Kodi Baibulo Limanena Kuti Kumwa Mowa Ndi Tchimo?
Yankho la m’Baibulo
Baibulo limasonyeza kuti kumwa mowa si kulakwa. Limanena kuti mowa ndi mphatso yochokera kwa Mulungu imene imapangitsa kuti anthu azisangalala. (Salimo 104:14, 15; Mlaliki 3:13; 9:7) Baibulo limanenanso kuti mowa ukhoza kuthandiza munthu amene akudwala matenda a m’mimba.—1 Timoteyo 5:23.
Yesu nayenso ankamwa vinyo pamene anali padziko lapansi. (Mateyu 26:29; Luka 7:34) Komanso pa nthawi ina, Yesu anasandutsa madzi kukhala vinyo paphwando la ukwati.—Yohane 2:1-10.
Mavuto amene amabwera chifukwa cha kumwa mowa wambiri
Ngakhale kuti kumwa mowa si kulakwa, Baibulo limanena kuti kumwa mowa wambiri komanso kuledzera n’kulakwa. Choncho, Mkhristu amene wasankha kumwa mowa, ayenera kupewa kuchita zimenezi. (1 Timoteyo 3:8; Tito 2:2, 3) Baibulo limatchula mavuto amene amabwera ngati munthu amamwa mowa wambiri komanso kuledzera. Mwachitsanzo:
Kumapangitsa kuti munthu asamaganize bwino. (Miyambo 23:29-35) Munthu amene waledzera amalephera kutsatira lamulo la m’Baibulo lakuti, “mupereke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyera ndi yovomerezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwiritsa ntchito luntha la kuganiza.”—Aroma 12:1.
Kumwa mowa wambiri kumapangitsa kuti munthu azichita zinthu mopanda manyazi komanso ‘kumawononga nzeru za munthu.’—Hoseya 4:11; Aefeso 5:18.
Kumayambitsanso matenda oopsa ndipo kumachititsa kuti munthu akhale mphawi.—Miyambo 23:21, 31, 32.
Mulungu amadana kwambiri ndi anthu amene amamwa mowa wambiri komanso kuledzera.—Miyambo 23:20; Agalatiya 5:19-21.
Kodi munthu angadziwe bwanji kuti waledzera?
Munthu angadziwe kuti waledzera ngati wayamba kuchita zinthu zomwe zikhoza kubweretsa mavuto kwa iyeyo komanso anthu ena. Baibulo silimangonena kuti munthu amasonyeza kuti waledzera ngati wakomoka nawo mowawo. Limanenanso kuti munthu woledzera amachita zinthu zosokonekera, amayenda mwadzandidzandi, amalimbana ndi anthu komanso amayankhula zosamveka. (Yobu 12:25; Salimo 107:27; Miyambo 23:29, 30, 33) Pali anthu ena omwe amamwa mowa wambiri koma osaledzera. Anthu amenewanso amakumana ndi mavuto osaneneka.—Luka 21:34, 35.
Kodi ndi nthawi iti pamene munthu sayenera kumwa mowa?
Baibulo limasonyezanso kuti pali nthawi zina zomwe Akhristu ayenera kupewa kumwa mowa. Mwachitsanzo:
Ngati anthu ena angakhumudwe akawaona akumwa mowa.—Aroma 14:21.
Ngati boma limaletsa anthu kumwa mowa.—Aroma 13:1.
Ngati munthu sangakwanitse kudziletsa kuti asamwe mowa wambiri komanso kuledzera. Anthu amene ali ndi vuto limeneli ayenera kuyesetsa kusintha mwansanga.—Mateyu 5:29, 30.