalato pa zinthu zina, ndipo dothi limene alichotsa zinyalalalo ankaligwiritsanso ntchito pamalopo. Kwa maola oposa 4 miliyoni, abale ndi alongo ongodzipereka oposa 11,000 anagwira ntchito yoyeretsa malowa omwe kukula kwake ndi mahekitala 34.
Malowa akadzatha kumangidwa adzakhala ndi minda yokhala ndi zomera za m’derali komanso zochokera m’madera ena, madamu, maluwa akutchire, ndiponso munda wazipatso. Si kuti malowa anakonzedwa kuti azingooneka okongola basi. Koma malowa alinso ndi zinyama ndi zolengedwa zina zakutchire, akuthandiza kuti madzi asamawonongeke, akuteteza mitengo ikuluikulu ndi zomera zina, akuchulukitsa chiwerengero cha zomera zochokera m’derali, komanso akuchititsa kuti anthu a m’derali azikhala kumalo okongola.
M’bale Paul Rogers, yemwe ali m’Komiti Yoyang’anira Ntchito Yomanga, anati: “Malo omwe tinagula sankasamalidwa komanso ankagwiritsidwa ntchito molakwika kwa zaka zambiri. Malowa anayamba kusintha pamene gulu la abale ndi alongo ongodzipereka linagwira ntchito yoika zinyalala m’magulu osiyanasiyana. Ntchito yoyeretsa malowa itatha, dothi la pamalowa linagwiritsidwa ntchito kupangira mapiri komanso makhwawa ofanana ndi omwe ali pafupi ndi malowa, ndipo anadzalanso mitengo yatsopano, zitsamba ndiponso zomera zina. Mmene malowa anakongolera ntchitoyi itatha akutikumbutsa mawu a palemba la Ezekieli 36:35, 36, akuti: ‘Anthu adzanena kuti: “Dziko ilo limene linali bwinja tsopano lakhala ngati munda wa Edeni” . . . Anthu a mitundu ina . . . adzadziwa kuti ine Yehova, ndamanga zinthu zimene zinagwetsedwa. Adzadziwa kuti ndabzala mitengo m’dziko limene linali bwinja.’”
Alongo awiri akuchotsa zinyalala m’damu. Mathilakitala ndi amene anagwiritsidwa ntchito pochotsa zinyalala zikuluzikulu komanso matope, pomwe zinyalala zing’onozing’ono ndi zomera zosafunika zinachotsedwa ndi manja. Zomera zam’madzi zoposa 8,000 zinabzalidwa, ndipo zikuthandiza kuti madzi azikhala oyera
Limodzi mwa madamu momwe mumapita madzi ochokera m’misewu yapafupi komanso ku ofesi ya nthambi. Kumanzere kwa chithunzichi kuli siteji ya basi pomwe pali malo omwe anthu a m’derali angaimepo kuti athe kuona malo okongolawa
Anthu atatu okonza kaonekedwe ka malowa akubzala mtengo. Pafupifupi mitengo 15,000, zitsamba, komanso zomera zina zabzalidwa kale
Mitengo 6 ya maolivi, yomwe yakhala pafupifupi zaka 100, yabzalidwa kutsogolo kwa maofesi
Alongo akujambulitsa pamene akugwira ntchito yokonza kaonekedwe ka malowa. Pafupifupi maluwa 18,000 abzalidwa pamalowa m’dera lomwe lili ndi mitengo. Zomera zosachepera 80 peresenti zomwe zinasankhidwa kuti zibzalidwe pamalowa ndi zomwe zimamera m’derali
Maluwa, zitsamba, komanso mitengo zikuoneka mokongola kunja kwa Nyumba Yogona F