Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Mulungu Analenga Mdyerekezi?

Kodi Mulungu Analenga Mdyerekezi?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo limasonyeza kuti Mulungu sanalenge Mdyerekezi. Koma iye analenga munthu amene kenako anadzakhala Mdyerekezi. Ponena za Mulungu, Baibulo limati: “Ntchito yake ndi yangwiro, njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika, amene sachita chosalungama. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.” (Deuteronomo 32:3-5) Tikaona mawu amenewa, tingadziwe kuti nthawi inayake Satana Mdyerekezi anali m’modzi wa ana auzimu a Mulungu, kapena kuti mngelo wolungama ndiponso wangwiro.

 Palemba la Yohane 8:44, Yesu ananena kuti Mdyerekezi “sanakhazikike m’choonadi.” Mfundo imeneyi ikusonyeza kuti nthawi inayake Satana anali m’choonadi ndipo sankachita zoipa.

 Komabe, mofanana ndi angelo onse komanso anthu amene Yehova analenga, mngelo amene anadzakhala Satana anali ndi ufulu wosankha kuchita zabwino kapena zoipa. Popeza iye anasankha kutsutsana ndi Mulungu ndiponso kunyengerera Adamu ndi Hava kuti akhale kumbali yake, iye anasankha yekha kukhala Satana, dzina lomwe limatanthauza “Wotsutsa.”—Genesis 3:1-5; Chivumbulutso 12:9.