ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
Kodi Ndiwonjezere Anzanga?
“Ndimamva bwino ndikakhala ndi kagulu ka anzanga amene ndimacheza nawo nthawi zonse, ndipo ndi zovuta kwambiri kuti ndisiye kucheza nawo.”—Alan.
“Ndili ndi kagulu kochepa ka anzanga, ndipo zimenezi zimandisangalatsa. Sindikonda kucheza ndi anthu amene sindikuwadziwa.”—Sara.
Kodi nanunso mumamva ngati mmene Alan ndi Sara amamvera? Kodi muli ndi kagulu ka anzanu omwe mumagwirizana nawo kwambiri moti simufuna kupeza anzanu atsopano?
Ngati ndi choncho, nkhaniyi ikuthandizani.
Vuto lomangocheza ndi kagulu kenakake ka anthu
Sikulakwa kukhala ndi kagulu kenakake ka anzanu omwe mumagwirizana nawo kwambiri. Kukhala ndi anzanu omwe mumagwirizana nawo kwambiri kumakuthandizani kumva kuti muli m’gulu linalake komanso malo amene anthu amakuonani kuti ndinu wofunika ngakhale kuti pali zina zomwe mumalakwitsa.
“Zimasangalatsa anthu ena akamakukonda komanso ukakhala m’gulu linalake. Ukhala wamng’ono umangofuna kukhala ndi anzako ocheza nawo.”—Karen, wazaka 19.
Kodi Mukudziwa? Atumwi 12 a Yesu anali ena mwa anthu omwe anali anzake a Yesu, koma panali atumwi atatu omwe anali anzake kwambiri. Atumwiwo anali Petulo, Yakobo komanso Yohane.—Maliko 9:2; Luka 8:51.
Komabe, kumangocheza ndi kagulu kenakake ka anthu osafuna kuchezanso ndi anthu ena, kungayambitse mavuto. Mwachitsanzo:
Kungapangitse kuti mutsekereze mwayi wopeza anzanu ena abwino kwambiri.
“Kungokhala ndi anzako omwe amafanana nawe kumachititsa kuti usadziwe zinthu zatsopano komanso kuti usadziwane ndi anthu abwino kwambiri.”—Evan, wazaka 21.
Kungapangitse kuti muzioneka ngati munthu wonyada.
“Kungokhala ndi kagulu kenakake ka anzanu, kungachititse anthu ena kuganiza kuti simukufuna kuyankhula ndi anthu enanso.”—Sara, wazaka 17.
Kungakupangitseni kuti muzivutitsa anthu ena.
“Zingatheke kuti munthu savutitsa anthu ena, koma ngati anzake amachita zimenezi, nayenso amayamba kuona kuti zilibe vuto komanso n’zosangalatsa.”—James, wazaka 17.
Kungakulowetseni m’mavuto makamaka ngati mukufunitsitsa kuti mukhalebe m’gululo zivute zitani.
“Ngati m’gulu la anthu amene amagwirizana kwambiri muli mmodzi amene ndi woipa, kumakhala kosavuta kuti gulu lonse liyambe kuchita zinthu zoipa.”—Martina, wazaka 17.
Zimene mungachite
Ganizirani mofatsa mfundo zimene mumayendera.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndi mfundo ziti zimene ndimayesetsa kuyendera? Kodi anzanga amapangitsa kuti ndizitsatira mfundozi kapena ndizivutika kuzitsatira? Kodi ndikuyenerabe kucheza ndi anzangawa muli monse mmene zingakhalire?’
Mfundo ya m’Baibulo: “Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.”—1 Akorinto 15:33.
“Ngati m’gulu la anthu amene umacheza nawo muli anthu amene sayendera mfundo zimene iweyo umayendera, ukhoza kuyamba kuchita zinthu zimene pawekha sukanachita.”—Ellen, wazaka 14.
Ganizirani mofatsa zinthu zimene mumaona kuti n’zofunika.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimakonda kwambiri anzanga omwe ndimacheza nawo moti ndikhoza kulolera kuphwanya mfundo zomwe ndimayendera n’cholinga choti ndizicheza nawobe? Kodi ndingatani ngati mnzanga atachita chinachake choipa?’
Mfundo ya m’Baibulo: “Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula.”—Chivumbulutso 3:19.
“Ngati mnzanu wina wachita chinachake cholakwika, ndipo mukuona kuti simungapitirize kucheza naye zingakuvuteni kumuuza chifukwa mungaoneke ngati osakhulupirika.”—Melanie, wazaka 22.
Muzicheza ndi anthu enanso.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndingapindule ngati nditayamba kucheza ndi anthu ena amene sindikuwadziwa n’cholinga choti akhalenso anzanga?’
Mfundo ya m’Baibulo: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”—Afilipi 2:4.
“Ana ena amaoneka ngati osamasuka chifukwa chakuti amakhala movutika kunyumba kwawo. Koma ukawadziwa bwino, nthawi zambiri umaona kuti pali zinthu zina zimene amachita bwino.”—Brian ,wazaka 19.
Mfundo yofunika kwambiri: Palibe vuto lililonse ngati munthu atakhala ndi kagulu kenakake ka anzake omwe amagwirizana nawo kwambiri. Komabe, mungapindule ngati mutamachezanso ndi anthu ena kuti muonjezere anzanuwo. Baibulo limati: “Wothirira ena mosaumira nayenso adzathiriridwa mosaumira.”—Miyambo 11:25.